Mutu 2

1Pamenepo iwe ulibe chowiringula, munthu iwe, aliyense amene uli oweruza, pakuti m’mene uweruza wina, umadzitsutsa wekha; pakuti iwe amene uweruza umachitanso zinthu zomwezo. 2Koma tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu1 chili monga mwa choonadi kwa iwo amene achita zinthu zoterezi. 3Ndipo uganiza ichi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zinthu zotere, ndipo uzichitanso [iwe mwini], kuti iweyo udzathawa chiweruzo cha Mulungu2? 4kapena upeputsa kulemera kwa ubwino wake, ndi kulekerera, ndi chipiliro, osadziwa kuti ubwino wa Mulungu3 umakutsogolera ku kulapa? 5koma molingana ndi kuuma komanso kusalapa kwa mtima wako, udziunjikira wekha mkwiyo, m’tsiku la mkwiyo ndi vumbulutso la kuweruza kolungama kwa Mulungu4, 6amene adzabwezera kwa aliyense molingana ndi ntchito zake: 7kwa iwo amene, m’chipiliro apitiriza ntchito zabwino, kufunafuna ulemelero ndi ulemu ndi kupanda chivundi, adzabwezera moyo wosatha. 8Koma kwa iwo amene ali andeu, ndipo samvera ku choonadi, koma amvera chisalungamo, [padzakhala pamenepo] mkwiyo ndi kuzaza, 9msautso ndi kuwawa mtima, pa moyo ulionse umene uchita choipa, kwa Myuda poyamba ndi Mhelene yemwe; 10koma ulemelero ndi ulemu ndi mtendere kwa aliyense amene achita zabwino, kwa Myuda poyamba ndi Mhelene yemwe: 11pakuti ndi Mulungu5 palibe tsankho la munthu. 12Pakuti monga ambiri anachimwa popanda lamulo adzaonongekanso popanda lamulo; ndiponso monga ambiri anachimwa pansi pa lamulo adzaweruzidwanso ndi lamulo, 13(pakuti osati akumva lamulo ali olungama pamaso pa Mulungu6, koma iwo akuchita lamulo adzalungamitsidwa. 14Pakuti pamene [iwo ali] amitundu, amene alibe lamulo, achita mwa chikhalidwe zinthu za lamulo, amenewa pokhala opanda lamulo, akhala lamulo pa iwo okha; 15amene amaonetsa ntchito ya lamulo yolembedwa m’mitima mwao, chikumbumtima chao kuwachitiranso umboni, malingaliro awo kutsutsana kapena kunenezana wina ndi mzake pakati pawo;) 16m’tsiku limene Mulungu7 adzaweruza zinsinsi za anthu, molingana ndi uthenga wanga wabwino, mwa Yesu Khristu.

17Koma ngati iwe utchedwa Myuda, ndi kukhazikika m’lamulo, ndi kudzitamandira mwa Mulungu8, 18ndi kudziwa chifuniro, ndipo mwachidziwitso kuvomereza zinthu zimene zili zoposa, zolangizidwa kuchokera mu lamulo; 19ndipo ali nako kulimba mtima kuti iwe mwini uli mtsogoleri wa akhungu, kuwala kwa iwo amene ali mumdima, 20mlangizi wa anthu opusa, mphunzitsi wa makanda, okhala nawo maonekedwe a chidziwitso ndi choonadi ndi chikhulupiliro m’lamulo: 21iwe amene umaphunzitsa wina, kodi suziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikira kuti usabe, kodi umabanso? 22iwe amene umati [munthu sakuyenera] kuchita chigololo, umachitanso chigololo? Iwe wakudana nawo mafano, kodi umabanso za mkachisi? 23iwe amene umadzitamandira mu lamulo, kodi pa kulakwira kwako lamulo uchitira mwano Mulungu9? 24Pakuti dzina la Mulungu10 lichitidwa mwano pakati pa amitundu chifukwa cha inu, monga kwalembedwa. 25Pakuti mdulidwe umapindulanji ngati usunga lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, kudulidwa kwanu kumasanduka kusadulidwa. 26Pamenepo ngati kusadulidwa kusunga zofunikira za lamulo, kodi kusadulidwa kwake sikuyesedwa ngati mdulidwe, 27ndipo kusadulidwa mwa chibadwidwe, kokwaniritsa lamulo, kumaweruza inu, amene ndi lemba ndi mdulidwe, muchimwira lamulo? 28Pakuti iye siMyuda amene ali m’maonekedwe, kapena simdulidwe umene uli owonekera m’thupi; 29koma iye [ndi] Myuda [amene ali choncho] mkati mwake; ndi mdulidwe, wa mumtima, wa mumzimu, osati m’malembo;amene mayamiko ake sali a anthu, koma a Mulungu11.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu>1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10ElohimuElohimu11Elohimu