Mutu 7

1Ndipo zitapita izi ndinaona angelo anayi atayima pa ngodya zinayi za dziko lapansi, akugwira mphepo zinayi za dziko lapansi, kuti mphepo isaombe padziko lapansi, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse. 2Ndipo ndinaona mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa, okhala nacho chizindikiro cha Mulungu1 wamoyo; ndipo anafuula ndi mau akulu kwa angelo anayi aja amene analandira mphamvu kuononga dziko lapansi ndi nyanja, 3nanena, Usaononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidzawasindika chizindikiro akapolo a Mulungu2 wathu pamphumi pawo. 4Ndipo ndinamva chiwerengero cha iwo osindikidwa chizindikirowo, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi, osindikidwa chizindikiro kuchokera ku fuko lililonse la ana a Israyeli: 5kuchokera ku fuko la Yuda, zikwi khumi ndi ziwiri osindikizidwa; kuchokera ku fuko la Rubeni, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Gadi, zikwi khumi ndi ziwiri; 6kuchokera ku fuko la Aseri, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Nafitali, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Manase, zikwi khumi ndi ziwiri; 7kuchokera ku fuko la Simeoni, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Levi, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Isakara, zikwi khumi ndi ziwiri; 8kuchokera ku fuko la Zebuloni, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Yosefe, zikwi khumi ndi ziwiri; kuchokera ku fuko la Benjamini, zikwi khumi ndi ziwiri.

9Zitapita zinthu zimenezi ndinaona, ndipo taonani, khamu lalikulu, limene palibe akhoza kuliwerenga, kuchokera ku mitundu yonse ndi mafuko onse ndi anthu ndi zilankhulo, kuyimilira pamaso pa mpando wachifumu, ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi nthambi za kanjedza m’manja mwao. 10Ndipo anafuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu4 wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa. 11Ndipo angelo onse anayima mozungulira mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zolengedwa zamoyo zinayi, ndipo zinagwetsa nkhope zawo pansi pa mpando wachifumu, ndi kulambira Mulungu5, 12zinena, Amen: Mdalitso, ndi ulemelero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi mphamvu, kwa Mulungu6 wathu, ku nthawi za nthawi. Amen.

13Ndipo m’modzi wa akulu anayankha, nanena kwa ine, Awa amene avekedwa zovala zoyera, ndi ndani amenewa, ndipo akuchokera kuti? 14Ndipo ndinati kwa iye, Ambuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo iye anati kwa ine, Awa ndi amene anatuluka mu chisautso chachikulu, ndipo anachapa zovala zawo, ndipo anaziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. 15Pamenepo iwo ali ku mpando wachifumu wa Mulungu7, ndipo akumtumikira usana ndi usiku mkachisi mwake, ndipo iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawayalira iwo hema kuwaphimba. 16Sadzamvanso njala, kapenanso kumva ludzu, kapena dzuwa kuwagwera iwo, kapena kutentha kulikonse; 17hchifukwa Mwanawankhosa amene ali pakati pa mpando wachifumu adzawaweta iwo, ndipo adzawatsogolera ku kasupe wa madzi a moyo, ndipo Mulungu8 adzapukuta msozi ulionse wochoka m’maso mwao.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu