Mutu 5

1Tsopano poyesedwa olungama pa mfundo ya chikhulupiliro, tili nawo mtendere pa Mulungu1 kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; 2mwa ameneyu talowa mwachikhulupiliro m’kukonderedwa uku kumene ife tayimamo, ndipo tinyadira m’chiyembekezo cha ulemelero wa Mulungu2. 3Ndipo osati [ichi] chokha, komanso tinyadira m’masautso, podziwa kuti msautso umachita chipiliro; 4ndi chipiliro, chizolowezi; ndi chizolowezi, chiyembekezo; 5ndipo chiyembekezo sichitichititsa manyazi, chifukwa chikondi cha Mulungu3 chatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera amene anaperekedwa kwa ife: 6pakuti pokhalabe ife opanda mphamvu, mu nthawi yake Khristu anafera ochimwa. 7Pakuti nzosowa kuti kwa [munthu] wolungama akafere munthu wina, pakuti mwina kwa [munthu] wabwino kulimba mtima kufera munthu wina; 8koma Mulungu4 atsimikizira chikondi chake kwa ife, kuti pamene ife tinali ochimwabe, Khristu anatifera ife. 9Koposaposa pamenepo, pamene tinalungamitsidwa mu [mphamvu ya] mwazi wake, tidzapulumutsidwa ku mkwiyo mwa Iye. 10Pakuti ngati, pokhala adani, tayanjanitsidwa kwa Mulungu5 kudzera mu imfa ya Mwana wake, koposaposa, pamene tayanjanitsidwa, tidzapulumutsidwa mu [mphamvu ya] moyo wake. 11Ndipo osati [ichi] chokha, koma ife tili onyadira mwa Mulungu6, kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kudzera mwa iye tsopano talandira chiyanjanitso. 12Pa chifukwa ichi, monga mwa munthu m’modzi uchimo unalowa mdziko lapansi, ndi mwa uchimo imfa; ndipo pamenepo imfa inadutsa pa anthu onse, pakuti mwa ichi tonse tinachimwa: 13(pakuti kufikira lamulo tchimo linalowa m’dziko lapansi; koma tchimo silimawerengedwa pamene palibe lamulo; 14koma imfa inalamulira kuyambira Adamu mpaka Mose, ngakhale pa iwo amene sanachimwe mwa chifanizo cha kuchimwa kwa Adamu, amene ali chithunzithunzi cha iye amene akubwera. 15Komatu machitachita akukonderedwa sangafanane ndi kulakwa? Pakuti ngati mwa kulakwa kwa munthu m’modzi ambiri anafa, makamaka chachita chisomo cha Mulungu7, ndi mphatso ya ulere mu chisomo, chimene [chili] mwa munthu m’modzi Yesu Khristu, zinachulukira mwa ambiri. 16Ndipo osati mwa iye amene anachimwa kukhala mphatso? Pakuti chiweruzo chinali kwa iye wotsutsika, koma machitidwe a kukonderedwa, a zolakwa zambiri zinalungamitsidwa. 17Pakuti ngati mwa cholakwa cha munthu m’modzi imfa inalamulira kudzera mwa munthu m’modziyo, koposa kotani kwa iwo amene adzalandira chisomo chochuluka ndi mphatso ya ulere ya kulungama, ilamulira m’moyo mwa m’modzi Yesu Khristu:) 18kotero pamenepo monga [zinalili] mwa kulakwa kamodzi pa anthu onse kunadza kutsutsika, kotero kuti mwa kulungama kumodzi pa anthu onse kunadza kulungamitsidwa kwa moyo. 19Pakutidi mwa kusamvera kwa munthu m’modzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwechonso mwa kumvera kwa m’modzi ambiri ayesedwa olungama. 20Koma lamulo linalowa, cholinga kuti uchimo ukachulukire; koma pamene uchimo uchulukira chisomo chimachulukira kwambiri, 21kuti monga momwe uchimo unalamulira mu [mphamvu ya] imfa, koteronso chisomo chikalamulire kudzera mwa kulungama ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. 1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu