Mutu 5

1Zitapita zinthu izi panali phwando la Ayuda, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. 2Tsopano kumeneko m’Yerusalemu, pa chipata cha nkhosa, panali thamanda, limene limatchedwa m’Chiheberi, Betesda, lokhala nalo makumbi asanu. 3Ndipo m’menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala, [akudikira kuvundulidwa kwa madzi. 4Pakuti mngelo amatsikira nyengo ina m’thamanda navundula madzi. Aliyense woyambilira kulowa atavundulidwa madziwo amachiritsidwa, kumatenda alionse amene amavutika nawo.] 5Koma kunali munthu kumeneko amene amadwala m’chivutiko chake kwa zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. 6Yesu poona [munthu] ameneyu, nadziwa kuti ali [m’nyengo imeneyo] kwa nthawi yaitali tsopano, anati kwa iye, Ufuna kuchiritsidwa kodi? 7[Munthu] wodwalayo anamuyankha Iye, Ambuye, ndilibe munthu, pamene madzi avundulidwa, andiponye ine m’thamanda; komatu pamene ine ndifika wina abwera patsogolo panga. 8Yesu anati kwa iye, Tauka, yalula mphasa yako nuyende. 9Ndipo nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa, nayalula mphasa yake nayenda: ndipo tsiku limenelo linali la sabata. 10Pamenepo Ayuda anati kwa [munthu] wochiritsidwayo, Ndi pasabata, sikololedwa kwa iwe kuyalula mphasa yako. 11Iye anawayankha iwo, Iye amene wandichiritsa ine, anati kwa ine, Yalula mphasa yako nuyende. 12Iwo anamufunsa iye [pamenepo], Ndani amene ananena kwa iwe, Yalula mphasa yako nuyende? 13Komatu iye amene anachiritsidwa sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anachoka kachetechete, pakuti pamenepo panali khamu lalikulu. 14Zitapita zinthu izi Yesu anampeza iye m’kachisi, ndipo anati kwa iye, Taona, wachiritsidwa: usakachimwenso, kuti chinthu china choipa chisachitike kwa iwe. 15Munthuyo ananyamuka nauza Ayuda kuti anali Yesu amene anamchiritsa iye. 16Ndipo pachifukwa chimenechi Ayuda anamlondalonda Yesu [nafuna kumupha Iye], chifukwa anachita zinthu zimenezi pa sabata. 17Koma Yesu anawayankha iwo, Atate wanga agwira ntchito kufikira pano ndipo Inenso ndigwira ntchito. 18Pachimenechi Ayuda anafunabe kumupha Iye, chifukwa sanangophwanya sabata kokha, komanso kuti anati Mulungu1 ndi Atate wake, kudzipanga yekha wofanana ndi Mulungu2. 19Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Mwana sangapange kanthu pa Iye yekha, koma chokhacho chimene Iye waona Atate akuchita: pakuti zinthu zonse zimene Iye azichita, zinthu zimenezonso Mwana achita chimodzimodzi. 20Pakuti Atate akonda Mwana ndipo amuonetsa Iye zinthu zonse zimene Iye mwini azichita; ndipo Iye amuonetsa ntchito zazikulu kuposa izi, kuti mudabwe. 21Pakuti ngakhale monga Atate adzutsa akufa ndi kuwapatsa [iwo] moyo, chomwechonso Mwana apereka moyo kwa iwo amene Iye afuna: 22pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka chiweruzo chonse kwa Mwana; 23kuti onse akalemekeze Mwana, monga umo alemekeza Atate. Iye amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene anamtuma Iye. 24Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupilira Iye amene anandituma, ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’kuweruza, koma wachotsedwa ku imfa ndi kulowa m’moyo. 25Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, kuti ola likubwera, ndipo lafika, pamene akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu3, ndipo iwo amene adzamva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti ngakhale Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, kotero waperekanso kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha, 27ndipo anampatsa Iye ulamuliro kuperekanso chiweruzo, chifukwa Iye ndi Mwana wa munthu. 28Musadabwe ndi izi, pakuti ola likubwera pamene onse amene ali m’manda adzamva mau ake, 29ndipo adzamuka; iwo amene anachita zabwino, ku kuuka kwa moyo, ndipo iwo amene achita zoipa, ku kuuka kwa chiweruzo. 30Sindingathe kuchita kanthu pandekha; monga Ine ndikumvera, ndiweruza, ndipo chiweruzo changa ndi cholungama, chifukwa sindipanga chifuniro changa, komatu chifuniro cha Iye amene wandituma Ine. 31Ngati ndichitira umboni okhudza Ine mwini, umboni wanga suli woona. 32Wochita umboni wokhudza Ine ndi wina, ndipo Ine ndidziwa kuti umboni umene achitira wokhudza Ine ndi woona. 33Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anakuchitirani umboni wa choonadi. 34Koma Ine sindilandira umboni kuchoka kwa munthu, koma ndalankhula izi kuti inu mukapulumutsidwe. 35Iye anali nyali yoyaka ndi yowala, ndipo inu munafunitsitsa kwa kanthawi kusangalala m’kuwala kwake. 36Koma Ine ndili ndi mboni [imene ili] yaikulu kuposa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa kuti ndizimalizitse, ntchito zimene Ine ndizichita, zindichitira umboni okhudza Ine kuti Atate ndi amene anandituma ine. 37Ndipo Atate amene anandituma Ine anandichitira mwini umboni okhudza Ine. Inutu simunamva mau ake nthawi ina iliyonse, kapena kuona maonekedwe ake, 38ndipo inu simunalole mau ake akhazikike mwa inu; pakuti Iye amene anamtuma, inu simunamkhulupilire. 39Mufunafuna malemba, pakuti muganiza kuti m’menemo muli nawo moyo wosatha, ndipo iwo ndi amene achitira umboni okhudza Ine; 40ndipo inu simubwera kwa Ine kuti mukhale nawo moyo. 41Ine sindilandira ulemelero kuchokera kwa anthu, 42koma Ine ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu4 mwa inu. 43Ine ndadza m’dzina la Atate wanga, ndipo inu simundilandira; ngati wina abwera m’dzina lake, ameneyo mumlandira. 44Kodi mukhulupilira bwanji, inu amene mulandira ulemelero kwa wina ndi mzake, ndipo simufuna ulemelero umene [umachokera] kwa Mulungu5 yekha? 45Musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate: alipo [m’modzi] wokunenezani inu, Mose, amene inu mumkhulupilira; 46pakuti ngati mukanakhulupilira Mose, mukanakhulupilira Inenso, pakuti iye analemba zokhudza Ine. 475Koma ngati simukhulupilira zolemba zake, mudzakhulupilira bwanji mau anga?

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu