Mutu 14

1Ndipo ndinaona, taonani, Mwanawankhosa atayima pa phiri la Ziyoni, ndi iye zikwi mphambu makumi anayi kudza anayi, olembedwa pa mphumi pawo dzina lake ndi dzina la Atate wake. 2Ndipo ndinamva mau kuchokera m’mwamba okhala ngati mkokomo wa madzi ochuluka, ndi ngati mau a bingu lalikulu. Ndipo mau amene ndinamva [anali] monga a oimba azeze kuyimba azeze awo; 143ndipo iwo anayimba nyimbo yatsopano pa mpando wachifumu, ndiponso pamaso pa zolengedwa zamoyo zinayi ndi akulu. Ndipo palibe amene anaphunzira nyimboyo kupatula zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi amene anagulidwa kuchoka padziko lapansi. 4Amenewa ndiwo amene sanadetsedwe ndi akazi, pakuti adakali anamwali: amenewa ndiwo amene anatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene anapita. Iwowa anagulidwa kuchoka kwa anthu [monga] zipatso zoyambilira kwa Mulungu1 ndi kwa Mwanawankhosa: 5ndipo mkamwa mwao munalibe bodza limene linapezeka; [pakuti] iwo alibe banga.

6Ndipo ndinaona mngelo wina akuuluka mkatikati mwa thambo, wakukhala nawo uthenga wabwino wamuyaya kulalikidwa kwa iwo akukhala padziko lapansi, ndi ku fuko lililonse ndi mtundu ndi manenedwe ndi anthu, 7nanena ndi mau okweza, Opani Mulungu2 ndipo mpatseni iye ulemelero, pakuti nthawi ya chiweruzo chake yafika; ndipo mlambireni iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe a madzi.

8Ndipo wina, mngelo wachiwiri anatsatira, nanena, Babulo wamkulu wagwa, wagwa, amene vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake unamwedwa ndi mitundu yonse.

9Ndipo wina, mngelo wachitatu anawatsata iwo, nanena ndi mau akulu, ngati aliyense adzalambira chilombo ndi chifanizo chake, ndi kulandira chizindikiro pamphumi pake kapena pa dzanja pake, 10ameneyonso adzamwa vinyo wa mkwiyo wa Mulungu3 wokonzedwera mosasakaniza m’chikho cha mkwiyo wake, ndipo adzalangika m’moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera ndi pamaso pa Mwanawankhosa. 11Ndipo utsi wa chilango chake udzapita ku nthawi za nthawi, ndipo alibe mpumulo usana ndi usiku amene alambira chirombocho ndi chifanizo chake, ndiponso ngati wina akalandira chizindikiro cha dzina lake. 12Pano pali chipiliro cha oyera mtima, amene asunga malamulo a Mulungu4 ndi chikhulupiliro cha Yesu.

13Ndipo ndinamva mau kuchokera m’mwamba akunena, Lemba, Odala akumwalira amene amwalira mwa Ambuye kuyambira tsopano. Inde, atero Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zimawatsata.

14Ndipo ndinaona, taonani, mtambo woyera, ndipo pa mtambo wakukhalapo onga Mwana wa munthu, wakukhala naye pamutu pake korona wa golide, ndi m’manja mwake chikwawa chakuthwa. 15Ndipo mngelo wina anatuluka mkachisi, akulira ndi mau okweza kwa iye wakukhala pa mtambo, Tumiza chikwakwa chako ndipo ukakolole; pakuti nthawi ya kukolola yafika, pakuti zokolola za dziko lapansi zauma. 16Ndipo iye wakukhala pa mtambo anayika chikwakwa chake padziko lapansi, ndipo dziko lapansi linakololedwa.

17Ndipo mngelo wina anatuluka m’kachisi amene ali kumwamba, iyenso anali nacho chikwakwa chakuthwa. 18Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa, wakukhala nazo mphamvu pa moto, ndipo anayitana ndi mau ofuula kwa iye amene anali ndi chikwakwa chakuthwa, nanena, Tumiza chikwakwa chako chakuthwa, ndipo usonkhanitse mitolo ya mpesa ya dziko lapansi; pakuti zipatso zake zakhwima. 19Ndipo mngelo anayika chikwakwa chake padziko lapansi, ndipo anasonkhanitsa mpesa wa dziko lapansi, ndipo anaponya [nthambi] m’choponderamo mpesa wa mkwiyo wa Mulungu5; 20 ndipo choponderamo mpesa chinapondedwa kunja kwa mzinda, ndipo mwazi unatuluka m’choponderamo mpesa kufikira zidutswa za akavalo kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu