Mutu 6

1Ndipo Iye anatuluka kumeneko nabwera kudziko lake lomwe, ndipo ophunzira ake anamlondola. 2Ndipo pamene sabata linafika Iye anayamba kuphunzitsa mu sunagoge, ndipo ambiri amene anamva anali odabwa, nanena, Azitenga kuti zinthu izi [munthu] uyu? Ndipo ndi nzeru yotani yopatsidwa kwa Iye, ndi ntchito ya mphamvu yochitidwa ndi manja ake? 3Kodi uyu sim’misiri wa matabwa, Mwana wa Mariya, ndi m’bale wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali ndi ife konkuno? Ndipo iwo anakhumudwa mwa Iye. 4Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri samanyozeka kupatula m’dziko lake lomwe, komanso pakati pa abale ake, ndi m’nyumba mwake momwe. 5Ndipo Iye sanachite ntchito iliyonse ya mphamvu kumeneko, kupatula kusanjika manja ake pa anthu odwala owerengeka amene anawachiritsa. 6Ndipo Iye anali wodabwa chifukwa cha kusakhulupilira kwao. Ndipo Iye anayendayenda mozungulira midzi naphunzitsa.

7Ndipo anadziitanira kwa [Iye] khumi ndi awiriwo; ndipo anayamba kuwatumiza iwo awiri [ndi] awiri, ndipo anawapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa; 8ndipo anawalamulira iwo kuti asatenge kanthu panjira, kupatula ndodo yokha; asatenge mfundo zolembedwa, asatenge mkate, anatenge ndalama m’malamba awo; 9komatu avale nkhwaira, ndipo asavale zovala mthupi ziwiri. 10Ndipo Iye anati kwa iwo, Kulikonse kumene mudzalowa m’nyumba, khalani komweko kufikira inu mutachokako. 11Ndipo malo alionse kumene sakulandirani kapena kumvera inu, tulukani kumeneko, tsatsani fumbi la kunsi kwa mapazi anu likhale umboni kwa iwo. 12Ndipo iwo anapita nalalikira kuti anthu alape; 13ndipo iwo anatulutsa ziwanda zochuluka, nadzoza mafuta odwala ambiri, nawachiritsa.

14Ndipo mfumu Herode anamva [za Iye] (pakuti dzina lake linatchuka), nati, Yohane m’batizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye. 15Ndipo ena anati, ndi Eliya; ndiponso ena anati, ndiye mneneri, monga m’modzi mwa aneneri. 16Koma Herode pamene anamva [ichi] anati, Yohane amene ndinamdula mutu, ndi iyeyu; wauka [kwa akufa]. 17Pakuti ndi Herode yemweyu amene anatuma ndi kum’gwira Yohane, ndipo anamtsekera mndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa Filipo m’bale wake, chifukwa anamkwatira iye. 18Pakuti Yohane ananena kwa Herode, sikololedwa kuti iwe ukwatire mkazi wa m’bale wako. 19Komatu Herodiya anachisunga ichi [m’malingaliro mwake] motsutsana ndi iye, ndipo anafunitsitsa atamupha, ndipo sanakwanitse: 20pakuti Herode amaopa Yohane podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga bwino iye; ndipo pakumumva, akuchita zinthu zambiri, ndipo anamumva iye mokondwera. 21Ndipo pamene linafika tsiku la tchuthi, pamene Herode, amakumbukira tsiku lake lobadwa, anakonzera mgonero akazembe ake, ndi akuluakulu ankhondo komanso [anthu] a chifumu aku Galileya; 22ndipo mwana wamkazi wa Herodiyayu atalowa, ndi kuvina, anasangalatsa Herode ndi iwo onse amene anali [naye] pagome; ndipo mfumu inati kwa buthuli, Pempha chilichonse chimene iwe ufuna ndipo ndidzakupatsa. 23Ndipo anamulumbilira iye, chilichonse chimene iwe udzandipempha ndidzakupatsa, kufikira theka la ufumu wanga. 24Ndipo iye anatuluka panja, nanena kwa mayi wake, Kodi ndipemphe chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wa Yohane m’batizi. 25Ndipo pomwepo pakulowa mwachangu kwa mfumu, anapempha nati, Ine ndikufuna mwachangu mundipatse mutu wa Yohane m’batizi mu mbizi. 26Ndipo mfumu, [pamene] inamva chisoni, koma chifukwa cha lumbiro limene anapanga ndi iwo amene anali [naye] pagome sakanatha kuphwanya mau ake kwa buthulo. 27Ndipo pomwepo mfumuyo, pakutumiza m’modzi wa alonda, analamula kuti mutu wake ubweretsedwe. Ndipo iye anatuluka napita kukamdula mutu m’ndende, 28ndipo anabweretsa mutu wake mu mbizi, ndi kupereka kwa buthulo, ndipo butulo linapereka mutuwo kwa mayi wake. 29Ndipo ophunzira ake atamva [ichi], anabwera natenga thupi lake, naliika m’manda.

30Ndipo atumwi anasonkhanira pamodzi kwa Yesu. Ndipo iwo anafotokozera kwa Iye zinthu zonse, zimene iwo anachita komanso zimene anaphunzitsa. 31Ndipo Iye ananena kwa iwo, Bwerani inu nokha padera kumalo a chipululu kuti mupumule pang’ono. Pakuti iwo amene amabwera ndi ena kupita anali ochuluka, ndipo iwo sanapeze mpata wopuma ndi kudya. 32Ndipo iwo anachoka napita kumalo a chipululu pa ngalawa. 33Ndipo ambiri anawaona iwo akupita, ndipo anawazindikira, ndipo anathamanga pamodzi wapansi, natuluka m’mizinda yawo yonse, ndipo anayamba kufika [kumeneko] asanafike iwo.

34Ndipo potuluka [m’ngalawa] [Yesu] anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anagwidwa chifundo pa iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. 35Ndipo pamene dzuwa linapendeka ndithu, ophunzira ake anabwera nanena kwa Iye, Malo ano ndi achipululu, ndipo dzuwa lapendeka kale; 36awuzeni apite kumiraga ndi kumidzi yozungulira, ndipo akadzigulire okha mkate, pakuti alibe kanthu kakudya. 37Ndipo Iye poyankha anati kwa iwo, Apatseni ndinu kudya. Ndipo iwo anati kwa Iye, Kodi tipite tikagule mkate wokwana marupiya mazana awiri ndi kuwapatsa kudya? 38Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi muli ndi mikate ingati? Pitani [ndipo] mukaone. Ndipo pamene iwo anadziwa anati, Isanu ndi nsomba ziwiri. 39Ndipo Iye anawalamulira kuwakhazika iwo m’magulu pa msipu wobiriwira. 40Ndipo iwo anakhala m’magulu a anthu zana limodzi komanso makumi asanu. 41Ndipo atatenga mikate isanu ndi nsomba ziwiri, anayang’ana kumwamba, nazidalitsa, ndipo ananyema mikate, napereka [iyo] kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa iwo. Ndipo nsomba ziwiri Iye anazigawa kwa iwo onse. 42Ndipo onse anadya ndi kukhuta. 43Ndipo anatolera makombo nadzaza mitanga khumi ndi iwiri, ndi nsomba. 44Ndipo iwo amene anadya anali amuna zikwi zisanu.

45Ndipo pomwepo anawalamulira ophunzira ake kupita kukakwera ngalawa, ndi kupita tsidya lina la Betsaida, pamene Iye anauzanso khamulo kuti lidzipita. 46Ndipo, atawalola iwo kuchoka, Iye ananyamuka napita kuphiri kukapemphera.

47Ndipo pofika madzulo, ngalawa inali pakati pa nyanja, ndipo Iye yekha anali kumtunda. 48Ndipo powaona iwo akuvutika ndi kupalasa, pakuti mphepo imalimbana nawo, inali ngati ola lachinayi la ulonda Iye anadza kwa iwo akuyenda panyanja, ndipo akanatha kuwadutsa iwo. 49Koma iwo pakumuona Iye akuyenda panyanja, anaganiza kuti akuona mzukwa, ndipo anafuula. 50Pakuti onse anamuona ndipo anasautsika. Ndipo pomwepo Iye analankhula ndi iwo, ndi kuti, Limbani mtima: Ndinetu musaope. 51Ndipo Iye anapita kwa iwo m’ngalawa, ndipo mphepo inaleka. Ndipo anali ozizwa mwa iwo okha mopitilira muyeso, nadabwa; 52pakuti iwo sanamvetse za mkatewo: pakuti mtima wao unaumitsidwa.

53Ndipo ataoloka, anafika kumtunda kwa Genesareti nakocheza kumeneko. 54Ndipo pakutsika m’ngalawa, pomwepo pakumzindikira Iye, 55iwo anathamanga m’dziko lonselo nayamba kutengera iwo amene anali kudwala pa makama, kumene anamva kuti Iye anali. 56Ndipo kulikonse kumene Iye analowa m’midzi, kapena m’mizinda, kapena m’maiko, iwo anaika odwala m’misika, ndipo anampempha Iye kuti akangokhudza mphonje ya chovala chake; ndipo ambiri amene anamkhudza anachiritsidwa.