Mutu 16
1Zinthu izi ndalankhula kwa inu kuti musakhumudwitsidwe. 2Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ola likubwera kuti aliyense wakupha inu adzaganiza kuti akutumikira Mulungu1; 3ndipo iwo adzachita zinthu izi chifukwa sanam’dziwe Atate kapena Ine. 4Koma ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti pamene ola lawo lifika, mudzakumbukire, kuti ndinalankhula [awa] kwa inu. Komatu sindinalankhule zinthu izi kwa inu pachiyambi, chifukwa Ine ndinali ndi inu. 5Koma tsopano ndipita kwa Iye amene anandituma Ine, ndipo palibe mwa inu amene wandifunsa, Mukupita kuti? 6Koma chifukwa ndalankhula zinthu izi kwa inu, chisoni chadzadza m’mitima mwanu. 7Koma ndinena zoona kwa inu, Nzopindulitsa kwa inu kuti ndichoke; pakuti ngati sindichoka, Mtonthozi sabwera kwa inu; koma ndikachoka ndidzamtumiza Iye kwa inu. 8Ndipo akadzabwera, adzaonetsera ku dziko lapansi, za uchimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruzo: 9za uchimo, chifukwa sanakhulupilire pa Ine; 10za chilungamo, chifukwa ndipita kwa Atate wanga, ndipo simudzandionanso; 11za chiweruzo, chifukwa wolamula wa dziko lapansi waweruzidwa.
12Ndili nazobe zinthu zambiri zolankhula ndi inu, koma simungazimvetse pano. 13Koma Iye akadzabwera, Mzimu wa choonadi, adzakutsogolerani mu choonadi chonse: pakuti Iye sadzalankhula za Iye mwini; koma zimene Iye azazimva adzazilankhula; ndipo adzalengeza kwa inu chimene chikubwera. 14Iye adzalemekeza Ine, pakuti adzalandira za Ine ndipo adzazilengeza kwa inu. 15Zinthu zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga; pa chifukwa chimenechi ndanena kuti adzalandira za Ine ndipo adzazilengeza kwa inu. 16Mu kanthawi kochepa simudzandionanso Ine; ndiponso mu kanthawi kochepa mudzandiona Ine, ndipo, Chifukwa Ine ndipita kwa Atate? 17Pamenepo [ena] mwa ophunzira ake anati kwa wina ndi mzake, Ndi chani ichi chimene akunena kwa ife, Mu kanthawi kochepa simudzandionanso Ine; ndiponso mu kanthawi kochepa mudzandiona Ine, ndipo, Chifukwa Ine ndipita kwa Atate? 18Pamenepo iwo anati, Kodi ndi chiyani ichi akunena [za] kanthawi kochepa? Ife sitikudziwa [za] chimene Iye akulankhula. 19Pamenepo Yesu anadziwa kuti iwo amafuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mukufunsana za ichi pakati panu kuti ndanena, Kanthawi kochepa simudzandionanso Ine; ndiponso mu kanthawi kochepa mudzandiona Ine? 20Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, kuti mudzalira ndi kubuma, inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; ndipo inu mudzachita chisoni, koma chisoni chanu chidzasanduka chimwemwe. 21Pamene mkazi, akubereka mwana, amakhala ndi chisoni chifukwa ola lake lafika; koma pamene mwana wabadwa, samakumbukiranso za mavuto, pachifukwa cha chimwemwe kuti munthu wabadwa m’dziko lapansi. 22Ndipo inu tsopano muli nacho chisoni; koma ndidzakuonaninso, ndipo mitima yanu idzasangalala, ndipo chimwemwe chanu palibe munthu angakuchitireni. 23Ndipo m’tsiku limenelo simudzafunsa kanthu kwa Ine: zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Chilichonse chimene mudzapempha kwa Atate m’dzina langa, adzakupatsani. 24Kufikira pano palibe chimene mwapempha m’dzina langa: pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chidzaze. 25Zinthu izi ndalankhula kwa inu m’mafanizo; ola likubwera kuti sindidzalankhulanso kwa inu m’mafanizo, koma ndidzalankhula kwa inu mwachindunji zokhudza Atate. 26Tsiku limenelo mudzapempha m’dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti ndidzakupempherani kwa Atate m’malo mwanu, 27pakuti Atate mwini ali nacho chikondi pa inu, chifukwa munali nacho chikondi pa Ine, ndipo munakhulupilira kuti ndinachokera kwa Mulungu2. 28Ine ndinachokera kwa Atate ndipo ndinabwera padziko lapansi; ndikuchokanso padziko lapansi, ndipo ndikupita kwa Atate.
29Ophunzira ake anati kwa Iye, Taonani, tsopano Inu mwayamba kulankhula mwachindunji ndipo simukulankhulanso m’mafanizo. 30Tsopano ife tadziwa kuti inu mukudziwa zinthu zonse, ndipo palibe kusoweka kuti wina akufunseni Inu. Pachimenechi ife tikukhulupilira kuti munachokera kwa Mulungu3. 31Yesu anawankha iwo, Kodi tsopano mwakhulupilira? 32Taonani, ola likubwera, ndipo lafika, kuti mudzabalalitsidwa, aliyense ku zake zomwe, ndipo mudzandisiya Ine ndekha; komabe Ine sindili ndekha, pakuti Atate ali ndi Ine. 33Zinthu izi ndalankhula kwa inu kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. M’dziko lapansi muli nawo mazunzo; koma khalani olimba mtima: Ine ndalilaka dziko lapansi.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu