Mutu 4
1Ndipo Petro ndi Yohane analowa limodzi m’kachisi pa ola la pemphero, [limene ndi] ola lachisanu ndi chinayi; 2ndipo munthu wina amene anali wolumala kuchokera m’mimba mwa mayi wake ananyamulidwa, amene tsiku lililonse amayikidwa pa chipata cha kachisi chotchedwa Chokongola; 3ameneyu, poona Petro ndi Yohane akufuna kulowa m’kachisi, anawapempha zaulere. 4Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang’ane ife. 5Ndipo iye anawavomereza iwo, kuyembekezera kuti adzalandira kenakake kuchokera kwa iwo. 6Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; komatu chimene ndili nacho, chimenechi ndikupatsa iwe: m’dzina la Yesu Khristu Mnazarayo tauka nuyende. 7Ndipo anamugwira dzanja lake lamanja ndi kumdzutsa, ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi mafupa a mfundo za kumapazi kwake zinalimbitsidwa. 8Ndipo mopintchama iye anayimilira nayenda, ndipo analowa pamodzi nawo m’kachisi, akuyenda, ndi kupintchama, ndi kutamanda Mulungu1. 9Ndipo anthu onse anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu2; 10ndipo iwo anamzindikira iye, kuti anali amene amakhala akupemphetsa pa chipata Chokongola cha kachisi; ndipo iwo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa zimene zinachitika kwa iye. 11Ndipo pamene iye anagwiritsitsa Petro ndi Yohane, anthu onse anathamangira pamodzi kwa iwo mu khumbi limene limatchedwa la Solomo, ali odabwa zedi.
12Ndipo Petro, poona ichi, anawayankha anthuwo, Amuna inu a Israyeli, chifukwa chiyani mukuzizwa ndi ichi? Kapenanso chifukwa chiyani mukutipenyetsetsa ife ngati kuti mwa mphamvu yathu ndi chipembedzo chathu tamuyendetsa iye? 13Mulungu3 wa Abrahamu ndi Isake ndi Yakobo, Mulungu4 wa atate athu, walemekeza mtumiki wake Yesu, amene inu munampereka, ndi kumukana pamaso pa Pilato, pamene iye anamuweruza kuti amasulidwe. 14Koma inu munamukana Woyerayo ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu amene anali wakupha amasulidwe kwa inu; 15koma mwini wake wa moyo inu munamupha, amene Mulungu5 anamuukitsa pakati pa akufa, pamenepo ndife mboni. 16Ndipo, mwachikhulupiliro m’dzina lake, dzina lakelo linampanga [munthu] uyu kukhala wolimba amene inu munamuona ndi kumdziwa; ndipo chikhulupiliro chimene chili mwa iye chamupatsa kuchira kwathunthu pamaso pa inu nonse. 17Ndipo tsopano, abale, ndikudziwa kuti munachita ichi mwa umbuli, monganso a ulamuliro anu; 18komatu Mulungu6 wakwaniritsa chimene anachinena kale lomwe pakamwa pa aneneri, kuti Khristu wake akazunzike. 19Pamenepo lapani ndi kutembenuka, kufafanizidwa kwa machimo anu, kuti nthawi zakutsitsimuka zibwere kuchokera pamaso pa Ambuye, 20ndipo akatumize Yesu Khristu, amene anazodzedweratu pa inu, 21amenedi kumwamba kuyenera kumlandira kufikira nthawi ya kubwenzeretsedwa kwa zinthu zonse, imene Mulungu7 analankhula ndi pakamwa pa aneneri ake oyera kuchokera nthawi yoyamba. 22Mose ananenadi kuti, Mulungu8 adzaukitsira kwa inu mneneri pakati pa abale anu monga ine: ameneyo mudzamumvera zilizonse zimene adzalankhula kwa inu. 23Ndipo kudzatero kuti moyo uliwonse umene sudzamvera mneneri ameneyo udzaonongeka pakati pa anthu. 24Ndipodi aneneri onse kuchokera pa Samueli ndi onse amene analowa m’malo mwake, onse amene analankhula, analengeza za masiku amenewa. 25Ndinu ana a aneneri ndi a pangano limene Mulungu9 anaikiza kwa makolo athu, nanena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbewu yako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsika. 26Kuyambira kwa inu Mulungu10, ataukitsa mtumiki wake, anamtuma Iye, kukadalitsa inu pakutembenuza aliyense [wa inu] kuchoka ku zoipa zanu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu