Mutu 24
1Koma tsiku lotsatira la sabata, m’bandakucha, iwo anafika kumanda, atatenga zonunkhira zimene anakonza. 2Ndipo anapeza mwala wokunkhunizidwa pa khomo la manda wosema. 3Ndipo pamene iwo analowa sanapeze thupi la Ambuye Yesu. 4Ndipo kunachitika kuti pamene iwo anazingwa za ichi, kuti taonani, amuna awiri anayimilira pafupi nawo atavala zonyezimira. 5Ndipo pamene iwo anadzazidwa ndi mantha anaweramira nkhope zawo pansi, nanena kwa iwo, Chifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? 6Iye sali muno, koma wauka: kumbukirani momwe Iye analankhulira kwa inu, adakali mu Galileya, 7anati, Mwana wa munthu akuyenera kuperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa, ndi kupachikidwa, ndi kuukanso tsiku lachitatu. 8Ndipo iwo anakumbukira mau ake; 9ndipo, atachoka kumanda, anafotokozera zonse izi kwa khumi ndi m’modziwo ndi ena onse. 10Tsopano anali Mariya wa Magadala, ndi Yohana, ndi Mariya [amake] a Yakobo, ndi iwo anali nawo pamodzi, amene anawafotokozera zinthu izi ophunzirawo. 11Ndipo mau awo anaoneka ngati nthano m’maso mwao, ndipo sanawakhulupilire iwo. 12Koma Petro, anayimilira, nathamanga kupita kumandako, ndipo powerana anaona nsalu ya bafuta anamkulungayo itatsala yokha, ndipo anapita kunyumba, ali wodabwa ndi zochitikazo.
13Ndipo taonani, awiri mwa iwo tsiku lomwelo amapita kumudzi wotchedwa Emau umene mtunda wake unali wotalika ma stadiya makumi asanu ndi limodzi kuchokera ku Yerusalemu; 14ndipo iwowa amakambitsana wina ndi mzake zokhudza zinthu zimene zinachitikazo. 15Ndipo kunachitika pamene iwo amakambirana ndi kufunsana, kuti Yesu mwini anayandikira, nayenda nawo pamodzi; 16koma maso awo anatsekeka kotero kuti sanamzindikire Iye. 17Ndipo Iye anati kwa iwo, Zokambirana zanji izi mukuchita pakati panu pamene mukuyenda, ndi kuyang’ana pansi? 18Ndipo m’modzi [wa iwo], dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi ukuyenda wekha mu Yerusalemu, ndipo sukudziwa zimene zachitika m’masiku awa? 19Ndipo Iye anati kwa iwo, Zinthu zake ziti? Ndipo iwo anati kwa Iye, Zinthu zokhudza Yesu Mnazarayo, amene anali mneneri wamphamvu mu ntchito ndi m’mau pamaso pa Mulungu1 ndi anthu onse; 20ndi momwe ansembe akulu ndi akulu athu anamperekera Iye ku chiweruzo cha imfa ndi kumpachika. 21Koma ife tinali ndi chiyembekezo kuti Iye anali [yemweyo] amene akuyenera kuombola Israyeli. Komatu pamenepo, pambali pa zonsezi, tsopano, lero ndi tsiku lachitatu chichitikire zimenezi. 22Ndipo akazi ena pakati pathu atidabwitsa ife, atapita m’bandakucha kumanda, 23ndipo, sanapeze thupi lake, anabwera, nanena kuti anaonanso masomphenya a angelo, amene ananena kuti Iye ali ndi moyo. 24Ndipo ena mwa ife anapita kumanda, ndipo anapezadi kuti zili chomwecho, monga umo akazi ananenera, koma Iyeyo sanamuone. 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Osaganiza ndi osakhulupilira mtima msanga zimene aneneri analankhula! 26Sanayenera kodi Khristu kuvutika zinthu zimenezi ndi kulowa mu ulemelero wake? 27Ndipo kuyambira kwa Mose ndi aneneri onse, Iye anawatanthauzira iwo m’malemba monse zokhudza Iye mwini. 28Ndipo iwo anayandikira m’mudzi m’mene amapita, ndipo Iye anachita ngati akupitilirabe. 29Ndipo iwo anamkakamiza Iye, nanena, Khalani ndi ife, pakuti kuli madzulo ndipo dzuwa likupendeka. Ndipo Iye analowa nakhala nawo. 30Ndipo kunachitika kuti pamene Iye anali nawo pa gome, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, nawapatsa iwo. 31Ndipo maso awo anatseguka, ndipo iwo anamzindikira Iye. Ndipo anasowa pakati pawo. 32Ndipo iwo anati kwa wina ndi mzake, Kodi mtima wathu sunatenthe pamene amalankhula nafe panjira paja, [ndiponso] pamene Iye anatitsegulira ife malemba? 33Ndipo iwo ananyamuka ola lomwelo, nabwerera ku Yerusalemu. Ndipo iwo anawapeza khumi ndi m’modziwo, ndi iwo amene anali nawo, atasonkhana pamodzi, 34nanena, Ambuye waukadi ndipo anawonekera kwa Simoni. 35Ndipo iwo anafotokozera zimene [zinachitika] panjira, ndi momwe Iye anazidziwitsa kwa iwo m’kunyema mkate.
36Ndipo pamene iwo amanena zinthu izi, Iye mwini anaima pakati pawo, nanena kwa iwo, Mtendere ukhale kwa inu. 37Koma iwo, poopsedwa ndi kuchita mantha, anayesa kuti akuona mzimu. 38Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukuvutika? Ndipo chifukwa chiyani malingaliro anu akukula m’mitima mwanu? 39Taonani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine amene. Ndikhudzeni ndi kuona, pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuona Ine ndili nazo. 40Ndipo Iye atalankhula izi anawaonetsa iwo manja ake ndi mapazi ake. 41Koma pamene iwo anali osakhulupilirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo anali odabwa, Iye anati kwa iwo, Kodi muli ndi kanthu pano kakudya? 42Ndipo iwo anampatsa chidutswa cha nsomba yokazinga ndi malesa a uchi; 43ndipo Iye anatenga nadya pamaso pawo. 44Ndipo Iye anati kwa iwo, Awa ndi mau amene ndinalankhula nanu pamene ndinali nanu, kuti zonse zimene zinalembedwa zokhudza Ine m’chilamulo cha Mose ndi aneneri ndi Masalmo zikwaniritsidwe. 45Pamenepo Iye anatsegula malingaliro awo kumvetsetsa malembo, 46ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, ndiponso kunayenera kuti Khristu akamve zowawa, ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu; 47ndi kuti kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kulalikidwe m’dzina lake kwa mitundu yonse kuyambira ku Yerusalemu. 48Ndipo ndinu mboni ya zinthu zimenezi. 49Ndipo taonani, nditumiza lonjezano la Atate wanga pa inu; koma mukhalebe mu mzindamu kufikira mutavekedwa ndi mphamvu yochokera kumwamba.
50Ndipo Iye anawatsogolera kukafika mpaka ku Betaniya, ndipo anakweza manja ake, nawadalitsa iwo. 51Ndipo kunachitika pamene Iye amawadalitsa iwo, anachotsedwa pakati pawo ndipo anatengedwa kupita kumwamba. 52Ndipo iwo, anamlambira Iye, nabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu, 53ndipo anakhalabe m’kachisi nalemekeza ndi kuyamika Mulungu2.
1Elohimu2Elohimu