Mutu 10

1Pakuti ine sindifuna kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu anali pansi pa mtambo, ndipo onse anawoloka nyanja; 2ndipo onse anabatizidwa mwa Mose mu mtambo ndi m’nyanja; 3ndipo onse anadya chakudya cha uzimu chomwecho, 4ndipo onse anamwa chakumwa cha uzimu chomwecho, pakuti iwo onse anamwa pa mwala wa uzimu umene unawatsata [iwo]: (tsopano mwalawu unali Khristu;) 5komabe Mulungu1 sanakondwere nawo ambiri a iwo, pakuti anamwazidwa m’chipululu. 6Koma zinthu izi zinachitika [monga] chitsanzo kwa ife, kuti tisamalakelake zinthu zoipa, monga iwonso analakalaka. 7Kapena musamapembedze mafano, monga anachita ena mwa iwo; pakuti kwalembedwa, Anthu anakhala pansi nadya ndi kumwa nauka ndi kusewera. 8Kapena tisamachite chigololo, monga ena mwa iwo anachita chigololo, ndipo anafa tsiku limodzi anthu zikwi makumi awiri ndi zitatu. 9Kapena tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anamuyesa, ndipo anaonongedwa ndi njoka. 10Kapena musamawiringule inu, monga ena mwa iwo anawiringula, ndipo anaonongeka ndi woonongayo. 11Tsopano zonse izi zinachitika kwa iwo monga chitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitilimbikitse, amene matsiriziro a nthawi yino afika kale. 12Chotero kuti amene akuganiza kuti akuyima adziyang’anire kuti angagwe. 13Palibe yesero limene mwakumana nalo komatu lokhalo limene munthu amakumana nalo; ndipo Mulungu2 ndi wokhulupirika, amene sadzalola inu kuti muyesedwe kopyola muyeso wa kupilira kwanu, komatu ndi yesero adzakupatsaninso njira, kuti mukapilire. 14Pamenepo, abale anga, thawani kupembedza mafano. 15Ndikulankhula monga kwa anthu anzeru: kodi inu mukulingalira chimene ndikunena. 16Chikho cha madalitso chimene ife tikudalitsa, kodi sichiyanjano cha mwazi wa Khristu? Mkate umene ife timanyema, kodi sichiyanjano cha thupi la Khristu? 17Chifukwa ife, pokhala ambiri, tili thupi limodzi; pakuti ife tonse tidyako ku mkate umodzi umenewu. 18Onani Israyeli monga mwa thupi: kodi iwo amene amadya zoperekedwa nsembe sayanjana ndi gomelo? 19Kodi pamenepo ndidzalankhula chiyani? Kuti chimene chaperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu, kapena kuti fanolo lili kathu? 20Koma kuti chimene [amitundu] apereka nsembe apereka kwa ziwanda, ndipo osati kwa Mulungu3. Tsopano ine sindifuna kuti muyanjane ndi ziwanda. 21Inu simungamwere chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda: simungayanjane pa gome la Ambuye, ndi pa gome la ziwanda. 22Kodi tikuutsa nsanje ya Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

23Zinthu zonse ziloledwa, koma sizonse zipindulitsa; zinthu zonse ziloledwa, koma sizonse zimangilira. 24Aliyense asafunefune zokomera iye, koma zokomera mzake. 25Chilichonse chogulitsidwa pa msika idyani, musafunse mafunso pa chikumbumtima chanu. 26Pakuti dziko lapansi ndi la Ambuye ndi chidzalo chake. 27Koma ngati wina wa osakhulupilira wakuyitanani, ndipo mwaganiza kupita, zonse zimene zayikidwazo idyani, musafunse mafunso pa chikumbumtima chanu. 28Koma ngati wina anena kwa inu, Ichi chaperekedwa nsembe, musadye, kuchitira iye amene wanena ichi, ndi chikumbumtima; 29komatu chikumbumtima, osati chanu, koma cha winayo: pakuti chifukwa chiyani ufulu wanga uweruzidwa ndi chikumbutima cha munthu wina? 30Pakuti ngati ndilandira ndi chiyamiko, ndilankhuliranji zoipa za chimene ine ndayamika nacho Ambuye? 31Pamenepo kaya mudya, kapena kumwa, kapena kalikonse kamene muchita chitani mwa ulemelero wa Mulungu4. 32Musapereke mpata ku chokhumudwitsa, kaya ndi Myuda, kapena Mherene, kapena mpingo wa Mulungu5. 33Ngakhalenso ine kusangalatsa onse mu zinthu zonse; posafuna phindu la ine mwini, koma la ambiri, kuti akapulumutsidwe.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu