Mutu 9

1Ndipo pamene analowa m’ngalawa, Iye anaoloka ndipo anafika mu mzinda wa kwawo. 2Ndipo taonani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wogonekedwa pa chika; ndipo Yesu, pakuona chikhulupiliro chawo, ananena kwa wamanjenjeyo, limba mtima, mwana; machimo ako akhululukidwa. 3Ndipo taonani, ena mwa alembi ananena kwa iwo okha, [munthu] uyu akuchitira mwano Mulungu. 4Ndipo Yesu, pakuona malingaliro awo, ananena, chifukwa chiyani inu mukuganiza zoipa m’mitima mwanu? 5Pakuti chosavuta ndi chiti: kunena kuti, machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, tauka nuyende? 6Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi ya kukhululukira machimo, (pamenepo analankhula kwa wamanjenjeyo,) tauka, tenga chika lako nupite kunyumba kwako. 7Ndipo anauka napita kunyumba kwake. 8Koma makamu a anthu pakuona [ichi], anagwidwa ndi mantha, ndipo analemekeza Mulungu1 amene anapereka mphamvu yotere kwa anthu.

9Ndipo Yesu, pakudutsa pamenepo, anaona munthu dzina lake Mateyu atakhala polandilira msonkho, ndipo anati kwa iye nditsate Ine. Ndipo ananyamuka namtsata Iye. 10Ndipo inafika nthawi, pamene anali pa gome m’nyumba, kuti taonani, okhometsa misonkho ambiri ndi ochimwa anabwera nakhala pa gome ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11Ndipo Afarisi pakuona [ichi], ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa chiyani mphunzitsi wanu akudya pamodzi ndi amisonkho komanso ochimwa? 12Koma [Yesu] pakumva ichi, ananena, iwo amene ali ndi mphamvu safuna sing’anga, koma iwo amene akudwala. 13Koma pitani ndipo muphunzire [ichi] ndi chiyani — Ine ndifuna chifundo osati nsembe; pakuti sindinabwere kudzaitana [anthu] olungama koma ochimwa.

14Ndipo anabwera kwa Iye ophunzira a Yohane, nanena, chifukwa chiyani ife pamodzi ndi Afarisi timasala kudya pafupipafupi, koma ophunzira anu samasala kudya? 15Ndipo Yesu ananena ndi iwo, kodi ana amuna a mnyumba ya ukwati akhoza kulira nthawi yaitali pamene mkwati ali nawo pafupi? Komatu masiku akubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pamenepo adzasala kudya. 16Komatu palibe munthu amene amaphatika chigamba cha nsalu yatsopano pa chovala chakale, pakuti chigambacho chizomoka ndipo kung’ambika kwakukulu kumachitika. 17Kapena anthu samathira vinyo watsopano m’zikumba zakale, akatero zikumbazo zimaphulika ndipo vinyo amatayika, ndipo zikumba zimaonongeka; komatu amathira vinyo watsopano mu zikumba zatsopanonso, ndipo zonse zimasungika bwino pamodzi.

18Pamene amalankhula izi kwa iwo, taonani, munthu wa ulamuliro analowa namgwadira Iye, nanena, mwana wanga wamkazi wangomwalira kumene; koma tabwerani kuti mukamusanje manja anu ndipo adzakhala ndi moyo. 19Ndipo Yesu anauka namtsatira iye, [chomwechonso] ophunzira ake. 20Ndipo taonani, mzimayi, amene anali ndi nthenda yakukha mwazi [kwa] zaka khumi ndi ziwiri, anafika kumbuyo nakhudza mphonje ya chofunda chake; 21pakuti analankhula mwa iye yekha, ndikangokhudza chofunda chake ndichiritsidwa. 22Koma Yesu pakutembenuka ndi kumuona iye, anati, limba mtima, mwana wanga wamkazi; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe. Ndipo mzimayiyu anachiritsiwa kuchokera ola lomwelo. 23Ndipo Yesu atafika kunyumba kwa munthu wa ulamuliro uja, anaona oimba zitoliro komanso khamu lobuma, 24iye anati, tulukani, pakuti kabuthuka sikanafe, koma kakugona. Ndipo anamuseka Iye mwa chipongwe. 25Koma pamene khamu lija lidatulutsidwa kunja, analowa mkati natenga dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka. 26Ndipo mbiri ya izi inadziwika dela lonse la kumeneko.

27Ndipo pamene Yesu amadutsa kuchokera kumeneko, [amuna] awiri akhungu anamutsatira iye, akufuula ndipo anati, tichitireni chifundo ife, Mwana wa Davide. 28Ndipo pamene Iye anafika kunyumbako, [amuna] akhungu aja anabwera kwa Iye. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Kodi mukukhulupilira kuti Ine ndikhoza kuchita ichi? iwo anati kwa Iye, inde, Ambuye. 29Pamenepo anakhudza maso awo, nanena, Molingana ndi chikhulupiriro chanu, zikhale momwemo kwa inu. 30Ndipo maso awo anatseguka; ndipo Yesu anawauzitsa iwo momveka bwino, nanena, Onetsetsani, kuti munthu wina aliyense asadziwe za ichi. 31Komatu iwo, pamene anatuluka, anabukitsa dzina lake dera lonselo.

32Komatu pamene awa amatuluka, taonani, anabweretsa kwa iye munthu wosalankhula wogwidwa ndi chiwanda. 33Ndipo chiwanda chitatulutsidwa, wosalankhulayo analankhula. Ndipo khamu la anthu linali lodabwa, linati, Zoterezi sizinaonekeko mu Israyeli. 34Koma Afarisi anati, Iye amatulutsa ziwanda kudzera mu mphamvu ya mfumu ya ziwanda.

35Ndipo Yesu anazungulira m’mizinda yawo yonse ndi m’midzi, naphunzitsa m’masunagoge, ndi kulalikira uthenga wabwino wa ufumu, ndipo anachiritsa nthenda iliyonse komanso kufooka kulikonse kwa mthupi.

36Koma pamene anaona khamu la anthu anagwidwa chifundo pa iwo, pakuti anali ozunzika, ndi otaika ngati nkhosa zopanda m’busa. 37Kenako Iye analankhula kwa ophunzira ake, Zokolola [ndi] zambiri koma ogwira ntchito [ali] ochepa; 38chotero pempherani kwa Ambuye mwini zokolola, kuti Iye atumize antchito ku zokolola zake.

1Elohimu