Mutu 3

1Kodi tikuyenera kuyambanso kudzitamandira tokha? Kapena tikuyenera, monga mwa makalata olembedwa kwa inu, kapena [kutamandidwa] kochokera kwa inu? 2Inuyo ndi kalata wathu, wolembedwa m’mitima mwathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse, 3powonetsedwa kukhala kalata ya Khristu yowonetsedwa kwa ife, yolembedwa, osati ndi kapezi, koma Mzimu wa 1Mulungu wamoyo; osati m’magome a miyala, koma magome a mitima ya thupi. 4Ndipo kulimbika mtima tili nako ife mwa Khristu kwa 2Mulungu: 5osati kuti tili nako kuthekera pa ife tokha kuganizira kalikonse monga kathu kokha, komatu kuthekera kwathu ndi kwa 3Mulungu; 6amenenso watipanga ife kukhala othekera, [monga] atumiki a chipangano chatsopano; osati wa kalata, koma wa mzimu. Pakuti chilembo chimapha, koma Mzimu amapereka moyo. 7(Koma ngati utumiki wa imfa, m’makalata, olochedwa m’miyala, kuyamba ndi ulemelero, kotero kuti ana a Israyeli asayang’ane maso awo pa nkhope ya Mose, chifukwa cha ulemelero wa nkhope yake, [ulemelero] umene unali kuchotsedwa; 8koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala mu ulemelero? 9Pakuti ngati utumiki wotsutsidwa ukhala ulemelero, koposa kotani utumiki wa kulungama uchulukira mu ulemelero. 10Pakutinso chimene chinalemekezedwa sichinalemekezedwe m’menemo, pa chifukwa cha ulemelero woposawo. 11Pakuti ngati chimene chikuchotsedwa [chinakhazikitsidwa] ndi ulemelero, koposa kotani chimene chichulukira [chitsalira] mu ulemelero. 12Pamenepo pokhala ndi chiyembekezo chotere, tigwiritsa ntchito kwambiri kulimba mtima: 13ndipo osati molingana ndi Mose poyika nsalu yophimba nkhope yake, kotero kuti ana a Israyeli ayike maso awo pa icho chimene chinachotsedwa. 14Koma malingaliro awo adetsedwa, pakuti kufikira tsiku la lero nsalu yotchinga nkhope ikhalabe yosachotsedwa molingana ndi pangano la kale, limene mwa Khristu lachotsedwa. 15Koma kufikira tsiku la lero, pamene wawerengedwa Mose, chotchinga nkhope chikhala pa mitima yawo. 16Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, nsalu yophimba nkhope ichotsedwa.) 17Tsopano Ambuye ndi Mzimu, koma pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu. 18Koma ife tonse, tiyang’anira pa ulemelero wa Ambuye, ndi nkhope yovundukula, tisandulika molingana ndi chithunzithunzi chomwecho kuchoka ku ulemelero kupita ku ulemelero, monga ngati mwa Ambuye, Mzimunso.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu