Mutu 13

1Tsopano panali mu Antiokeya, mu mpingo umene unali [kumeneko], aneneri ndi aphunzitsi: Barnaba, ndi Simeoni amene anatchedwanso m’Niguro, ndi Lukiya waku Kurene, ndi Manayeni, m’chimwene wake wa Herode chiwangacho woleledwa m’nyumba imodzi, ndi Saulo. 2Ndipo pamene iwo amatumikira Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, Undipatulire ine tsopano Barnaba ndi Saulo pa ntchito imene ndinawayitanira iwo. 3Pamenepo, atatsala kudya ndi kupemphera, ndipo anawasanjika manja iwo, nawalola kuti apite. 4Pamenepo iwo, anatumizidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya, ndipo pamenepo anakwera ngalawa napita ku Kupro. 5Ndipo pokhala mu Salami, iwo analalikira mau a Mulungu1 m’sunagoge wa Ayuda. Ndipo iwo analinso ndi Yohane monga owathandizira [wao]. 6Ndipo atadutsa pa chilumba chonse kufikira ku Pafo, anapeza munthu wina wa matsenga, mneneri wachinyengo, Myuda, amene dzina lake linali Bara-yesu, 7amene anali ndi kazembe Sergio Paulo, munthu wanzeru. Iye, pamene anayitana Barnaba ndi Saulo, anafunitsitsa kumva mau a Mulungu2. 8Komanso Elima wamatsengayo (pakuti tanthauzo la dzina lake ndi limeneli) anatsutsana nawo iwo, nayesa kubweza kazembeyo ku chikhulupiliro. 9Koma Saulo, amenenso anali Paulo, wodzala ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye, 10nanena, Wodzala ndi chinyengo chonse komanso kuchenjera konse: mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo; kodi sudzasiya kuononga njira zoongoka za Ambuye? 11Ndipo tsopano taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu, sudzaona dzuwa kwa nthawi. Ndipo nthawi yomweyo linamugwera khungu ndi mdima; ndipo pamene anatuluka kunja anafuna munthu womutsogolera padzanja. 12Pamenepo kazembeyo, poona chochitikacho, anakhulupilira, nazizwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.

13Ndipo atayenda pa ngalawa kuchokera ku Pafo, Paulo ndi amzake anafika ku Perge, waku Pemfaliya; ndipo Yohane analekana nawo nabwerera ku Yerusalemu. 14Koma iwo, pakudutsa kuchokera ku Perge, anafika ku Antiokeya wa m’Pisidiya; ndipo polowa m’sunagoge patsiku la sabata anakhala pansi. 15Ndipo atamaliza kuwerenga za m’chilamulo ndi aneneri, olamulira a sunagoge anawayitanitsa iwo, nati, Abale, ngati tili ndi mau a chilimbikitso kwa anthuwa, tiyeni tilankhule. 16Ndipo Paulo, anauka napereka chizindikiro ndi dzanja lake, nati, A Israyeli inu, ndi inu akuopa Mulungu3, tamverani. 17? Mulungu4 wa anthu awa a Israyeli anasankha makolo athu, ndipo anawakweza anthuwa pa ulendo wawo m’dziko la Aigupto, ndi dzanja lake la mphamvu anawatulutsa m’dzikolo, 18ndipo kwa nthawi yokwanira pafupifupi zaka makumi anayi anawasamalira m’chipululu. 19Ndipo m’mene anawononga mitundu isanu ndi iwiri m’dziko la Kenani, Iye anawapatsa iwo dziko lawo monga cholowa. 20Ndipo zitapita zinthu izi anawapatsa [iwo] oweruza kufikira Samueli mneneriyo, [kufikira kumapeto a] pafupifupi zaka mazana anayi kufikira makumi asanu. 21Ndipo pamenepo iwo anafunsa mfumu, ndipo Mulungu5 anawapatsa iwo Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, kwa zaka makumi anayi. 22Ndipo atamuchotsa iye anawaukitsira iwo Davide kukhala mfumu, amenenso poperekera umboni anati, Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa kumtima kwanga, amene adzachita chifuniro changa chonse. 23Mu mbeu ya munthu ameneyu molingana mwa lonjezano Mulungu6 anabweretsa kwa Israyeli, Yesu; 24Yohane atalalikiratu za kulowa kwake [pakati pa anthu] ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israyeli. 25Ndipo monga Yohane atakwaniritsa cholinga chake anati, Kodi mukuganiza kuti ndine ndani? Sindine [Iyeyo]. Koma taonani, akubwera wina pambuyo panga, amene nkhwayira zake sindili woyenera kumasula. 26Abale inu, ana a mtundu wa Abrahamu, ndi iwo amene pakati panu amaopa Mulungu7, kwa inu mau a chipulumutso ichi atumizidwa: 27kwa iwo amene akhala mu Yerusalemu, ndi olamulira awo, sanamdziwe Iye, anakwaniritsa mau a aneneri amene amawerengedwa la sabata lililonse, [pa] kumuweruza [Iye]. 28Ndipo pamene sanapeze [mwa Iye] chifukwa chomuphera, anamupempha Pilato kuti Iye aphedwe. 29Ndipo pamene iwo anakwaniritsa zinthu zonse zolembedwa zokhudza Iye, anamutsitsa pa mtanda ndi kumuika m’manda osema; 30koma Mulungu8 anamuukitsa kuchoka pakati pa akufa, 31amene anaonekera kwa masiku ambiri kwa iwo amene anabwera naye kuchoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu, amene tsopano ndi mboni zake kwa anthu. 32Ndipo ife tilalikira uthenga wabwino wa lonjezano loperekedwa kwa makolo athu, 33kuti Mulungu9 wakwaniritsa ili kwa ife ana awo, pamene anamuukitsa Yesu; monganso kunalembedwa m’Masalmo wachiwiri, Ndiwe Mwana wanga: lero ndakubala iwe. 34Koma kuti anamuukitsa Iye pakati pa akufa, palibenso kubwerera ku chivundi, Iye analankhula chonchi: Ine ndidzakupatsani chifundo chokhulupirika cha Davide. 35Pamenepo iye anatinso m’Masalmo ena, Simudzapereka wa chisomo chanu kukaona chivundi. 36Pakutidi Davide, mu m’badwo wake anatumikira ku chifuniro cha Mulungu10, anagona tulo, ndipo anayikidwa kwa makolo ake ndipo anaona chivundi. 37Koma Iye amene Mulungu11 anamuukitsa sanaone konse chivundi. 38Zidziwike kwa inu, pamenepo, abale, kuti kudzera mwa munthu Uyu chikhululukiro cha machimo chilalikidwa kwa inu, 39ndipo kuchokera ku zinthu zonse zimene inu simungalungamitsidwe nazo mu lamulo la Mose, mwa Uyu aliyense wokhulupilira alungamitsidwa. 40Onetsetsani pamenepo kuti chimene chinalankhulidwa mwa aneneri sichikufikira pa [inu], 41Taonani, opeputsa inu, ndipo dabwani ndi kuonongeka; pakuti ine ndikugwira ntchito m’masiku anu, ntchito imene inu simungakhulupilire ngati munthu adzakuuzani inu. 42Ndipo pamene iwo anatuluka kunja anapempha kuti mau awa alankhulidwe kwa iwo sabata likudzalo. 43Ndipo osonkhana m’sunagoge atabalalika, Ayuda ambiri ndi opinduka opembedza anamtsatira Paulo ndi Barnaba, amene polankhula kwa iwo, anawaumiriza kupitiriza mu chisomo cha Mulungu12. 44Ndipo pa sabata lobweralo pafupifupi mzinda wonse unasonkhana pamodzi kudzamva mau a Mulungu13. 45Koma Ayuda poona makamuwo, anazadzidwa ndi nsanje, natsutsana ndi zinthu zonenedwa ndi Paulo, [kutsutsana ndi] kulankhula mwa chipongwe. 46Ndipo Paulo ndi Barnaba analankhula molimba mtima ndi kuti, Kunali koyenera kuti mau a Mulungu14 alankhulidwe koyamba kwa inu; koma, pakuti mukuwakana, ndi kudziweruza nokha osayenera ku moyo wosatha, Taonani, ife tatembenukira kwa amitundu; 47pakuti pamenepo Ambuye anatilamulira ife: Ndakuikani inu mukhale kuwala kwa amitundu, kuti mudzakhala chipulumutso kumalekezero a dziko lapansi. 48Ndipo [iwo a] amitundu, pakumva awa, anakondwera, ndipo analemekeza mau a Ambuye, nakhulupilira, monga ochuluka anazozedwa ku moyo wosatha. 49Ndipo mau a Ambuye anatengedwa kudziko lonse. 50Koma Ayuda anamemeza akazi amene anali ochita bwino amene anali opembedza, ndi mzika zotchuka za mu mzindawo, ndipo anaukitsa chizunzo pa Paulo ndi Barnaba, ndipo anawathamangitsa m’malire awo. 51Koma iwo, atasatsa fumbi la ku mapazi kwao motsutsana nawo, anafika ku Ikoniyo. 52Ndipo ophunzira adzadza ndi chimwemwe komanso Mzimu Woyera.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu