Mutu 13

1Tsopano nthawi yomweyo analipo ena amene anamufotokozera Iye za Agalileya amene mwazi wao unasakanizidwa ndi mwazi wa nsembe. 2Ndipo poyankha Iye anati kwa iwo, Kodi mukuganiza kuti Agalileyawa anali ochimwitsitsa kuposa Agalileya ena onse kuti anamva zowawa zotere? 3Ayi ndithu, Ine ndinena kwa inu, ngati simulapa, mudzaonongeka chomwechi. 4Kapena iwo khumi asanu ndi atatu aja amene nsanja ya Siloamu inawagwera ndi kuwapha iwo, kodi mukuganiza kuti iwo anali ochimwitsitsa kuposa anthu onse okhala mu Yerusalemu? 5Ayi ndithu, Ine ndinena kwa inu, ngati inu simulapa, nonse mudzaonongekanso chomwechi.

6Ndipo Iye analankhula fanizo ili: [munthu] wina anali ndi mtengo wa mkuyu wodzalidwa m’munda mwake, ndipo iye anabwera kudzafuna chipatso pa mtengowo ndipo sanapeze chipatso chilichonse. 7Ndipo anati kwa woyang’anira mundawo, Taona, zaka zitatu [izi] ndabwera kudzafuna chipatso pa mtengo wa mkuyu uwu koma sindinachipezepo: uduleni; chifukwa chiyani ukupangitsa nthaka kukhala yopanda ntchito? 8Koma poyankha anati kwa iye, Mbuye, baulekani kaye kwa chaka chino chokha, kufikira ndikaukumbira kwete ndi kuikapo ndowe, 9ndipo ngati ukabereka chipatso — koma ngati ayi, pamenepo mukaudule.

10Ndipo Iye amaphunzitsa mu imodzi ya masunagoge pa sabata. 11Ndipo taonani, [panali] mkazi wakukhala nawo mzimu wa kumdwalitsa kwa zaka khumi zisanu ndi zitatu, ndipo anakhala mopindika msana ndipo kwathunthu sanathe kuweramuka ndi kudzutsa mutu wake. 12Ndipo Yesu, pomuona iye, anamuitana, nati kwa iye, Mkazi iwe, wamasulidwa ku chivutiko chako. 13Ndipo anayika manja ake pa iye; ndipo nthawi yomweyo anawongoka, nalemekeza Mulungu1. 14Koma mkulu wa sunagoge, anavutika mtima chifukwa Yesu anachiritsa pa sabata, poyankhapo iye anati ku khamulo, Pali masiku asanu ndi limodzi amene [anthu] akuyenera kugwira ntchito; mwa amenewa mukhoza kubwera ndi kuchiritsidwa, ndipo osati tsiku la sabata. 15Ambuye pomwepo anamuyankha iye nanena, Onyenga inu! Kodi aliyense mwa inu pa sabata samasula ng’ombe kapena bulu wake mkhola mwake ndi kuyilondolera [iyo] kukamwa madzi? 16Ndipo [mkazi] uyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, amene Satana anamumanga, taonani, zaka [izi] khumi zisanu ndi zitatu, kodi sakuyenera kumasulidwa ku goli limeneli tsiku la sabata? 17Ndipo pamene amalankhula zinthu izi, onse amene anatsutsana naye anachita manyazi; ndipo anthu onse anakondwera ndi zinthu zonse zimene zinachitidwa ndi Iye.

18Ndipo Iye anati, Kodi ufumu wa Mulungu2 uli ngati chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? 19Uli ngati [mbewu] ya mpiru imene munthu waitenga naiponya m’munda mwake; ndipo inakula nikhala mtengo waukulu, ndipo mbalame zakumwamba zigonera mu nthambi zake.

20Ndiponso anati, Kodi ufumu wa Kumwamba3 ndidzaufanizira ndi chiyani? 21Uli ngati chotupitsa mkate, chimene mkazi anachitenga nachibisa mu milingo itatu ya chakudya kufikira chonse chitupitsidwa.

22Ndipo Iye anapyola mzinda umodzi ndi mudzi pa mudzi wina, naphunzitsa, ndipo anayenda kupita ku Yerusalemu. 23Ndipo m’modzi anati kwa Iye, Mbuye, kodi ndi ochepa amene adzapulumutsidwa? Koma Iye anati kwa iwo, 24Yetsetsani motsimikiza kulowa pa chipata chopapatiza, pakuti ambiri, ndinena kwa inu, adzafunitsitsa kulowa ndipo sadzakwanitsa. 25Kuchokera nthawi imene mbuye wa nyumba adzauka ndipo adzatseka chitseko, ndipo mudzayamba kuima kunja ndi kugogoda pakhomo, munena, Ambuye, titsegulireni ife; ndipo Iye poyankha adzati kwa inu, sindikudziwani inu kumene mukuchokera: 26pamene mudzayamba inu kulankhula, Ife takhala tikudya ndi kumwa pamaso panu, ndipo Inu mwakhala mukuphunzitsa m’makwalala mwathu; 27ndipo Iye adzati, Ndikuuzani, sindikudziwani inu kumene mukuchokera; chokani kwa Ine, [inu] nonse ochita zoipa. 28Kudzakhala kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse mu ufumu wa Mulungu4, koma inuyo mutaponyedwa kunja. 29Ndipo adzabwera iwo kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kum’mwera, ndipo adzakhala pa gome mu ufumu wa Mulungu5. 30Ndipo taonani, alipo amene ali akumapeto adzakhala oyambilira, ndi oyambilira adzakhala akumapeto.

31Mu ola lomwelo Afarisi ena anabwera, nanena kwa Iye, Tulukani, ndipo chokani kuno, pakuti Herode akufuna kukuphani inu. 32Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani, kayiuzeni nkhandweyo, Taonani, Ine ndikutulutsa ziwanda ndipo ndimalizitsa kuchiritsa matenda lero ndi mawa, ndipo [tsiku] lachitatu nditsirizitsa; 33koma ndiyenera ndiyende lero ndi mawa ndi [tsiku] lotsatiralo, pakuti sikuyenera kuti mneneri awonongeke kunja kwa Yerusalemu. 34Yerusalemu, Yerusalemu, [mzinda] umene umapha aneneri ndi miyala iwo amene atumizidwa kwa iye, ndinasonkhanitsa pamodzi kawirikawiri ana ako, monga thazi ndi anapiye m’mapiko ake, ndipo iwe sunafune ayi. 35Taona, nyumba yako yasiyidwa kwa iwe; ndipo ndinena kwa iwe, kuti suzandiona Ine kufikira muzati, Wodala [ali] iye wakudza m’dzina la Ambuye.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu