Mutu 20

1Pakuti ufumu wakumwamba uli ngati mwini nyumba amene analawirira m’mamawa kukafuna antchito olima m’munda wake wa mpesa. 2Ndipo atagwirizana ndi antchitowo pa lupiya latheka limodzi patsiku, iye anawatumiza m’munda wake wa mpesa. 3Ndipo atatuluka pafupifupi [pa] ola lachitatu, iye anaona anthu ena atayima pamalo a msika ali osowa chochita; 4ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso m’munda wa mpesa, ndipo chilichonse chimene chili chilungamo ndidzakupatsani ine. Ndipo iwo anapita njira yawo. 5Kenakonso, patapita ngati ola lachisanu ndi chimodzi komanso ola lachisanu ndi chinayi, iye anachita chimodzimodzi. 6Koma pa [ola] la khumi ndi chimodzi, atatuluka kunja, iye anapezanso ena atangoyima, ndipo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mwangoima pano tsiku lonse popanda chochita? 7Iwo anati kwa iye, Chifukwa palibe munthu amene watilemba ntchito ife. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso m’munda wa mpesa [ndipo chilichonse chimene chili chilungamo mudzalandira]. 8Koma madzulo atafika, mbuye wa munda wampesa ananena kwa akapitawo ake, Aitaneni antchito aja ndipo muwapatse [iwo] malipiro awo, kuyambira wotsirizira kukamalizira woyambilira. 9Ndipo pamene iwo [amene anabwera ku ntchito] pafupifupi ola la khumi ndi chimodzi, analandira aliyense rupiya la theka limodzi. 10Ndipo atabwera woyambilira aja, iwo amayembekezera kuti alandira zochuluka, ndipo iwonso analandira aliyense rupiya la theka limodzi. 11Ndipo pakulandira iwo anang’ung’uza motsutsana ndi mwini nyumba uja, 12nanena, Awa otsirizawa agwira ntchito ola limodzi, ndipo mwawapatsa molingana ndi ife, amene tagwira ntchito yolemetsa ya tsiku lonse ndi kutentha. 13Koma iye pakuyankha anati kwa m’modzi wa iwo, Mzanga, Ine sindinakulakwire iwe. Kodi sunagwirizane ndi ine kuti ndikupatse rupiya latheka limodzi? 14Tenga chimene chili chako ndipo udzipita. Komatu ndi chifuniro changa kupereka kwa womalizayu chimodzimodzi ndi iwe: 15kodi sikololedwa kuchita chimene ndifuna pa zinthu zanga? Kodi diso lako laipa chifukwa ndine wabwino? 16Chomwecho wotsiriza adzakhala woyamba, ndipo woyamba adzakhala wotsiriza; pakuti ambiri ndi oitanidwa, koma ochepa ndi osankhika.

17Ndipo Yesu, pakukwera kupita ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri pamodzi ndi [iye] napita nawo paokha panjira, ndipo anati kwa iwo, 18Taonani ife tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi, ndipo adzamuweruza iye ku imfa; 19ndipo iwo adzampereka iye kwa amitundu kuti amnyoze ndi kumkwapula ndi kumpachika, ndipo tsiku lachitatu adzaukanso.

20Kenako anabwera kwa iye amayi a ana a Zebedayo, pamodzi ndi ana ake amuna, namgwadira, ndipo anapempha kanthu kwa iye. 21Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi ndikuchitire chiyani? Iye anati kwa Yesu, Lankhulani [mau] kuti ana anga amuna awa adzakhale, wina kudzanja lamanja ndipo wina kudzanja lamanzere mu ufumu wanu. 22Ndipo Yesu pakuyankha anati, Iwe sudziwa chimene ukupempha. Kodi ukhoza kumwera chikho chimene Ine ndikufuna kumwerako? Iwo anati kwa Iye, Ifetu tikhoza kumwera. 23[Ndipo] Iye anati kwa iwo, Inutu zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kukhala kudzanja langa lamanja komanso dzanja [langa] lamanzere, sikuli kwa Ine kupereka, komatu kwa iwo amene chakonzedwa ndi Atate wanga. 24Ndipo khumiwo, pakumva [za ichi], anakwiya nawo abale awiriwo. 25Koma Yesu pakuwaitana iwo kwa [Iye], anati, Inu mudziwa kuti olamulira mafuko amadzipanga umbuye pa iwo, komanso amapanga ulamuliro waukulu pa iwo. 26Sizidzakhala chomwechi pakati pa inu, komatu amene adzakhala wamkulu pakati panu, akhale mtumiki; 27ndipo aliyense amene adzakhala woyamba pakati panu, ameneyo akhale kapolo; 28monga zoonadi Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndiponso kudzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

29Ndipo pamene anatuluka mu Yeriko makamu a anthu anamutsatira Iye. 30Ndipo taonani, anthu awiri akhungu, akukhala mphepete mwanjira, pakumva kuti Yesu akudutsa, anafuula nati, Tichitireni chifundo ife, Ambuye, Mwana wa Davide. 31Koma khamulo linawadzudzula iwo, kuti akhale chete. Koma iwo anafuulirabe kwambiri, nanena, Tichitireni chifundo ife, Ambuye, Mwana wa Davide. 32Ndipo Yesu, pakuima, anawaitana iwo ndipo anati, Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani? 33Iwo anati kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu atsegukenso. 34Ndipo Yesu, pakugwidwa ndi chifundo, anakhudza maso awo; ndipo nthawi yomweyo maso awo anapenyanso, ndipo iwo anamtsatira Iye.