Mutu 14
1Ndipo kunachitika, pamene analowa m’nyumba ya m’modzi wa akulu, [amenenso anali] mkulu wa Afarisi, kukadya mkate pa sabata, kuti iwo anali kumuona Iye. 2Ndipo taonani, panali [munthu] wokha dovu patsogolo pake. 3Ndipo Yesu poyankha analankhula kwa akadaulo achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi ndi kololedwa kuchiritsa patsiku la sabata? 4Koma iwo anakhala chete. Ndipo Iye anamutenga wodwalayo namchiritsa ndipo anamulola kuti apite. 5Ndipo poyankha Iye anati kwa iwo, Ndani wa inu pamene bulu kapena ng’ombe yake yagwera m’chitsime, kuti nthawi yomweyo sayitulutsa patsiku la sabata? 6Ndipo iwo sanakwanitse kumuyankha Iye zinthu izi.
7Ndipo Iye analankhula fanizo kwa iwo amene anaitanidwa, poona momwe iwo amasankhira mipando ya ulemu, nanena nawo, 8Pamene waitanidwa ndi aliyense ku ukwati, usazikhazike wekha pa gome la ulemu, kuti kapena wina wa ulemu kuposa iwe akaitanidwa ndi iye, 9ndipo iye wakuitana iwe ndi uyu adzabwera kwa iwe nati, Pereka malo kwa [munthu] uyu, ndipo kuti udzachita manyazi kukakhala malo a pansi. 10Koma pamene iwe waitanidwa, pita ndipo kazikhazike wekha malo a pansi, kuti pamene iye wakuitana iwe abwera, adzanene kwa iwe, Bwenzi langa, pita pamalo a ulemu: pamenepo udzakhala wolemekezeka pamaso pa onse amene akhala pa gome ndi iwe; 11pakuti aliyense amene amadzikweza yekha adzatsitsidwa, ndipo wodzitsitsa yekha adzakwezedwa.
12Ndipo Yesu analankhulanso kwa kwa iye amene anamuitana, Pamene iwe ukonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usayitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anasi ako olemera, kuti mwina iwonso adzakuitane iwe pobwezera pake, kuti chobwezera chikachitike kwa iwe. 13Koma pamene ukonza phwando, uyitane osauka, opunduka, otsimphina, akhungu: 14ndipo iwe udzadalitsika; pakuti iwo alibe [njira] yobwezera iwe; pakuti chidzabwezedwa kwa iwe pa chiukitso cha olungama.
15Ndipo m’modzi wa iwo wokhala ndi [iwo] pa gome, pakumva zinthu izi, anati kwa Iye, Wodala [iye] amene adzadya mkate mu ufumu wa Mulungu1. 16Ndipo Yesu anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikulu ndipo anaitana anthu ambiri. 17Ndipo iye anatumiza kapolo wake kukanena kwa iwo anayitanidwawo, Bwerani, pakuti zinthu zonse zakonzedwa. 18Ndipo onse posasiyapo ndi m’modzi yemwe, anayamba kupepesa. Woyamba anati kwa iye, Ndagula malo, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawaone; ndikupempha kuti ulandire kupepesa kwanga. 19Ndipo wina anati, Ndagula ng’ombe zisanu zokoka ngolo, ndipo ndikuyenera kupita kukaziyendera; ndikupempha kuti ulandire kupepesa kwanga. 20Ndipo wina anati, Ndakwatira kumene mkazi, ndipo pachifukwa chimenechi sindingathe kubwera. 21Ndipo kapolo uja anabwera napereka mau onse aja kwa mbuye wake. Pomwepo mwini nyumba, mopsa mtima, anati kwa kapolo wake, Pita mwachangu m’makwalala ndi m’misewu ya mu mzinda, ndipo ubweretse kuno osauka, ndi olumala ndi otsimphina ndi akhungu. 22Ndipo kapoloyo anati, Mbuye, ndachita monga mwanenera, ndipo malo adakalipobe. 23Ndipo mbuye anati kwa kapoloyo, Upite mphambano ndi m’mipanda ndipo uwakakamize iwo kubwera, kuti nyumba yanga ikadzaze; 24pakuti Ine ndinena kwa iwe, palibe mwa anthu anayitanidwa aja amene adzalawa chakudya changa.
25Ndipo makamu ambiri a anthu anapita naye; ndipo, pocheuka anati kwa iwo, 26Ngati munthu adza kwa Ine, ndipo sakuda atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana ake, ndi abale ake, ndi alongo ake, inde, ndi moyo wakenso, iyeyu sangathe kukhala wophunzira wanga; 27ndipo amene sangathe kusenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangathe kukhala wophunzira wanga. 28Pakuti ndani mwa inu, amene amafuna kumanga nsanja yaitali, sakhala kaye pansi ndi kuwerengera mtengo wake, ngati ali nazo [zofunikira] kumalidzitsa ntchitoyo; 29kupangira kuti, amayika maziko pa ntchitoyo ndi kulephera kumalidzitsa, kuti onse owonerera ichi angayambe kumuseka iye, 30nanena, Munthu uyu anayamba kumanga ndipo sanakwanitse kutsirizitsa? 31Kapena ndi mfumu yotani, pamene ipita kukamenyana nkhondo ndi mfumu ina, sikhala kaye pansi poyamba, natenga upangiri ngati angapambane ndi asilikali zikwi khumi kulimbana ndi uyu amene ali ndi asilikali zikwi makumi awiri? 32ndipo ngati satero, pamene ali kutali, atumiza nthumwi, napempha mgwirizano wa mtendere. 33Chomwechonso aliyense wa inu amene sakana zonse zimene ali nazo sangathe kukhala wophunzira wanga. 34Mchere [pamenepo] [ndi] wabwino, koma ngati mchere usukuluka, kodi udzakoleletsedwa ndi chiyani? 35Sukhalanso woyenera mu nthaka kapena mu ndowe; umatayidwa kunja. Iye amene ali nawo makutu akumva, amve.
1Elohimu