Mutu 7
1Musaweruze, kuti inunso mungaweruzidwe; 2pakuti ndi mlingo wa chiweruzo umene mumapereka, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi; ndipo ndi muyeso umene muyesera, muyeso womwewo udzayesedwa kwa inu. 3Koma chifukwa chiyani uyang’ana kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako, koma osasamala chipika chimene chili m’diso lako? 4Kapena mudzanena bwanji kwa m’bale wanu, ndilole [ine], ndidzachotse kachitsotso m’diso lako; ndipo pamenepo, chipika chidakali m’diso lako? 5Wonyenga iwe, uyambe wachotsa chipika m’diso lako, ndipo kenako udzaona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali m’diso la m’bale wako.
6Musamapereke chimene chili choyera kwa agalu, kapena kuponya ngale zanu kwa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi awo, ndi kutembenukira kwa inu ndi kukupwetekani.
7Pemphani ndipo chidzapatsidwa kwa inu. Funani, ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu. 8Pakuti aliyense amene amapempha amalandira ; ndipo iye amene amafuna amapeza; ndipo kwa iye amene amagogoda chidzatsegulidwa. 9Kapena ndani mwa inu, ngati mwana wake adzampempha mkate, adzampatsa iye mwala; 10ndipo akampempha nsomba, adzampatsa iye njoka? 11Chotero ngati inu, okhala oipa, mumadziwa [m’mene] mumaperekera mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate wanu amene ali kumwamba adzapereka zinthu zabwino kwa iwo amene amupempha iye? 12Chomwecho zinthu zonse zimene mufuna kuti anthu akuchitireni inu, koteronso inu kawachitireni chimodzimodzi; pakuti limeneli ndi lamulo ndi aneneri.
13Lowani pa chipata chopapatiza, pakuti chipata chili chachikulu komanso njira yopita kuchionongeko ili yotakata, ndipo alipo ambiri amene amalowa pa chipatachi. 14Pakuti chipata chili chopapatiza ndipo njira yake ili yaing’ono yopita ku moyo, ndipo ali ochepa amene amaipeza njirayi.
15Komatu muchenjere ndi aneneri onyenga, amene amabwera kwa inu ndi zovala za nkhosa, koma mkati mwao ali mimbulu yolusa. 16Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi [amuna] samasonkhanitsa ma phava a mpesa kuchoka pa minga, kapena kuchoka pa mthula? 17Chotero mtengo uliwonse wabwino umabereka zipatso zabwino, koma mtengo woipa umaberekanso zipatso zoipa. 18Mtengo wabwino sungabereke zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubereka zipatso zabwino. 19Mtengo ulionse wosabereka zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto. 20Ndipotu ndi zipatso zawo muzawadziwa ndithu.
21Siyense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wa kumwamba, koma iye wakuchita chifuniro cha Atate wanga amene ali kumwamba. 22Ambiri adzanena kwa ine tsiku limenelo, sitinanenere kodi mu dzina lanu, kapena mu dzina lanu kutulutsa ziwanda, kapenanso mu dzina lanu kuchita ntchito zambiri za mphamvu? 23ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu. Chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
24Iye amene adzamva mau anga ndi kuwachita, ndidzamufanizira ndi munthu wochenjera, amene amanga nyumba yake pa thanthwe; 25ndipo mvula inagwa, nidzala mitsinje, ndipo mphepo inaomba ndi kugunda panyumbapo, ndipo nyumbayo siinagwe, pakuti inamangidwa pa thanthwe. 26Ndipo aliyense amene amva mau anga ndi kusawachita, ndidzamufanizira ndi munthu wopusa, amene amanga nyumba yake pa mchenga; 27ndipo mvula inagwa, nidzala mitsinje, ndipo mphepo inaomba ndi kugunda panyumbapo, ndipo nyumbayo inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.
28Ndipo kunachitika kuti Yesu atamaliza kulankhula mau awa, makamu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29pakuti anaphunzitsa monga wokhala nawo ulamuliro, osati ngati alembi awo.