Mutu 21
1Zitapita zinthu izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiya. Ndipo Iye anadzionetsera [yekha] motere. 2Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi wotchedwa Didimo, ndi Natanayeli amene anali wa ku Kana wa Galileya, ndi [ana] a Zebedayo, ndi ena awiri a ophunzira ake. 3Simoni Petro anati kwa iwo, Ndikupita kukasodza. Iwo anati kwa iye, Ifenso tipita nawe. Iwo anapita, nakwera m’ngalawa, ndipo usiku umenewo sanagwire kanthu. 4Ndipo m’mamawa kwambiri poyamba kucha, Yesu anayimilira pambali pa nyanja; komabe ophunzira sanam’dziwe kuti anali Yesu. 5Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Ananu, muli nako kanthu kakudya? Iwo anamuyankha Iye, Ayi. 8Ndipo Iye anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya manja ya ngalawa ndipo mudzapeza. Pamenepo iwo anaponya, ndipo sanakwanitse kulikoka, ku khamu la nsombazo. 7Pamenepo wophunzira amene Yesu anamukonda anati kwa Petro, Ndi Ambuye Uyu. Pamenepo Simoni Petro, pakumva kuti ndi Ambuye, anavala zovala zake (pakuti anali wa maliseche), ndipo anaziponya yekha m’nyanja; 8ndipo ophunzira enawo anabwera m’ngalawa yaing’ono, pakuti sanatalikirane ndi kumtunda, koma malo ena pafupifupi mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo. 9Pamene iwo anatuluka pa mtunda, anaona moto wa makala pamenepo, ndi nsomba inayikidwa pamenepo, ndi mkate. 10Yesu anati kwa iwo, Bweretsani tsopano nsomba zimene mwatenga. 11Simoni Petro anakokera khoka ku mtunda lodzadza ndi nsomba zikuluzikulu, zana limodzi ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo ngakhale kuti nsombazi zinali zochuluka kwambiri, koma khoka silinang’ambike. 12Yesu anati kwa iwo, Bwerani [ndipo] tidzadye. Koma palibe wa ophunzira ake anatha kumufunsa, Ndinu ndani? Podziwa kuti anali Ambuye. 13Yesu anabwera ndipo anatenga mkate nawapatsa iwo, ndi nsomba chimodzimodzinso. 14Kameneka kanali kachitatu kuti Yesu adzionetsere kwa ophunzira ake, ataukitsidwa pakati pa akufa.
15Pamene iwo anadya, Yesu anati kwa Simoni Petro, Simoni, [mwana] wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Anati kwa Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ine ndinadziphatika kwa Inu. Anati kwa iye, Dyetsa nkhosa zanga. 16Anatinso kachiwiri kwa iye, Simoni, [mwana] wa Yona, undikonda Ine? Anati kwa Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ine ndinadziphatika kwa Inu. Anati kwa iye, Weta nkhosa zanga. 17Anati kwa iye kachitatu, Simoni [mwana] wa Yona, kodi iwe unadziphatika kwa Ine? Petro anamva chisoni kuti ananena kwa iye kachitatu, Kodi unadziphatika kwa Ine? Ndipo anati kwa Iye, Ambuye, mukudziwa zinthu zonse; Inu mukudziwa kuti ndinadziphatika kwa inu. Yesu anati kwa iye, Dyetsa nkhosa zanga. 18Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa iwe, Pamene unali mnyamata, unadzimangira wekha m’chiuno, ndipo unayenda kulikonse kumene unafuna; koma pamene udzakalamba, udzatambasula dzanja lako, ndipo wina adzakumangira m’chiuno, ndi kukutengera kumene iwe sufunako. 19komatu Iye ananena izi kuzindiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu1. Ndipo atanena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine. 20Petro, potembenuka, anaona wophunzira amene Yesu anamukonda akutsatira, amenenso anatsamira pachifuwa chake pa mgonero, ndipo amene anati, Ambuye, ndani amene adzapereka Inu? 21Petro, pomuona iye, anati kwa Yesu, Ambuye, nanga [za] [munthu] uyu? 22Yesu anati kwa iye, Ngati Ine ndifuna kuti akhalebe kufikira ndikabwera, chimenechi [ndi chiyani] kwa iwe? Iweyo unditsate Ine. 23Pamenepo mau awa anapita pakati pa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Ndipotu Yesu sananene kwa iye, kuti sadzafa; koma kuti, Ngati Ine ndifuna kuti akhalebe kufikira ndikabwera, chimenechi [ndi chiyani] kwa iwe?
24Uyu ndi wophunzira amene anachitira umboni wokhudza zinthu izi, ndipo iye amene walemba zinthu zimenezi; ndipo ife tidziwa kuti umboni wake ndi oona. 25Ndipo ziliponso zinthu zina zambiri zimene Yesu anazichita, kuti zikanalembedwa chimodzichimodzi, ine ndiganiza kuti ngakhale dziko lapansi silikanakwanitsa kusunga mabuku olembedwawo.
1Elohimu