Mutu-2

1Tsopano tikupemphani inu, abale, pakubwera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana kwathu pamodzi kwa iye, 2kuti musakhale ogwedezeka msanga m’malingaliro, kapena kusautsika, kaya ndi mwa mzimu, kapena mwa mau, kapena mwa chilembo, ngati kuti zinali mwa ife, kuti tsiku la Ambuye lafika. 3Musalole aliyense akunamizeni inu mwanjira ina iliyonse, chifukwa sizizachitika pokhapokha mpatuko utafika, ndipo munthu wochimwa atavumbulutsidwa, mwana wa chiwonongeko; 4amene atsutsana nazo ndi kuzikweza mwini yekha pamwamba pa zonse zotchedwa Mulungu1, kapena chida cha ulemu; cholinga kuti iye mwini akakhale pansi m’kachisi wa Mulungu2, kudzionetsera yekha kuti iye ali Mulungu3. 5Kodi simukumbukira chimenechi, pamene ndinali nanu, ndinalankhula zinthu zimenezi kwa inu? 6Ndipo tsopano inu mukudziwa chimene chimaletsa, kuti iye akavumbulutsidwe mu nyengo ya iye yekha. 7Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayamba kale kugwira ntchito; chokhachi alipo iye amletsa tsopano kufikira atachoka iye, 8ndipo pamenepo wosaweruzikayo adzavumbulutsidwa, amene Ambuye Yesu adzamuwononga koopsa ndi mpweya wa mkamwa mwake, nadzamuthetsa ndi maonekedwe a kubwera kwake; 9amene kubwera kwake ndi kolingana mwa machitidwe a Satana mu mphamvu zonse ndi zisonyezo ndi zozizwa zonyenga, 10ndi m’chinyengo chonse chosalungama kwa iwo amene akuonongeka, chifukwa sanalandire chikondi cha choonadi kuti apulumutsidwe. 11Ndipo pachifukwa chimenechi Mulungu4 atumiza kwa iwo machitidwe akusocheretsa, kuti akakhulupilire chimene chili chabodza, 12kuti iwo onse akaweruzidwe amene sanakhulupilire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama. 13Koma ife tifuna kuyamika Mulungu5 nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa mwa Ambuye, kuti Mulungu6 wakusankhani inu kuyambira pachiyambi kufikira ku chipulumutso m’chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiliro cha choonadi: 14kumene iye anakuitanani mwa uthenga wathu wabwino, kukalandira ulemelero wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 15Chomwecho, abale, chilimikani, ndi kugwiritsitsa malangizo amene mwaphunzitsidwa, kaya ndi mwa mau kapena mwa kalata. 16Koma Ambuye wathu Yesu Khristu mwini, ndi Mulungu7 komanso Atate wathu, amene anatikonda, ndipo anatipatsa ife chitonthonzo choonekera kunja ndi chiyembekezo chabwino mwa chisomo, 17limbikitsani mitima yanu, ndipo khazikikani mu ntchito iliyonse yabwino ndi mau.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu