Mutu 19

1Ndipo Iye analowa ndi kudutsira ku Yeriko. 2Ndipo taonani, [panali] munthu dzina lake Zakeyu, ndipo iyeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali munthu wolemera. 3Ndipo iye anafunitsitsa kumuona Yesu kuti anali ndani: ndipo iye sanakwanitse popeza panali khamu la anthu, chifukwa iye anali wamfupi mu msinkhu. 4Ndipo pakuthamanga anakwera mu mkuyu kuti amuwone Iye, pakuti amadutsira [njira] imeneyo. 5Ndipo pamene Iye anafika pamalopo, Yesu anayang’ana m’mwamba ndipo anamuona, ndipo anati kwa iye, Zakeyu, fulumira tsika pansi, pakuti lero ndikuyenera kukhala m’nyumba mwako. 6Ndipo iye anafulumira natsika pansi, ndipo anamulandira Iye ndi chimwemwe. 7Ndipo onse anang’ung’uza ataona [ichi], nanena, Iyeyu analowa nakhala ndi munthu wochimwa. 8Koma Zakeyu anayimilira ndi kunena kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, theka la katundu wanga ndidzapereka kwa osauka, ndipo ngati ndinatenga kwa munthu aliyense mwa chinyengo, ndidzam’bwezera [iye] kanayi. 9Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chafika pa nyumba iyi, monga iyeyunso ali mwana wa Abrahamu; 10pakuti Mwana wa munthu wafika kusakasaka chimene chili chotayikacho.

11Komatu pamene iwo amamvetsera zinthu izi, Iye anaonjezera polankhula fanizo, chifukwa anawandikira ku Yerusalemu ndipo iwo anaganiza kuti ufumu wa Mulungu1 watsala pang’ono kuti uwonekere. 12Chomwecho Iye anati, Munthu wa fuko lomveka anapita ku dziko lakutali kukadzilandilira yekha ufumu, ndi kubwerako. 13Ndipo pamene anayitana akapolo ake khumi, anawapatsa iwo ndalama khumi, ndipo anati kwa iwo, Chitani nazoni malonda ndikubwera. 14Komatu nzika zake zinamuda iye, ndipo zinatumiza akazembe pambuyo pake, nanena, Ife sitifuna [munthu] uyu kuti atilamulire. 15Ndipo kunachitika kuti pobwerera, atalandira ufumu, anafunitsitsa kuti akapolo ake amene anawapatsa ndalama aja ayitanidwe kwa iye, cholinga kuti adziwe phindu limene aliyense wa iwo wapanga pochita malonda. 16Ndipo woyamba anabwera, nanena, Mbuye [wanga], ndalama yanu yapindula ndalama zina khumi. 17Ndipo anati kwa iye, [Wachita] bwino, iwe kapolo wokhulupirika; chifukwa unakhala wokhulupirika mu chimene chinali chaching’ono, khala wolamulira pa mizinda khumi. 18Ndipo wachiwiri anabwera, nanena, Mbuye [wanga], ndalama yanu yapanga ndalama zina zisanu. 19Ndipo iye anatinso kwa uyu, Ndipo iwe, khala wolamulira mizinda isanu. 20Ndipo wina anabwera, nanena, Mbuye [wanga], taonani, ndalama yanu [ndi iyi] imene ndinayisunga mu kansalu. 21Pakuti ine ndinaopa inu chifukwa ndinu munthu wa nkhanza: mumatenga chimene simunayike pansi, ndipo mumakolola chimene simunafetse. 22Anati kwa iye, Zochoka pakamwa pako ndidzakuweruza nazo iwe, kapolo woipa: iwe unadziwa kuti ndine munthu wa nkhanza, wotenga chimene sindinayike pansi ndi kukolola chimene sindinafetse. 23Ndiye chifukwa chiyani sunapereke ndalama yanga kwa wosunga ndalama; ndipo ine ndikanatha kuilandira pobwera ndi phindu lake? 24Ndipo iye anati kwa iwo amene anaimilira pamenepo, Mlandeni iye ndalamayo ndipo muipereke kwa iye amene ali ndi ndalama khumi. 25Ndipo iwo anati kwa Iye, Ambuye, ali kale ndi ndalama khumi. 26Pakuti ndinena kwa inu, kuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe, ngakhale chimene ali nacho chidzalandidwa kwa iye. 27Kuonjezera apo adani anga, amene sanafune ine kuti ndiwalamulire, abweretseni kuno ndipo muwaphe [iwo] pamaso panga.

28Ndipo atanena zinthu izi, Iye anawatsogolera, napita ku Yerusalemu.

29Ndipo kunachitika kuti pamene anawandikira ku Betefage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Azitona, anatumiza awiri a ophunzira ake, 30nanena, Pitani m’mudzi woyang’anana ndi [inu], kumeneko mukapeza, pakulowa, mwana wa bulu womangidwa, amene palibe [mwana] wa munthu anakhalapo nthawi ina iliyonse: m’masuleni ameneyo ndipo m’bweretseni iye [kuno]. 31Ndipo ngati wina akufunsani inu, Chifukwa chiyani mukum’masula [iye]? Pamenepo mukanene ndi iye, Chifukwa Ambuye akumfuna. 32Ndipo iwo amene anatumidwa, atapita panjira yawo, anapeza monga ananenera kwa iwo. 33Ndipo pamene amamasula mwana wa buluyo, eni ake anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukumasula mwana wa buluyo? 34Ndipo iwo anati, Chifukwa Ambuye amufuna iye. 35Ndipo iwo anamtengera iye kwa Yesu; ndipo atayala zovala zawo pa mwana wa buluyo, anamuyika Yesu pa [iye]. 36Ndipo pamene Iye amapita, anayala zovala zawo m’njira. 37Ndipo pamene Iye amawandikira, atatsetsereka kale pa phiri la Azitona, unyinji onse wa ophunzira unayamba, kukondwera, ndi kuyamika Mulungu2 ndi mau okweza pa ntchito zonse za mphamvu zimene iwo anaziona, 38nanena, Yodala Mfumu yakudza m’dzina la Ambuye: mtendere ukhale kumwamba, ndi ulemelero m’mwambamwamba. 39Ndipo ena mwa Afarisi m’khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu. 40Ndipo Iye poyankha anati kwa iwo, Ndinena kwa inu, ngati awa adzakhala chete, miyala ndi imene idzafuula. 41Ndipo pamene Iye amawandikira, pakuona mzindawo, anaulilira, 42nanena, Ukanadziwa, ngakhale kuti, mu tsiku lako ili, zinthu zimene zili za mtendere wako: koma tsopano zabisika pamaso pako; 43pakuti masiku adzafika pa iwe, kuti adani ako adzakumangira linga mozungulira iwe, ndipo adzakutsekera iwe, nazakusunga mbali zonse, 44ndipo adzakugwira iwe ngakhale pamodzi ndi nthaka, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa mwala umzake: chifukwa sunadziwe nyengo ya kuyenderedwa kwako.

45Ndipo polowa m’kachisi, Iye anayamba kutulutsa iwo amene amagulitsa ndi kugula m’menemo, 46nanena nawo, Kwalembedwa, Nyumba yanga ndi nyumba yopemphereramo, koma inu mwaipanga kukhala phanga la achifwamba. 47Ndipo Iye amaphunzitsa tsiku ndi tsiku m’kachisi: ndipo ansembe akulu ndi alembi ndi akulu a anthu anafuna kumuononga Iye, 48ndipo sanapeze chimene adzachita, pakuti anthu onse anakangamira pa Iye kumumvera.

1Elohimu2Elohimu