Mutu 1
1Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu1, molingana ndi lonjezano la moyo, moyo umene uli mwa Khristu Yesu, 2kwa Timoteyo, mwana wanga wokondedwa: chisomo, chifundo, mtendere, zochokera kwa Mulungu2 Atate, ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.
3Ine ndiyamika Mulungu3, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, m’mene sindinasiye kukumbukira iwe m’mapemphero anga usiku ndi usana, 4pokhumbitsitsa kukuona iwe, pokumbukira misozi yako, kuti ndikadzale ndi chimwemwe; 5pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chimene chakhala mwa inu, chimene poyamba chinakhala mwa gogo wako Loisi, ndi mwa mayi wako Yunike, ndipo ndakopeka mtima kuti mwa iwenso. 6Pakuti pachifukwa chimenechi ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu4 imene ili mwa iwe pakuyika kwa manja anga. 7Pakuti Mulungu5 sanatipatse ife mzimu wa mantha, koma wa mphamvu, ndi wa chikondi, ndi wakulingalira mwa nzeru. 8Chomwecho musachite manyazi ndi umboni wa Ambuye wathu, kapena wa ine ngati wandende wake; koma umve zoipa pamodzi ndi uthenga wabwino, molingana ndi mphamvu ya Mulungu6; 9amene anatipulumutsa ife, ndipo anatiyitana ife ndi mayitanidwe oyera, osati kolingana ndi ntchito zathu, koma kolingana ndi cholinga chake komanso chisomo, chimene chinaperekedwa kwa ife mwa Khristu Yesu zisanafike nthawi zoyamba, 10koma tsopano chaonetsedwa mwa kuonekera kwa Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, amene anaitha imfa, ndi kuonetsera poyera moyo ndi chisavundi mwa uthenga wabwino; 11umene ine ndinasankhidwa mtumiki ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa amitundu. 12Pachifukwanso ichi ndizunzika zinthu zimenezi; koma ndilibe manyazi; pakuti ndimdziwa amene ndimkhulupirira, ndipo ndakopeka kuti ali wothekera kusungira pa tsiku limenelo chikhulupiriro chimene ndayikiza kwa iye. 13Ugwiritsitse ndi kutsatira chiphunzitso chabwino, chimene [mau] ake unamva kwa ine, m’chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu. 14Usunge, mwa Mzimu Woyera amene akhalira mwa ife, uthenga umene unalandira. 15Dziwa ichi, kuti onse amene ali m’Asiya, amene ndi Fugelo ndi Hermogene, anabwerera kusiyana ndi ine. 16Ambuye apereke chifundo kunyumba kwa Onesiforo, pakuti kawirikawiri anatsitsimutsa ine, ndipo sanachite manyazi ndi unyolo wanga; 17koma pokhala m’Roma anandifunafuna mwa khama, ndipo anandipeza [ine] — 181 Ambuye apereke kwa iye kupeza chifundo kuchokera kwa Ambuye m’tsiku limenelo — ndi m’mene anachitira utumiki m’Efeso iwe ukudziwa bwino lomwe.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu