Mutu 1
1Inetu ndinakonza mau oyamba aja, iwe Teofilo, okhudza zinthu zonse zimene Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa, 2kufikira tsiku limenelo, lomwe pokhala mwa Mzimu Woyera anawalamulira ophunzira amene anawasankha, Iye anatengedwa kupita kumwamba; 3kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo, atamva zowawa, ndi zitsimikizo zambiri; zimene zinaonedwa ndi iwo m’masiku makumi anayi, ndi kulankhula za zinthu zokhudza ufumu wa Mulungu1; 4ndipo, pakusonkhana nawo pamodzi ndi [iwo], anawalamulira kuti asachoke mu Yerusalemu, koma kuti adikire lonjezano la Atate, limene [Iye anati] munalimva kwa Ine. 5Pakutidi Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera asanapite masiku ambiri kuyambira pano.
6Pamenepo iwo, pokhala pamodzi, anamfunsa Iye nati, Ambuye, Kodi nthawi yake ndi ino imene mudzabwenzeretsa ufumu wa Israyeli? 7Ndipo Iye anati kwa iwo, Sikwainu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wa Iye yekha; 8komatu mulandira mphamvu, Mzimu Woyera akabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya ndi m’Samariya, ndi malekezero a dziko lapansi. 9Ndipo atalankhula zinthu izi anatengedwa kupita kumwamba, iwo anamuona [Iye], ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa pamaso pawo.
10Ndipo adakali chipenyere m’mwamba, pamene Iye amapita, taonani, anthu awirinso anayimilira pambali pawo atavala zovala zoyera, 11amenenso anati, Amuna a Galileya, muyimiranji ndi kuyang’ana m’mwamba? Yesu uyu amene wachotsedwa kwa inu kupita m’mwamba, adzabweranso m’njira yomweyi imene mwamuona Iye akupita m’mwamba. 12Kenako iwo anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri lotchedwa [phiri] la Azitona, limene linali pafupi ndi Yerusalemu, ulendo woyenda tsiku la sabata. 13Ndipo pamene anafika mu [mzindamo], anakwera m’chipinda cha pamwamba, m’mene mumakhala Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo [mwana] wa Alifeyu, ndi Simoni Zelote, ndi Yuda [m’bale wake] wa Yakobo. 14Iwo onse anadzipereka okha ndi cholinga chimodzi kupemphera kosalekeza, ndi akazi [angapo], ndi Mariya mayi wake wa Yesu, ndi abale ake. .
15Ndipo m’masiku amenewo Petro, pakuyimilira pakati pa abale, anati, (gulu la anthu [amene] anali pamodzi [analipo] pafupifupi zana limodzi ndi makumi awiri,) 16Abale, kunali koyenera kuti malemba akwaniritsidwe, amene Mzimu Woyera analankhula pachiyambi, kudzera pakamwa pa Davide, zokhudza Yudase, amene anali mtsogoleri wa iwo amene adamgwira Yesu; 17pakuti iye anawerengedwa pakati pathu, ndipo analandira gawo mu utumiki uwu. 18(Zoonadi [munthu] uyu anagula munda ndi cholowa cha choipacho, ndipo, atagwa cha mutu, anaphulika pakati, ndipo matumbo ake onse anakhutukira kunja. 19Ndipo kunadziwika kwa onse okhala m’Yerusalemu, kotero kuti munda umenewo unatchedwa monga mwa manenedwe awo Akeldama; ndiko kuti, munda wa mwazi.) 20Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalmo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasapezeke wokhalamo m’menemo; ndipo, kuyang’anira kwake kutengedwe ndi wina. 21Pamenepo ndi kofunikira, kuti kwa anthu amene anasonkhana ndi ife mu nthawi zonse zimene Ambuye Yesu anabwera ndi kupita pakati pathu, 22kuyambira pa ubatizo wa Yohane kufikira tsiku limene anatengedwa kuchoka pakati pathu, m’modzi wa awa akhale mboni pamodzi ndi ife ya kuuka kwake.
23Ndipo iwo anasankha anthu awiri, Yosefe, wotchedwa Barsada, amene bambo ake anali Yusto, ndi Matiya. 24Ndipo iwo anapemphera nati, Inu Ambuye, wodziwa za mumtima mwa tonse, tionetsereni kuti ndani mwa awiriwa amene Inu mwamsankha, 25kulandira gawo la utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera pamene Yudase anagwa mwa kuchimwa ndi kupita malo a iye yekha. 26Ndipo iwo anachita maere pa iwo, ndipo maere anamgwera Matiya, ndipo anawerengedwa ndi atumwi khumi ndi m’modziwo.
1Elohimu