Mutu 14
1Tsopano iye amene ali wofooka m’chikhulupiliro alandiridwe, osati movutika m’maganizo ndi mafunso. 2Munthu wina atsimikizika kuti akhoza kudya zinthu zonse; koma wofooka amangodya masamba. 3Iye amene akudya zonse asachepse iye amene sakudya zonse: pakuti Mulungu1 amulandira iye. 4Ndiwe ndani kuti uweruza wantchito wa mwini wake? Kwa mbuye wake akhala wachilili kapena wakugwa. Ndipo iye azadzutsidwa; pakuti Ambuye ali nako kuthekera komudzutsa. 5Munthu wina amalitenga tsiku lina kukhala lopambana kuposa lina; wina amawatenga masiku onse kukhala [chimodzimodzi]. Aliyense akhale otsimikizika m’maganizo ake. 6Iye amene amasamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye. Ndipo iye amene amadya, akudya kwa Ambuye, pakuti iye amalemekeza Mulungu2; ndipo iye amene samadya, achita ichi kwa Ambuye ndipo alemekeza Mulungu3. 7Pakuti palibe wa ife amene amakhala ndi moyo kwa iye yekha, ndipo palibe amene amafa kwa iye yekha. 8Pakuti tonse ngati tikhala ndi moyo, tikhala ndi moyo kwa Ambuye; ndipo ngati tifa, timafa kwa Ambuye: pamenepo ngati tonse tikhala ndi moyo, komanso ngati tifa, tonsefe ndife a Ambuye. 9Pakuti kufika pamenepa Khristu anafa nakhalanso ndi moyo, kuti akalamulire akufa ndi amoyo omwe. 10Koma iwe, chifukwa chiyani uweruza m’bale wako? kapenanso, iwe, chifukwa chiyani upeputsa m’bale wako? Pakuti tonse tidzaonekera pa mpando wa chiweruzo wa Mulungu4. 11Pakuti kwalembedwa, Ndikhala ndi moyo, atero Ambuye, kuti kwa Ine bondo lililonse lipinde, ndi lilime lililonse livomereze kwa Mulungu5. 12Pamenepo tsopano aliyense wa ife adzayankha mlandu wake kwa Mulungu6. 13Tiyeni pamenepo tisaweruzanenso wina ndi mzake; koma makamaka weruzanani ichi, kuti musayike chopunthwitsa kapena msampha pa m’bale wanu. 14Ine ndikudziwa, ndipo ndikutsimikizika mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chodetsedwa pa chokha; pokhapokha kwa iye amene achitenga chilichonse kukhala chodetsedwa, kwa munthu ameneyo [chili] chodetsedwa. 15Pakuti pa chifukwa cha nyama m’bale wako akhumudwa, suyendanso molingana ndi chikondi. Musamuwononge ndi nyama iye amene Khristu anamufera. 16Musalore pamenepo chabwino chanu chilankhulidwe ngati choipa; 17pakuti ufumu wa Mulungu7 suli mu kudya ndi kumwa, koma kulungama, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18Pakuti iye amene mu izi atumikira Khristu ali wovomerezeka kwa Mulungu8 ndipo alandiridwa ndi anthu.
19Pamenepo tiyeni tilondole zinthu zobweretsa mtendere, ndi zinthu zimene munthu amangilirana nazo wina ndi mzake. 20Chifukwa cha nyama musaononge ntchito ya Mulungu9. Zinthu zonse zilidi zoyera; koma kuli koyipa kwa munthu amene ali wokhumudwa pamene akudya. 21Ndi kwabwino osadya nyama, kapena kumwa vinyo, kapena [kuchita kalikonse] kamene m’bale wako akhumudwa nako, kapena kutsutsika nako, kapenanso kufooka nako. 22Kodi iwe uli ndi chikhulupiliro? Khala nacho kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu10. Wodala munthu amene samadziweruza yekha mu zinthu zimene wazivomereza. 23Koma iye amene akayika, pamene akudya, atsutsidwa; chifukwa sakuchita izi mwa chikhulupiliro; koma kalikonse kopangidwa osati mwa chikhulupiliro ndi tchimo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu