Mutu 12

1Pamenepo Yesu, atatsala masiku asanu ndi limodzi pasaka asanafike, anabwera ku Betaniya, kumene kunali [munthu] wakufa Lazaro, amene Yesu anamudzutsa pakati pa akufa. 2Pamenepo iwo anamukonzera mgonero kumeneko, ndipo Marita anatumikira, koma Lazaro anali m’modzi wa iwo akukhala pa gome ndi Iye. 3Pamenepo Mariya, atatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a nardo a mtengo wapatali, anadzodza mapazi a Yesu, ndipo anapukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, ndipo nyumba yonse inadzadza ndi fungo lonunkhira la mafutawo. 4Pamenepo m’modzi wa ophunzira ake, Yudase [mwana] wa Simoni, Iskariote, amene akuyenera kumpereka Iye, anati, 5Chifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe marupiya mazana atatu ndi kupereka kwa osauka? 6Komatu iye analankhula izi, osati kuti amasamala za osauka, koma chifukwa kuti anali wakuba ndipo thumba limakhala ndi iye, ndipo amatengako zimene zimayikidwa m’menemo. 7Pamenepo Yesu anati, Mleke iye pakuti anasungira ichi pa tsiku la kuyikidwa kwanga; 8pakuti osauka adzakhala ndi inu nthawi zonse, koma simuli nane nthawi zonse.

9Khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Iye anali kumeneko; ndipo iwo anabwera, osati chifukwa cha Yesu yekha, komanso kuti adzamuone Lazaro amene Iye anamuukitsa kwa akufa. 10Koma ansembe akulu anapangana kuti amuphenso Lazaro, 11chifukwa Ayuda ambiri anachoka chifukwa cha iye ndipo anakhulupilira pa Yesu.

12M’mawa wa tsiku linalo khamu lalikulu limene linabwera ku phwando, atamva kuti Yesu akubwera m’Yerusalemu, 13anatenga nthambi za kanjedza napita kukakumana naye, ndipo anafuula, Hosanna, wodala iye wakudza m’dzina la Ambuye, mfumu ya Israyeli. 14Ndipo Yesu, pamene anapeza mwana wa bulu, anakhala pa iye, monga kunalembedwa, 15Usaope, mwana wa mkazi wa Zioni: taona, Mfumu yako ikubwera, yokhala pa msana pa mwana wa bulu. 16 [Tsopano] ophunzira ake sanadziwe zinthu zimenezi pachiyambi; koma pamene Yesu anakwezedwa, pamenepo iwo anakumbukira kuti zinthu izi zinalembedwa za Iye, ndipo kuti iwo anachitira zinthu izi kwa Iye. 17Pamenepo khamu limene linali ndi Iye linachitira umboni chifukwa anayitana Lazaro kutuluka m’manda, ndipo anamtulutsa m’manda, ndipo anamuukitsa pakati pa akufa. 18Pameneponso khamu linakumana naye chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro ichi. 19Pamenepo Afarisi anati kwa wina ndi mzake, Muona kuti simupindula kanthu: taonani, pakuti dziko limtsatira Iye.

20Ndipo panali Ahelene pakati pa iwo amene anabwera kuti akalambire paphwando; 21pamenepo awa anabwera kwa Filipo, amene anali wa ku Betsaida wa Galileya, ndipo iwo anamufunsa iye nati, Mbuye, tifuna kuona Yesu. 22Filipi anabwera ndipo anamuuza Andreya, [ndipo pameneponso] Andreya anabwera ndi Filipo, ndipo iwo anamuuza Yesu. 23Koma Yesu anayankha iwo nati, Ola lafika kuti Mwana wa munthu alemekezedwe. 24Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa mu nthaka ndi kufa, ikhala payokha; koma ngati ifa, ibereka chipatso chochuluka. 25Iye wakukonda moyo wake adzautaya, ndipo iye wakuda moyo wake m’dziko ili adzausungira ku moyo wosatha. 26Ngati wina atumikira Ine, ameneyo Atate adzamchitira ulemu.

27Tsopano moyo wanga wasautsika, ndipo ndidzanena chiyani? Atate ndipulumutseni ku ola ili. Koma chifukwa cha ichi ndinabwerera ola limeneli. 28Atate lemekezani dzina lanu. Pamenepo anadza mau ochokera kumwamba, Ine ndidzalemekeza ndipo ndililemekezanso. 29Pomwepo khamulo, limene linaima [pamenepo] ndi kumva [ichi], linanena kuti kwagunda. Ena anati, Mngelo wayankhula ndi Iye. 30Yesu anayankha nati, Osati pachifukwa changa kuti mau amenewa anabwera, koma chifukwa cha inu. 31Tsopano pali chiweruzo cha dziko ili; tsopano mkulu wa dziko lapansi ili adzatayidwa kunja: 32ndipo Ine, ngati ndidzakwezedwa kuchoka dziko lapansi, ndidzakokera onse kwa Ine. 33Komatu izi analankhula kuzindikiritsa imfa yanji akuyenera Iye kufa. 34Khamu linamuyankha Iye, Ife tinamva kuchokera m’chilamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya; ndipo Inu munena bwanji kuti Mwana wa munthu akuyenera kukwezedwa? Ndani ameneyu, Mwana wa munthu? 35Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Komabe mwa kanthawi kochepa kuunika kuli pakati panu. Yendani pamene inu muli ndi kuunika, kuti mdima usakupitilireni. Ndipo iye woyenda mu mdima sadziwa kumene akupita. 36Pamene kuunika muli nako, khulupilirani m’kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunika. Yesu ananena zinthu izi, ndipo anapita kukazibisa yekha kwa iwo.

37Komatu ngakhale Iye anachita zizindikiro zambiri pamaso pawo, sanamkhulupilire Iye, 38kuti mau a mneneri Yesaya amene analankhula akwaniritsidwe, Ambuye, ndani amene wakhulupilira kulankhula kwathu? Ndipo dzanja la Ambuye lavumbulutsidwa kwa ndani? 39Pa chifukwa chimenechi iwo sanakhulupilire, chifukwa Yesaya analankhulanso, 40Iye anatseka maso awo ndiponso anaumitsa mitima yawo, kuti asaone ndi maso awo, ndi kuzindikira ndi mitima yawo ndi kutembenuka, ndi kuwachiritsa iwo. 41Zinthu izi analankhula Yesaya chifukwa iye anaona ulemelero wake ndipo analankhula za Iye. 42Kungakhale kutero kuchoka pakati pa akulunso ambiri anakhulupilira pa Iye, koma chifukwa cha Afarisi sanathe kumuvomereza [Iye], kuti asatulutsidwe msunagoge: 43pakuti iwo anakonda ulemelero kuchoka kwa anthu osati ulemelero kuchoka kwa Mulungu1.

44Koma Yesu anafuula nati, Iye wakukhulupilira pa Ine, sakhulupilira pa Ine, koma pa Iye amene anandituma Ine; 45ndipo iye wondiona Ine, waona Iye amene anandituma Ine. 46Ine ndabwera m’dziko lapansi [monga] kuwala, kuti aliyense wokhulupilira pa Ine asakhale mu mdima; 47ndipo ngati aliyense amva mau anga ndipo sawasunga [iwo], Sindimuweruza iye, pakuti sindinabwere kuti ndiweruze dziko lapansi, koma kuti ndikapulumutse dziko lapansi. 48Iye wakukana Ine ndipo salandira mau anga, ali naye womuweruza iye: mau amene Ine ndalankhula, amenewa adzamuweruza iye tsiku lomaliza. 49Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma Ine ameneyo Iye mwini anandipatsa zoti ndinene ndiponso zoti ndilankhule; 50ndipo ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Pamenepo zimene Ine ndilankhula, monga Atate wanena kwa Ine, zimenezo ndilankhula.

1Elohimu