Mutu 6

1Khalani tcheru kuti musachite zachifundo pamaso pa anthu kuti akuoneni iwo, pakuti mukatero mulibe mphoto ndi Atate wanu amene ali kumwamba. 2Pamene muchita za chifundo, musamayimba lipenga monga achinyengo amachitira m’masunagoge ndi m’misewu, kuti akalandire ulemerero kwa anthu. Ndinenetsadi kwa inu, iwo apezeratu mphoto yawo. 3Koma inu pamene muchita za chifundo, musalole dzanja lanu lamanzere lidziwe chimene dzanja lanu lamanja lachita; 4kuti zachifundo zanu zikhale za chinsinsi ndipo Atate wanu amene amaona za mtseri adzabwenzera [izo] kwa iwe.

5Ndipo pamene mupemphera, musakhale ngati achinyengowo; pakuti amakonda kupemphera atayimilira m’masunagoge ndi m’mphambano za m’msewu kuti akaonekere kwa anthu. Ndinenetsadi kwa inu, iwo alandiriratu mphoto yawo. 6Koma iwe, pamene upemphera, lowa m’chipinda chako, utatseka zitseko zako, pemphera kwa Atate wako amene ali mtseri, ndi Atate wako amene amaona za mtseri azakupatsa [izo] kwa iwe. 7Koma pamene ukupemphera, usamabwereze pachabe, monga amachitira a mitundu; pakuti aganiza kuti iwo adzamveredwa pakulankhula kwambiri. 8Inuyo musafanizidwe nawo, pakuti Atate wanu adziwa zinthu zimene mudzifuna musanapemphe [chilichonse] kwa Iye. 9Chomwecho pempherani inu: Atate wathu amene muli kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe, 10ufumu wanu udze, chifuniro chanu chichitike monga kumwamba chomwecho pansi pano; 11mutipatse ife lero mkate wathu wofunikira, 12ndipo mutikhululukire ife mangawa athu, monganso ife tawakhululukira a mangawa athu, 13ndipo musatitsogolere ife ku mayesero, koma mutipulumutse ife ku choipa. 14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu wakumwamba adzakukhululukiranso zolakwa [zanu], 15koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sazakhululukira zolakwa zanu.

16Ndipo pamene musala kudya, musakhale ngati onyengawo, ogwetsa nkhope zawo ndi chisoni; pakuti amayipitsa nkhope zawo, kuti akaonekere kwa anthu kuti akusala kudya: ndinenetsadi kwa inu, iwo alandiliratu mphoto yawo. 17Koma inu, [pamene] musala kudya, dzolani mafuta m’mutu mwanu ndi kutsuka nkhope zanu, 18kuti musaonekere kwa anthu kuti mukusala kudya, komatu kwa Atate wanu amene ali mtseri; ndipo Atate wanu amene ali mtseri adzapereka [ichi] kwa inu.

19Musazikundikire nokha chuma cha padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimachiononga, ndipo mbala zimakumba ndi kuchiba; 20koma muzikundikire nokha chuma chili kumwamba, kumene dzimbiri kapena njenjete sizingaononge, ndipo mbala sizingakumbe ndi kuchiba; 21pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wakonso umakhala komweko.

22Nyali ya thupi ndilo diso; ngati diso lako lidzakhala la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala: 23koma ngati thupi lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lakuda. Chotero ngati kuwala kumene kuli mwa inu kukhala mdima, mdima umenewu udzakhala waukulu bwanji!

24Palibe munthu amene adzatumikira ambuye awiri; pakuti mwina adzada wina ndi kukonda winayo, kapenanso adzakangamira wina ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu1 ndi chuma. 25Pachifukwa chimenechi ndinena kwa inu, musadandaule zokhudza moyo wanu, kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya, ndi thupi lanu siliposa chovala? 26Taonani mbalame za kumwamba, kuti sizifesa ayi, kapena sizimakolola ayi, kapenanso sizimatutira mu nkhokwe, ndipo Atate wanu wakumwamba azidyetsa izo. Kodi inu simuposa zimenezo? 27Kodi ndani mwa inu pakuda nkhawa akhoza kuonjezera kukula kwa msinkhu wake ndi mkono umodzi? 28Ndipo chifukwa chiyani mudandaula zokhudza zovala? Penyetsetsani mwachidwi maluwa a kuthengo, momwe amakulira: samagwiritsa ntchito kapena kupota; 29komatu ndinena kwa inu, kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake sanavaleko monga limodzi mwa awa. 30Koma ngati Mulungu2 aveka chotero udzu wa kuthengo, umene ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto, kodi Iye sadzachita kwakukulu ndi inu, inu achikhulupiriro chochepa? 31Chotero musadere nkhawa ndi kunena, kodi tidzadya chiyani? Kapena tidzamwa chiyani? Kapenanso tidzavala chiyani? 32pakuti zonse zimenezi mafuko azifuna; pakuti Atate wanu wakumwamba adziwa kuti muzisowa zonse zimenezi. 33Koma yambani mwafuna ufumu wa Mulungu3 ndi chilungamo chake, ndipo zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu. 34Kotero musadere nkhawa za mawa, pakuti mawa lizadzidera nkhawa lokha. Zokwanira za tsiku [zili] ndi zovuta zake.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu