Mutu 4

1Chotero anthu atiyese ife monga atumiki a Khristu, ndi adindo osunga zinsinsi za Mulungu1. 2Kuonjezerapo pamenepa, ndi pofunika mwa mdindo, kuti akhale munthu wokhulupirika. 3Komatu kwa ine ndi zochepa kuti ndikaweruzidwa ndi inu kapena bwalo lililonse. Kapenanso sindidziweruza ndekha. 4Pakuti ndilibe chikumbumtima chilichonse mwa ine; komatu sindikudzilungamitsa mwa ichi: koma iye amene amandiweruza ine ndi Ambuye. 5Chotero musaweruze kalikonse nthawi yake isanakwane, kufikira Ambuye akadza, amenenso adzabweretsa poyera zinthu zobisika za mumdima, ndipo adzaonetsera uphungu wa m’mitima; ndipo pamenepo aliyense adzakhala nawo mayamiko ake kuchokera kwa Mulungu2.

6Tsopano zinthu izi, abale, ndazisamutsa m’zochita zawo, kudzibweretsa kwa ine mwini ndi Apolo, pachifukwa cha inu, kuti mukaphunzire mwa ife phunziro losalola malingaliro anu kudutsa pamwamba pa zimene zinalembedwa, kuti inu musazitukumule pa chimenechi kwa wina ndi mzake. 7Pakuti ndani amene amakusiyanitsani inu? Ndipo inu muli ndi chiyani chimene simunalandire? Koma ngatinso inu munalandira, chifukwa chiyani mukudzitukumula ngati kuti simunalandire? 8Mwakwanitsidwa kale; mwalemera kale; mwalamulira popanda ife; ndipo ine ndikanakonda kuti mulamulire, cholinga kuti ifenso tikalamulire ndi inu. 9Pakuti ine ndiganiza kuti Mulungu3 watiyikira ife atumwi komaliza, osankhidwa kufikira imfa. Pakuti ife takhala choonetsedwa kudziko lapansi, kwa angelo pamodzi ndi anthu omwe. 10Ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ochenjera mwa Khristu: ndife ofooka, koma inu amphamvu: ndinu a ulemelero, koma ife onyozeka. 11Kufikira ola lino ife tonse tili ndi njala komanso ludzu, ndipo tili a maliseche, ndipo takhomedwa, ndipo tayendayenda opanda pokhala, 12ndipo tavutika, kugwira ntchito ndi manja athu. Potembeleredwa, ife tadalitsa; pozunzidwa, ife tapilira; 13Potukwanidwa, tapepesa: ife tasanduka zinyalala za dziko lapansi, okanidwa ndi onse, kufikira pano. 14Ndalemba izi osati kuti ndikuchititseni manyazi inu, koma ngati ana anga okondedwa ndikukuchenjezani. 15Pakuti ngati mukhala ndi aphunzitsi mwa Khristu zikwi khumi, pakuti ambiri sali atate; pakuti mwa Khristu Yesu ndakuberekani inu kudzera mu uthenga wabwino. 16Ine ndikupemphani inu pamenepo, kuti mukhale onditsanza ine.

17Pachifukwa chimenechi ndakutumizani inu kwa Timoteyo, amene ali mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakukumbutsani njira zanga monga zilili mwa Khristu, molingana ndi m’mene ine ndimaphunzitsira kulikonse mu mipingo yonse. 18Koma ena akudzitukumula, ngati kuti sindinabwere kwa inu; 19koma ine ndidza msanga kwa inu, ngati Ambuye alola; ndipo ine ndizadziwa, osati mau a iwo akudzitukumula, koma mphamvu yawo. 20Pakuti ufumu wa Mulungu4 suli m’mau, koma mu mphamvu. 21Kodi inu mudzatani? Kuti ndidzabwera kwa inu ndi chikwapu; kapena chikondi, ndi mu mzimu wakufatsa?

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu