Mutu 13
1Ngati ndilankhula ndi malilime a anthu kapena a angelo, koma ndilibe chikondi, Ndikhala ngati chinganga kapena nguli yoliritsa. 2Ndipo ngati ndili nawo uneneri, ndipo ndidziwa zinsinsi ndi chidziwitso chonse, ndipo ndikhala nacho chikhulupiliro chonse, chotero kuti chosuntha nacho mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. 3Ndipo ngati ndipereka katundu wanga yense mwa chakudya, ndipo ndipereka thupi langa kuti litenthedwe ndi moto, koma ndilibe chikondi, palibe phindu limene ndingapeze. 4Chikondi chimapilira, chimakoma mtima; chikondi chilibe nsanje ndi ena; chikondi chilibe kudukidwa ndi nsanje, sichidzikuza, 5sichimakondwera ndi makhalidwe oipa, sichitsata za icho chokha, sichipsa mtima msanga, sichilingalira zoipa, 6sichikondwera ndi zoipa koma chimakondwera ndi choonadi, 7chimapilira zinthu zonse, chimakhulupilira zinthu zonse, chimayembekeza zinthu zonse. 8Chikondi sichilephera; koma kapena mauneneri, adzapita; kapena malilime, adzaleka; kapena chidziwitso, chidzatha. 9Pakuti ife tidziwa zinthu pang’ono,ndipo timaneneranso pang’ono: 10koma pamene chinthu changwiro chafika, chimene chili pang’ono chidzatha. 11Pamene ine ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndipo ndinamva ngati mwana, ndinaganiza ngati mwana; pamene ndinakhala wamkulu, ndinasiya zimene zinali zachibwana. 12Pakuti tsopano tiona kudzera pa kalilole wosawoneka bwino lomwe, koma pamenepo tiona maso ndi maso; tsopano ndidziwa pang’ono, koma pamenepo ndidzaziwa mokwanira monganso ine ndadziwidwira. 13Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu izi; chikhulupiliro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu pa izi ndi chikondi.