Mutu 7
1Mwa ichi Melikizedeke, Mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu1 wamkulukulu, amene anakumana ndi Abrahamu pobwerera kuchoka kokupha mafumu, ndipo anamdalitsa iye; 2kwa ameneyo Abrahamu anampatsanso limodzi la magawo khumi la zonse; poyamba anasandulika Mfumu ya chilungamo, ndipo kenakonso Mfumu ya Salemu, ndiye Mfumu ya mtendere; 3wopanda atate, wopanda amayi, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe; alibe chiyambi cha masiku kapena chimaliziro cha moyo, koma wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu2, wokhalabe wa nsembe kosalekeza. 4Tsopano ganizirani m’mene ukulu wa umunthu wake unalili, kwa ameneyo [ngakhale] kholo lalikulu Abrahamu anapereka chakhumi chosankhika kuchokera mu zofunkha. 5Ndipo iwodi pakati pa ana a Levi, amene analandira unsembe, anali nawo ulamuliro wotenga chakhumi kuchokera kwa anthu monga mwa lamulo, ndiko kuchokera kwa abale awo, ngakhale kuti iwowa anachokera mchiuno mwa Abrahamu: 6koma iye amene alibe mawerengedwe a chibadwidwe anapereka chakhumi kwa Abrahamu, ndipo anamdalitsa iye amene anali ndi malonjezano. 7Koma posowa cholankhula, wamng’ono adalitsidwa ndi wamkulu. 8Ndipo pamenepa anthu akufa alandira chakhumi; koma pamenepo m’modzi mwa iwo wakuperekera umboni ndi yemwe ali ndi moyo; 9ndipo, kulankhula motero, kudzera mwa Abrahamu, Levinso, amene analandira chakhumi, nayenso anapereka chakhumi. 10Pakuti iye pamenepo anali m’chiuno mwa atate wake pamene Melikizedeke anakumana naye. 11Ngatidi pamenepo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi, pakuti anthu anali nalo lamulo loperekedwa kwa iwo molumikizana nalo, chosoweka chimene chinali pamenepo kuti wansembe auke molingana ndi dongosolo la Melikizedeke, ndipo osati kutchulidwa monga mwa dongosolo la Aroni? 12Pakuti, posandulika unsembe, pakuyeneranso kuchitika kusintha kwa lamulo. 13Pakuti iye, amene zinthu zimenezi zinanenedwa, ali wa mtundu wina, umene palibe mwa iwo akulumikizana ndi kutumikira pa guwa. 14Pakuti ndi chodziwikiratu kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda, mtundu umene Mose sanalankhuleko zokhudza ansembe. 15Ndipo kwadziwika koposa ndithu, kuti wansembe wina adzauka molingana ndi kufanana kwa Melikizedeke, 16amene anakhazikitsidwa osati monga mwa lamulo la kuthupi, koma molingana ndi mphamvu ya moyo wosaonongeka. 17Pakuti achitidwa umboni, Ndiwe wansembe wamuyaya molingana ndi dongosolo la Melikizedeke. 18Pakuti linayikidwa pambali lamulo lakalelo pakufooka kwake ndi kusapindulitsa kwake, 19(pakuti lamulo silipindulitsa kanthu,) ndipo kukhazikitsidwa kwa chiyembekezo choposa chimene chimatisendeza chifupi ndi Mulungu3. 20Ndipo sikunachitika popanda lumbiro la pangano; 21(pakuti iwo anakhala ansembe popanda lumbiro la pangano, koma iye wakulumbira ndi lumbiro la pangano, mwa iye amene anati, monga kwa iye, Ambuye walumbira, ndipo sadzalapa [mwa ilo], Ndiwe wansembe kwamuyaya [molingana ndi dongosolo la Melikizedeke];) 22momwemonso Yesu wakhala chikole cha pangano loposa. 23Ndipo iwo akhala ansembe ochuluka, pa chifukwa cha kupsinjika kupitirizabe mwa imfa; 24koma iye, chifukwa cha kupitiriza kwamuyaya, akhala ndi unsembe wosasinthika. 25Pameneponso iye ali nako kuthekera kopulumutsa iwo amene adza mwa Iye kwa Mulungu4, kukhalabe owapembedzera iwo. 26Pakuti wamkulu wa ansembe wotere anakhala kwa ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wolekanitsidwa kwa ochimwa, ndipo anakhala wamkulu kuposa miyamba: 27amene tsiku ndi tsiku analibe kusoweka, monga wamkulu wansembe, choyamba kupereka nsembe ya machimo ake omwe, kenako machimo a anthu; pakuti ichi iye anachita kamodzi kwatha pakudzipereka iye yekha. 28 Pakuti chilamulo chimayika anthu kukhala akulu ansembe, opanda chilema; koma mau a kulumbira lumbiro limene linafika chitapita chilamulo, Mwana wopanda banga nthawi zonse.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu