Mutu 5

1Pitani uko tsopano, achuma inu, lirani, chemani pa masautso anu amene akubwera kwa [inu]. 2Chuma chanu chikuola, ndipo zovala zanu zadyedwa ndi njenjete. 3Golide ndi siliva wadyeka, ndipo zilonda zawo zidzakhala mboni yokutsutsani inu, ndipo zidzadya thupi lanu ngati moto. Mwazikundikira chuma m’masiku otsiriza. 4Taonani, malipiro a antchito anu, amene akolola minda yanu, molakwitsa asungitsa kwa inu, nalira, ndipo kulira kwa iwo amene akolola kwamveka m’makutu mwa Ambuye wa makamu. 5Munakhala moyo osangalala padziko lapansi ndipo munazipembedzera nokha; mwadyetsa mitima yanu monga tsiku lophedwa; 6munamtsutsa, munamupha wolungamayo; iye sanakukanizeni inu.

7Pamenepo lezani mitima, abale, kufikira tsiku lakubwera Ambuye. Taonani, wantchito adikira chipatso chabwino cha dziko lapansi, kukhala nacho chipiliro pa icho kufikira chitalandira mvula yoyamba ndi yomaliza. 8Inunso ngalani nacho chipiliro: limbitsani mitima yanu, pakuti kubwera kwa Ambuye kwayandikira. 9Musadandaulane wina ndi mzake, abale, kuti musaweruzidwe. Taonani, woweruza wayima pakhomo. 10Tengani [monga] chitsanzo, abale, cha kuzunzika ndi kukhala ndi chipiliro, kwa aneneri, amene analankhula m’dzina la Ambuye. 11Taonani, tiwatcha iwo odala amene anapilira. Inu munamva za kupilira kwa Yobu, ndipo munaona chitsiriziro cha Ambuye; kuti Ambuye ali wodzala ndi chifundo, kusazikonda ndi chisoni.

12Koma zisanachitike zonsezi, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena pa lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndipo ayi wanu, ayi, kuti musagwe pansi pa chiweruzo.

13Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Alipo wina wakondwa? Ayimbe nyimbo ya masalimo. 14Alipo amene akudwala pakati panu? Aziyitanire yekha akulu a mpingo, ndipo iwo ampempherere iye, pomudzodza ndi mafuta m’dzina la Ambuye; 15ndipo pemphero la chikhulupiliro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Ambuye azamdzutsa iye; ndipo ngati iye akhala amene ali ndi machimo, adzakhululukidwa. 16Pamenepo vomerezanani machimo anu kwa wina ndi mzake, ndipo pemphereranani wina ndi mzake, kuti mukachiritsidwe. Pemphero la [munthu] wolungama lili ndi mphamvu koposa. 17Eliya anali munthu wakumva zomwe timva ife, ndipo iye anapemphera ndi pemphero kuti mvula isagwe; ndipo mvula sinagwe padziko lapansi kwa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi; 18ndipo anapempheranso, ndipo kumwamba kunapereka mvula, ndipo dziko lapansi linabala chipatso ndi kutumphuka.

19Abale anga, ngati wina wa inu achoka ku choonadi, ndipo wina am’bwezeretsa, 20adziwe iye amene wam’bwezeretsa wochimwayo kuchoka ku kulakwa kwake adzapulumutsa moyo ku imfa ndipo adzakwilira machimo ambiri.