Mutu 15
1Ndipo ndinaona chizindikiro china m’mwamba, chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri okhala nayo milili isanu ndi iwiri, omaliza; pakuti m’menemo mkwiyo wa Mulungu1 watsirizika.
2Ndipo ndinaona ngati nyanja ya mandala, yosakanikirana ndi moto, ndipo iwo amene anachigonjetsa chirombocho, ndi chifanizo chake, ndi chiwerengero cha dzina lake, anayima pa nyanja ya mandala, nakhala nawo azeze a Mulungu2. 3Ndipo iwo anayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu3, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Zazikulu ndi zodabwitsa ntchito zanu, Ambuye Mulungu4 Wamphamvuzonse; zolungama ndi zoona njira zanu, Inu Mfumu ya mafuko. 4Ndani amene sadzaopa [inu], Ambuye, ndi kulemekeza dzina lanu? pakuti [ndinu] woyera; pakuti mafuko onse adzabwera ndi kulambira pamaso panu; pakuti kulungama kwanu kwaonekera.
5Ndipo zitapita zinthu izi ndinaona, ndipo kachisi wa chihema cha umboni m’mwamba anatseguka; 6ndipo angelo asanu ndi awiri amene anali nayo miliri isanu ndi iwiri anatuluka mkachisi, atavala zovala zoyera ndi zonyezimira kwambiri, ndipo anazimangilira pachifuwa ndi malamba a golide. 7Ndipo chimodzi mwa zolengedwa zamoyo chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri aja mbale za golide zisanu ndi ziwiri, zodzadza ndi mkwiyo wa Mulungu5, amene akhala ku nthawi za nthawi. 8 Ndipo kachisi anadzadzidwa ndi utsi wochokera kwa Mulungu6 ndi ku mphamvu yake: ndipo palibe amene analowa mkachisimo kufikira itakwaniritsidwa miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu