Mutu 3

1Uwakumbutse kuti akhale omvera kwa akulu, kwa aulamuliro, kukhala okhulupirika pomvera, kukhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino, 2osalankhula zoipa za munthu wina, osakhala okonda mikangano, kukhala ofatsa, kusonyeza kudzichepetsa konse kwa anthu onse. 3Pakuti nafe poyamba tinakhala anthu opanda nzeru, osamvera, kusiya choonadi, kutumikira zilakolako zosiyanasiyana ndi zokondweretsa thupi, kukhala moyo wa kaduka ndi nsanje, mkwiyo, komanso maudani wina ndi mzake. 4koma pamene kukoma mtima ndi chikondi kwa munthu wa Mulungu1 Mpulumutsi wathu zaonekera, 5osati pa mfundo ya ntchito zabwino zimene [zinachitika] m’kulungama kumene ife tinachita, koma molingana ndi chifundo chake anatipulumutsa ife kudzera nkubadwanso mu uzimu mwa kukonzedwanso mwa Mzimu Woyera, 6amene iye anakhutulira pa ife mochuluka kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu; 7kuti, pamene tinalungamitsidwa mwa chisomo chake, ife tikakhale olowa mnyumba molingana ku chiyembekezo cha moyo wosatha. 8Mau ali okhulupirika, ndipo ine ndifunitsitsa kuti iwe ulimbikebe pa zinthu zimenezi, kuti iwo amene akhulupirira Mulungu2 akapenyerere ndi kusamalitsa kuchita ntchito zabwino. Zinthu zimenezi ndi zabwino ndi zopindulitsa kwa anthu. 9Koma upewe mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi mikangano, ndi magawano pokhuza lamulo; pakuti izi nzosapindulitsa komanso zachabe. 10Munthu wa mpatuko atachenjezedwa koyamba ndi kachiwiri umkanize, 11podziwa kuti munthu wotereyu wachoka pa chilungamo, ndipo wachimwa, naziweruza yekha.

12Pamene ndidzatuma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, chita machawi kubwera kwa ine ku Nikopoli; pakuti ndaganiza kudzakhalako m’nyengo yozizira. 13Zena woyimira milandu ndi Apolo uwakonzekeretse bwino pa ulendo wao, kuti kasasoweke kanthu kwa iwo; 14ndipo anthu athunso aphunzire kuchita ntchito zabwino kuti asakhale osabereka zipatso. 153 Onse amene ali ndi ine akukulonjera iwe. Uwalonjere onse amene amatikonda ife m’chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.

1Elohimu2Elohimu