Mutu 8

1M’masiku amenewo, pokhalaponso khamu lalikulu la anthu, ndipo iwo nakhala opanda kanthu kakudya, nadziyitanira yekha ophunzira ake kwa [Iye], nati kwa iwo, 2Ine ndikumva chifundo ndi khamulo, chifukwa akhala pamodzi ndi Ine kwa masiku atatu ndipo alibe kena kalikonse kakudya, 3ndipo ndikawauza amuke kunyumba kwao osadya, akomoka panjira; pakuti ena mwa iwowa akuchokera kutali. 4Ndipo ophunzira ake anamuyankha Iye, Kodi tidzakwanitsa bwanji kuwakhutitsa ndi mkate ku malo ano a chipululu? 5Ndipo Iye anawafunsa iwo, Kodi muli ndi mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri. 6Ndipo Iye analamulira khamulo likhale pansi. Ndipo atatenga mikate isanu ndi iwiriyo, Iye anayamika, nainyema [iyo] naipereka kwa ophunzira ake, kuti aipereke kwa [iwo]; ndipo iwo anaipereka kwa khamulo. 7Ndipo iwo anali nato tinsomba ting’onong’ono, ndipo atatidalitsa ito, Iye analamuliranso kuti timeneti tigawidwe kwa [iwo]. 8Ndipo iwo anadya ndi kukhuta. Ndipo anatenga zotsalira zimene zinakwana nsengwa zisanu ndi ziwiri. 9Ndipo iwo [amene anadya] analipo okwanira zikwi zinayi; ndipo Iye anawalola kuti apite.

10Ndipo pomwepo anapita kukakwera ngalawa ndi ophunzira ake, nafika kumbali ya Dalmanuta. 11Ndipo Afarisi anatuluka nayamba kutsutsana ndi Iye, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera kumwamba, kumuyesa Iye. 12Ndipo potsitsa moyo mu mzimu wake, Iye anati, Chifukwa chiyani m’badwo uwu ufuna chizindikiro? Indetu ndinena kwa inu, chizindikiro sichidzaperekedwa kwa m’badwo uwu. 13Ndipo Iye anawasiya iwo, ndipo pakukakweranso ngalawa, anapita kutsidya lina. 14Ndipo iwo anaiwala kutenga mkate, ndipo anasunga mkate umodzi okha, iwo analibenso mkate wina m’ngalawa. 15Ndipo Iye anawalamulira, nanena, Yang’anirani, chotupitsa mkate cha Afarisi ndi chotupitsa mkate cha Herode. 16Ndipo iwo anakambirana wina ndi mzake, [nanena], chifukwa tilibe mkate. 17Ndipo Yesu pakudziwa [ichi], anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukambirana kuti mulibe mkate? Kodi simuzindikira ndi kumvetsetsabe? Kodi mitima yanu idakalibe youma? 18Maso muli nawo, koma simupenya? Ndipo makutu muli nawo, koma simumva? Ndiponso simutha kukumbukira? 19Pamene ndinanyema mikate isanu kwa anthu zikwi zisanu, kodi ndi mitanga ingati ya makombo imene inu munatenga? Iwo anati kwa Iye, khumi ndi iwiri. 20Ndipo ndi mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinayi, kodi munadzala malichero angati a makombo amene munatenga? Ndipo iwo anati, isanu ndi iwiri. 21Ndipo Iye anati kwa iwo, Nanga ndi chifukwa chiyani simukutha kumvetsabe?

22Ndipo Iye anafika ku Betsaida; ndipo iwo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, ndipo anampempha kuti amkhudze iye. 23Ndipo pogwira dzanja la munthu wakhunguyo anamutsogolera kunja kwa mudzi, ndipo atamulavulira malovu m’maso mwake, anayika manja ake pa iye, ndipo anamufunsa ngati akuona kanthu. 24Ndipo pakuyang’ana m’mwamba, anati, Ndikuona anthu, pakuti ndikuwaona [iwo], ngati mitengo, ikuyenda. 25Pamenepo anasanjikanso manja ake pamaso pake, ndipo anaona bwino lomwe, ndipo anachiritsidwa naona zinthu zonse bwino lomwe. 26Ndipo anamutumiza iye kunyumba kwake, nanena, Usalowe konse m’mudzi, kapena kunena [ichi] kwa aliyense m’mudzimo.

27Ndipo Yesu anapita kwa ophunzira ake, mkati mwa mudzi wa Kaisareya Filipi. Ndipo pakuyenda panjira Iye anawafunsa ophunzira ake, nanena kwa iwo, Kodi anthu amati ndine ndani? 28Ndipo iwo anamuyankha Iye, nanena, Yohane m’batizi; ndipo ena, Eliya; koma ena, m’modzi wa aneneri. 29Ndipo Iye anawafunsa iwo, Koma inu, mumati ndine ndani? Ndipo Petro poyankha anati kwa Iye, Ndinu Khristu. 30Ndipo Iye anawauza mwachindunji, cholinga kuti asauze wina aliyense za Iye. 31Ndipo Iye anayamba kuwaphunzitsa iwo kuti Mwana wa munthu azazunzika mu zinthu zambiri, ndipo azakanidwa ndi akulu komanso ansembe akulu ndi alembi, ndi kuphedwa, ndipo pakutha masiku atatu adzaukanso. 32Ndipo Iye analankhula ichi poyera. Ndipo Petro, anamutenga [Iye] nayamba kumudzudzula. 33Koma Iye, pakutembenuka ndi kuona ophunzira ake, anamdzudzula Petro, nanena, Pita kumbuyo kwanga, Satana, pakuti malingaliro ako sali pa zinthu za Mulungu1, koma pa zinthu zimene zili za anthu. 34Ndipo atayitanitsa khamulo ndi ophunzira ake, Iye anati kwa iwo, Aliyense wofuna kubwera pambuyo panga, azikanize yekha, ndipo anyamule mtanda wake nanditsate Ine. 35Pakuti amene adzafuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi uthenga wabwino adzaupulumutsa. 36Pakuti munthu adzapindula chiyani ngati iye adzapeza dziko lonse lapansi ndi kutaya moyo wake? 37pakuti munthu adzapereka chiyani chosinthana ndi moyo wake? 38Pakuti amene adzachita manyazi ndi Ine komanso mau anga mu m’badwo uno wa chigololo ndi wochimwa, kwa iye Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi pamene adzabwera mu ulemelero wa Atate wake ndi angelo oyera.

1Elohimu