Mutu 8

1Ndipo pamene iye anatsika kuchokera ku phiri, khamu la anthu linamutsatira iye. 2Ndipo taonani, munthu wakhate anabwera kwa [iye] namgwadira, nanena, Ambuye ngati mungathe, mukhoza kundiyeretsa ine. 3Ndipo anatambasula dzanja lake namkhudza, nanena, ndikhoza; tayeretsedwa. Ndipo nthawi yomweyo khate lake linayeretsedwa. 4Ndipo Yesu analankhula kwa iye, taona iwe usauze munthu wina aliyense, koma pita, ukadzionetsere wekha kwa wansembe, ndipo ukapereke mtulo umene Mose anaukhazikitsa, ukhale umboni kwa iwo.

5Ndipo pamene Iye analowa mu Karpenao, kentuliyo anadza kwa Iye, nampempha, 6ndipo anati, Ambuye, wantchito wanga ali gone mnyumba akudwala manjenje, ndipo akuvutika koopsa. 7Ndipo Yesu analankhula kwa iye. Ine ndibwera ndipo ndidzamuchiritsa iye. 8Ndipo kentuliyo anayankha nati, Ambuye, ine sindili woyenera kuti mulowe pansi pa tsindwi langa; koma mungolankhula mau, ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. 9Pakuti inenso ndine munthu wa ulamuliro, ndipo pansi panga pali asilikali, ndipo ine ndikanena kwa [uyu], pita, amapita; ndipo kwa wina, bwera, ndipo amabwera; ndi kwa kapolo wanga, chita ichi, ndipo iye amachita chimenecho. 10Ndipo pamene Yesu anamva ichi, anali wodabwa, ndipo anati kwa iwo akumutsatira, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mu Israyeli sindinapeze chikhulupiriro chachikulu chotere. 11Komatu ndinena kwa inu, kuti ambiri adzabwera kuchokera kotulukira ndi kolowera [dzuwa], ndipo adzakhala pagome ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba; 12komatu ana a ufumu adzaponyedwa kunja kwa mdima: kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 13Ndipo Yesu anati kwa kentuliyo, pita, ndipo monga umo wakhulupilira, zikhale momwemo kwa iwe. Ndipo wantchito wake anachiritsidwa ola lomwelo.

14Ndipo pamene Yesu anafika ku nyumba ya Petro, anaona apongozi ake ali gone akudwala malungo; 15ndipo anakhudza dzanja lake, ndipo malungo anachoka mwa iye, ndipo anadzuka namtumikira Iye.

16Ndipo pakufika madzulo, anabwera nawo ambiri ogwidwa ndi ziwanda, ndipo anatulutsa mizimu ndi mau, ndipo Iye anachiritsa onse amene amadwala; 17kotero kuti chikwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa kudzera mwa Yesaya mneneri, kunena kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu ndipo ananyamula nthenda zathu.

18Ndipo Yesu pakuona khamu lalikulu la anthu litamzungulira Iye, analamula kuti apite tsidya lina. 19Ndipo mlembi anabwera ndi kunena kwa iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani kulikonse kumene mudzapita. 20Ndipo Yesu ananena kwa iye, nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndipo mbalame za mlengalenga zisa zawo; koma Mwana wa munthu alibe pamene akhoza kuikapo mutu wake. 21Koma wina wa ophunzira ake ananena kwa iye, Ambuye, ndiloleni ine ndiyambe ndapita kukaika maliro a atate wanga. 22Koma Yesu ananena kwa iye, nditsate Ine, ndipo leka akufa aike akufa awo.

23Ndipo Iye analowa m’ngalawa ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye; 24ndipo taonani, [madzi] anayamba kuchita namondwe pa nyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde; koma Iye anagona tulo. 25Ndipo ophunzira anabwera namuutsa Iye, nanena, Ambuye tipulumutseni: tikuonongeka ife. 26Ndipo Iye anati kwa iwo, muchitiranji mantha, inu a chikhulupiriro chochepa? Kenako, atadzuka, Iye anadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panali bata lalikulu. 27Koma anthu anali ozizwa, nanena, kodi ndi [munthu] wotani ameneyu, kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

28Ndipo anakumana ndi Iye, pamene anapita kutsidya lina la dziko la Agadara, anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, ali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe amene amadutsa njira imeneyo. 29Ndipo taonani, anafuula, nanena, kodi tili nanu chiyani, inu Mwana wa Mulungu1? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza ife nthawi yake isanafike? 30Tsopano panali, potalikirana ndi iwo, gulu la nkhumba zochuluka zikudya; 31ndipo ziwanda zinamupempha Iye, zinena, ngati mungatitulutse ife kunja, titumizeni mu gulu la nkhumbazo. 32Ndipo Iye analankhula kwa izo, pitani. Ndipo izo, pakutuluka, zinalowa mu gulu la nkhumba; ndipo taonani, gulu lonse [la nkhumbazo] linatsetsereka ku mtsetse ndi kulowa mnyanja, ndipo zinafera m’madzi. 33Koma iwo amene amadyetsa nkhumbazo anathawa, napita mu mzinda ndipo anafotokoza zonse zinachitika, komanso zimene zinachitikira iwo ogwidwa ndi ziwandawo. 34Ndipo taonani, mzinda onse unatuluka kukakumana ndi Yesu; ndipo pamene iwo anamuona, anamupempha [Iye] kuti achoke ku magombe awo.

1Elohimu