Mutu 23
1Ndipo khamu lonse, litamuwukira, linamtengera Iye kwa Pilato. 2Ndipo iwo anayamba kumneneza Iye, nanena, Tamupeza [munthu] uyu akusokoneza mtundu wathu, ndipo amakaniza kupereka msonkho kwa Kaisara, nanena kuti Iyeyu ndi Khristu, mfumu. 3Ndipo Pilato anamfunsa Iye nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo pomuyankha iye anati, Mwatero. 4Ndipo Pilato anati kwa ansembe akulu ndi makamuwo, Sindikupeza cholakwa mwa munthu uyu. 5Koma iwo analimbikira, nanena, Amapandutsa anthu, naphunzitsa m’Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ngakhalenso kufikira kuno. 6Koma Pilato, pakumva Galileya [akutchulidwa], anafunsa ngati munthuyo ndi m’Galileya; 7ndipo atadziwa kuti anali mu ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza kwa Herode, amenenso masiku ameneyo anali ku Yerusalemu.
8Ndipo pamene Herode anaona Yesu anasangalala kwambiri, pakuti kwa nthawi yaitali anafunitsitsa kumuona Iye, chifukwa anamva zinthu zambiri zokhudza Iye, ndipo iye anayembekezera kuona zizindikiro zochitidwa ndi Iye; 9ndipo iye anamfunsa m’mau ochuluka, koma Iye sanayankhe kanthu. 10Ndipo ansembe akulu ndi alembi anayimilira ndi kumneneza Iye mwa mavuvu. 11Ndipo Herode ndi asilikali ake atampeputsa Iye ndi kumchitira chipongwe, anamveka mwinjiro wonyezimira ndi kum’bwezera kwa Pilato. 12Ndipo Pilato ndi Herode anakhala pa ubwenzi wina ndi mzake tsiku lomwelo, pakuti iwo anakhala pa udani pakati pawo kuyambira kale.
13Ndipo Pilato, anayitanitsa pamodzi ansembe akulu ndi akulu a anthu, 14nanena nawo, Mwandibweretsera munthu uyu ngati munthu wopandutsa anthu [ku kuukira], ndipo taonani, ine ndamufunsa pamaso panu, sindinapeze kalikonse kolakwa mwa munthuyu monga mwa zinthu zomwe mukumneneza Iye; 15ngakhale Herode yemwe, pakuti ndinampereka kwa iye, ndipo taonani, palibe koyenera imfa kamene anachita Iye. 16Ndikamukwapula Iye pamenepo, ndidzam’masula. 17(Tsopano iye anali ndi mphamvu ya kuwamasulira iwo munthu m’modzi pa phwando.) 18Koma iwo anafuula pamodzi nanena, Mchotseni [munthu] uyu ndipo mutimasulire ife Baraba; 19amene anali m’modzi wa anthu oponyedwa mndende chifukwa chochita chipolowe mu mzinda, ndi kupha munthu. 20Pilato pamenepo, anafunitsitsa kumasula Yesu, nabwerezanso kulankhula [nawo]. 21Koma iwo poyankha anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni Iye. 22Ndipo iye analankhula nawonso kachitatu, Kodi [munthu] uyu wachita chiyani cholakwa? Inetu sindinapeze mwa Iye chifukwa cha kumuphera: ndingomukwapula Iye pamenepo ndi kum’masula. 23Koma iwo anakakamira ndi mau okwera, kupempha kuti apachikidwe. Ndipo mau awo [ndi a iwo ansembe akulu] anakulirabe. 24Ndipo Pilato anaweruza kuti chimene iwo akupempha chichitike. 25Ndipo anamasula iye amene, anaponyedwa mu ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu, amene iwo anamupempha, ndipo Yesu anaperekedwa monga mwa chifuniro chawo.
26Ndipo pamene amapita naye, anagwira munthu wina Simoni, waku Kurene, amene amachokera kumunda, ndipo anamusenzetsa mtanda pambuyo pa Yesu. 27Ndipo khamu lalikulu la anthu, ndi akazi omwe amene analira nadziguguda pa chifukwa anamtsatira Iye. 28Ndipo Yesu anatembenukira kwa iwo nanena. Ana akazi a Yerusalemu, musandililire Ine, koma muzililire nokha ndi ana anu; 29pakuti taonani, masiku akubwera pamene iwo adzanena, Wodala [ali] iwo osabereka, ndi mimba zawo zosaima, ndi mabele amene sanayamwitseko. 30Pamenepo adzayamba kulankhula kwa mapiri, Tigwereni ife; ndi kuzitunda, Tibiseni ife: 31pakuti ngati izi achitira mtengo wauwisi, nanga wouma adzauchitira chiyani? 32Tsopano amuna ena awiri, anatengedwa naye pamodzi kupita kukaphedwa.
33Ndipo pamene iwo anafika pa malo otchedwa Bade, kumeneko iwo anampachika Iye, ndipo amunawo, wina kudzanja lamanja ndi wina lamanzere. 34Ndipo Yesu anati, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo, anagawana zovala zake, nachita maere. 35Ndipo anthu anayimilira akuona, ndipo akulunso [anali nawo] namnyoza, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutsenso yekha ngati ndiye Khristu wosankhidwa wa Mulungu1. 36Ndipo asilikalinso anasewera naye, nafika nampatsa Iye vinyo wosasa, 37ndi kunena, Ngati ndiwe mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha. 38Ndipo panalinso lembo [lolembedwa] pamwamba pake mau a m’Chigiriki, ndi Chiroma, ndi Chiheberi: uyu ndiye Mfumu ya Ayuda.
39Tsopano m’modzi wa amunawo amene anapachikidwa naye analankhula momunyoza Iye, nanena, Kodi siwe Khristu? Udzipulumutse wekha ndi ife. 40Koma winayo poyankha anamdzudzula iye, nanena, Kodi iwe suopa Mulungu2, kuti tili m’chiweruzo chofanana? 41ndipo ife tikufunika chilungamo, pakuti tikulandira chilungamo cha kubwezera kwa zimene ife tinachita; koma [munthu] uyu sanachite kanthu kolakwa. 42Ndipo iye anati kwa Yesu, Mundikumbukire ine, [Ambuye], pamene mudzafika mu ufumu wanu. 43Ndipo Yesu anati kwa iye, Zoonadi ndinena kwa iwe, Lero lomwe lino udzakhala ndi Ine m’paradiso.
44Ndipo linali ngati ola lachisanu ndi chimodzi, ndipo panachita mdima padziko lonse kufikira ola lachisanu ndi chinayi. 45Ndipo dzuwa linadetsedwa, ndi chinsalu cha mkachisi chinang’ambika pakati. 46Ndipo Yesu, analira ndi mau okweza, nanena, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo atalankhula izi, anamwalira.
47Tsopano kenturiyo, powona zimene zinachitikazo, analemekeza Mulungu3, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama. 48Ndipo makamu onse amene anabwera pamodzi kuzapenya izi, poona zinthu zimene zinachitika, anabwerera, nadziguguda pa chifukwa [chawo]. 49Ndipo onse amene anamdziwa Iye anayima patali, akazinso amene anamtsatira Iye kuchokera ku Galileya, anaona zinthu zimenezi.
50Ndipo taonani, munthu wotchedwa Yosefe, amene anali mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama 51([munthu] amene sanagwirizane ndi maweruzidwe awo komanso zochita zawo), wa ku Arimateya, mzinda wa Ayuda, amenenso amadikilira, ufumu wa Mulungu4 52— iye anapita kwa Pilato kukapempha thupi la Yesu; 53ndipo analitsitsa, nalikulunga mu nsalu ya bafuta ndipo anamuika Iye m’manda a mwala wosema, m’mene sanaikemo wina aliyense. 54Ndipo linali tsiku lozikonzekeretsa. Ndipo tsiku la sabata linali kubwera. 55Ndipo akazi, amene anabwera pamodzi ndi Iye kuchokera ku Galileya, anamutsatira, naona manda wosemawo ndi momwe thupi lake linaikidwira. 56Ndipo anabwerera iwo nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino, ndipo anakhala chete pa sabata, molingana ndi lamulo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu