Mutu 18

1Ndipo Iye akalankhulanso fanizo kwa iwo ndi cholinga chakuti azipemphera nthawi zonse osafooka, 2nanena, Panali woweruza mu mzinda wina, amene anali wosaopa Mulungu1 ndipo samasamala za munthu: 3ndipo panali mkazi wa masiye mu mzinda womwewo, ndipo anabwera kwa iye, nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana ndi ine. 4Ndipo iye sanachite ichi pakutha nthawi; koma pambuyo pake anati mwa iye yekha, Ngakhale kuti sindiopa Mulungu2 ndi kusasamala za munthu, 5mwa mtundu uliwonse chifukwa cha mkazi wa masiyeyu kundivuta ine ndidzamuweruzira mlandu wake, kuti asamabwere mowirikiza kundivuta ine. 6Ndipo Ambuye anati, Tamverani zimene anachita woweruza wosalungama uyu zikulankhula. 7Ndipo kodi Mulungu3 sadzaweruzira wosankhika ake, amene adzalira kwa Iye usana ndi usiku, ndipo aleza nawo mtima? 8Inetu ndinena kwa inu kuti Iye adzawaweruzira iwo mwachangu. Koma pamene Mwana wa munthu adzabwera, kodi adzapeza chikhulupiliro padziko lapansi?

9Ndipo Iye analankhulanso kwa ena, amene amadzikhulupilira okha kuti anali olungama ndi kupeputsa [anthu] ena onse, fanizo limeneli: 10Anthu awiri analowa m’kachisi kukapemphera; wina anali Mfalisi, ndi wina wokhometsa msonkho. 11Mfalisi, poyimilira. Anapemphera mwa iye yekha: Mulungu4, ine ndikuyamikani kuti sindili ngati anthu ena onse, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso ngati wamsonkho uyu. 12Ndimasala kudya kawiri pa sabata, ndimapereka chakhumi pa zonse zimene ndimapeza. 13Ndipo wokhometsa msonkhoyu, pakuyima patali, sanathe kukweza maso ake kumwamba, koma anaziguguda pachifuwa, nanena Mulungu5, ndichitireni ine chifundo, munthu wochimwa. 14Ndinena kwa inu, [Munthu] uyu anapita kwawo wolungamitsidwa kusiyana ndi [winayu]. Pakuti aliyense wodzikweza yekha adzatsitsidwa, ndipo iye wodzichepetsa adzakwezedwa.

15Ndipo iwo anamubweretseranso Iye ana kuti awakhudze, koma pamene ophunzira anaona [ichi] anawadzudzula iwo. 16Koma Yesu powaitana iwo anati, Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse iwo, pakuti mwa otere muli ufumu wa Mulungu6. 17Zoonadi ndinena kwa inu, Amene sadzalandira ufumu wa Mulungu7 ngati mwana wamng’ono sadzalowa m’menemo.

18Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye nati, Mphunzitsi wabwino, ndichite chiyani kuti ndikalowe moyo wosatha? 19Koma Yesu anati kwa iye, Chifukwa chiyani unditchula ine wabwino? Palibe wabwino koma m’modzi ndiye, Mulungu8. 20Udziwa malamulo: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachitire umboni wonama, lemekeza atate wako ndi amako. 21Ndipo iye anati, Zinthu zonse izi ndakhala ndikuzisunga kuyambira ndili mwana. 22Ndipo pamene Yesu anamva izi, anati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowekabe kwa iwe: Ugulitse zonse zimene uli nazo ndipo ugawire kwa osauka, ndipo udzakhala nacho chuma m’mwamba, ndipo ubwere, nunditsate ine. 23Koma pamene iye anamva izi anali ndi chisoni, pakuti iye anali wolemera kwambiri. 24Koma pamene Yesu anaona kuti anali ndi chisoni chachikulu, anati, Nkovuta nanga kwa iwo amene ali ndi chuma kulowa mu ufumu wa Mulungu9; 25pakuti ndi kwapafupi ngamila kulowa pa bowo la singano kusiyana ndi munthu wolemera kulowa mu ufumu wa Mulungu10. 26Ndipo iwo amene anamva izi anati, Nanga ndani amene akhoza kupulumutsidwa? 27Koma Iye anati, Zinthu zimene zili zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu11. 28Ndipo Petro anati, Taonani, ife tasiya zinthu zonse ndipo takutsatani inu. 29Ndipo Iye anati kwa iwo, Zoonadi ndinena kwa inu, Palibe amene amasiya khomo, kapena makolo, kapena abale, kapena mkazi, kapena ana, chifukwa cha ufumu wa Mulungu12, 30amene sadzalandira zobwezera zochuluka nthawi imeneyi, ndi nthawi ili mkudza moyo wosatha.

31Ndipo Iye anatenga khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, Taonani, tikwera kupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zinalembedwa za Mwana wa munthu ndi aneneri zidzakwaniritsidwa; 32pakuti Iye adzaperekedwa kwa amitundu, ndipo adzachitidwa chipongwe, ndi kunyozedwa, ndi kumlavulira. 33Ndipo pamene adzamkwapula [iye] adzamupha; ndipo patsiku lachitatu adzaukanso kwa akufa. 34Ndipo iwo sanamvetse kalikonse pa zinthu zonse izi. Ndipo mau awa anabisidwa kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene chinanenedwacho.

35Ndipo kunachitika kuti pamene Iye analowa m’mudzi wa Yeriko, munthu wina wakhungu anakhala mphepete mwanjira kupempha. 36Ndipo pamene anamva khamu likudutsa, iye anafuna kudziwa kuti chimachitika ndi chiyani. 37Ndipo anamuuza iye kuti Yesu Mnazarayo amadutsa. 38Ndipo iye anayitana nati, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo. 39Ndipo iwo [amene anali] kupitapo anamdzudzula kuti akhale chete; koma iye anafuulabe kwambiri, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo ine. 40Ndipo Yesu anayima, ndi kulamula kuti abwere naye kwa Iye. Ndipo pamene anafika pafupi amafunsa iye [nati], 41Kodi ndikuchitire chiyani iwe? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenye. 42Ndipo Yesu anati kwa iye, Tapenya: chikhulupiliro chako chakuchiritsa iwe. 43Ndipo nthawi yomweyo iye anapenya, ndipo anamtsata Iye, nalemekeza Mulungu13. Ndipo anthu onse pamene anaona [ichi] anapereka mayamiko kwa Mulungu14.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu