Mutu 10

1Ndipo pamene anadziitanira kwa [Iye] ophunzira ake khumi ndi awiri, anawapatsa mphamvu pa mizimu yoipa, cholinga kuti akaitulutse, ndi kuchilitsa nthenda zonse ndi kufooka kulikonse kwa mthupi. 2Tsopano maina a atumwi khumi ndi awiriwo ali motere: woyamba, Simoni, amene amatchedwanso Petro, ndi Andreya m’bale wake; Yakobo [mwana] wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake; 3Filipo ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wokhometsa msonkho; Yakobo [mwana] wa Alifeyo, ndi Lebausi, amene amatchedwanso Tadeyo; 4Simoni Mkanani, ndi Yudasi Isikariote, amene anampereka Iye.

5Khumi ndi awiri amenewa Yesu anawatuma iwo pamene anawalangiza, nanena, Musapite ku njira ya amitundu, ndi ku mizinda ya Asamariya musamalowamo; 6koma m’malo mwake pitani kwa nkhosa zosochera za ku Israyeli. 7Ndipo mukapita, lalikirani, munene, Ufumu wa Mulungu wayandikira. 8Chiritsani odwala, [ukitsani akufa], konzani a khate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, perekaninso kwaulere. 9Musadzitengere nokha golide, kapena siliva, kapena makobili m’malamba mwanu, 10kapena thumba la kamba la panjira panu, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo: pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake. 11Komatu mzinda ulionse ndi mudzi ulionse umene mukalowa, fufuzani amene ali woyenera m’menemo, ndipo khalani momwemo kufikira mutachokako. 12Ndipo pamene mulowa m’nyumba alankhuleni a m’nyumbamo. 13Ndipo nyumbayo ikakhaladi yoyenera, mtendere wanu ukhale pa iyo; koma ngati sili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14Ndipo amene sazalandira inu, kapena kumva mau anu, pamene mutuluka m’nyumbamo kapena mu mzindawo sasani fumbi la kumapazi kwanu. 15Indetu ndinena kwa inu, tsiku la kuweruza mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi mlandu wa mzindawu. 16Taonani, ine ndikutumizani inu ngati nkhosa pakati pa mimbulu; khalani inu ochenjera ngati njoka, ndi owona mtima ngati nkhunda. 17Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani kwa akulu a milandu, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge mwao; 18ndipo adzakutengerani pamaso pa wolamula ndi mafumu chifukwa cha ine, chifukwa cha umboni wa kwa iwo komanso kwa amitundu. 19Komatu akakuperekani inu, musadandaule kuti mudzalankhula bwanji komanso mudzalankhula chiyani; pakuti chidzapatsidwa kwa inu cholankhula pa nthawi imeneyo. 20Pakuti inu sindinu wolankhula, koma Mzimu wa Atate wanu umene umalankhula mwa inu. 21Koma m’bale adzapereka m’bale wake ku imfa, ndipo atate kupereka mwana; ndipo ana adzaukira makolo ndipo adzawapha; 22ndipo adzakudani anthu onse chifukwa cha dzina langa. Koma iye amene adzapilira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumuka. 23Koma akakuzunzani inu mu mzinda uwu, thawirani ku mzinda wina; pakuti indetu ndinena kwa inu, simudzamaliza mizinda ya mu Israyeli kufikira Mwana wa munthu atabwera. 24Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo kuposa mbuye wake. 25Kumkwanira wophunzira kukhala ngati mphunzitsi wake, ndi kapolo kukhala ngati mbuye wake. Ngati anamutchula mwini nyumba Belezebule, nanga koposa kotani iwo a m’nyumba mwake? 26Kotero musawaope; pakuti palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndiponso chinsinsi chimene sichidzadziwika. 27Chimene ndilankhula kwa inu mumdima chilankhuleni powala, ndipo chimene muchimva m’khutu chilalikireni m’manyumba. 28Ndipo musachite mantha ndi iwo akupha thupi, koma sangathe kupha moyo; komatu muope Iye amene angathe kuononga moyo ndi thupi m’gehena. 29Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo palibe imodzi mwa izo idzagwa pansi popanda Atate wanu; 30komatu za inu ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu lawerengedwa lonse. 31Kotero musaope; inutu muli oposera mpheta zambiri. 32Aliyense amene adzandivomereza ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate wanga amene ali m’mwamba. 33Komatu amene adzandikana ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga amene ali m’mwamba. 34Musaganize kuti ndabwera kudzapereka mtendere padziko lapansi: sindinabwere kudzapereka mtendere, koma lupanga. 35Pakuti ndadza kudzasiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi mai ake, komanso mkazi wokwatiwa ndi apongozi ake akazi; 36ndipo a pabanja pake pa munthu [adzakhala] adani ake. 37Iye wakukonda atate kapena amake koposa Ine sali woyenera Ine. 38Ndipo iye amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sali woyenera Ine. 39Iye amene apeza moyo wake adzautaya, ndipo amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzaupeza. 40Iye amene walandira inu walandira Ine, ndipo amene walandira Ine walandira Iye amene anandituma Ine. 41Iye amene alandira mneneri mdzina la mneneri, adzalandira mphoto ya mneneri; ndipo iye amene adzalandira munthu wolungama, adzalandira mphoto ya munthu wolungama. 42Ndipo iye amene adzapereka [madzi] okha ozizira kwa m’modzi wa ana awa, m’dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphoto yake.