Mutu

1Mkuluyo kwa Gayo wokondedwa, amene ndimkonda m’choonadi.

2Wokondewa, ndifunitsitsa kuti mu zinthu zonse uchite bwino ndiponso mu thanzi lako, monga umo upambanira moyo wako. 3Pakuti ndinakondwera koposa pamene abale anabwera ndi kuchitira umboni kugwiritsitsa kwako choonadi, monga umo uyendera m’choonadi. 4Ndilibe chimwemwe choposa zinthu izi kumva kuti ana anga akuyenda m’choonadi. 5Wokondedwa, ukuchita mokhulupirika chilichonse chimene ukuchitira abale ndi alendo, 6(amene anachitira umboni za chikondi chako pamaso pa mpingo,) powaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu2, udzachita bwino; 7pakuti padzina limeneli anapita, osatenga kanthu ka iwo amitundu. 8Ife pamenepo tinafuna kulandira otere, kuti tikakhale ogwira ntchito pamodzi ndi choonadi. 9Ndinalemba kanthu kena ku mpingo; koma Diotrefe, amene anakonda kukhala wopambana pakati pawo, sanatilandire ife. 10Pachifukwa chimenechi, ngati ndibwera, ndidzamkumbutsa ntchito zake zimene anachita, polankhula motsutsana nafe ndi mau amwano; ndipo posakwanitsidwa ndi izi, sanalandire abale iye yekha; ndi iwo ofuna kutero anawaletsa, ndi kuwatulutsa mu mpingo. 11Wokondedwa usatengere chimene chili choipa, koma chabwino. Iye amene amachita chabwino ali wa Mulungu2. Iye wakuchita choipa sanaone Mulungu3. 12Demetriyo umboni wachitidwa kwa iye ndi onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichitira umboni, ndipo inu mudziwa kuti umboni wathu uli woona.

13Ndinali nazo zinthu zambiri zakulembera iwe, koma sinditero ndi kapezi ndi cholembera; 14koma ndiyembekezera kukuona iwe posachedwapa, ndipo tidzalankhulana kamwa ndi kamwa. [Mtendere] ukhale kwa iwe. Abale akulonjera iwe. Uwalonjere abalewo powatchula maina awo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu