Mutu 9
1Koma Saulo, wosaleka kupumira kuopseza ndi kupha ophunzira a Ambuye, anabwera kwa mkulu wa nsembe 2ndipo anamupempha iye makalata opita ku Damasiko, ku masunagoge, kuti iye akapeza aliyense panjira onse amuna ndi akazi omwe, awabweretse ali omangidwa ku Yerusalemu. 3Koma pamene amayenda, kunachitika kuti anafika kufupi ndi Damasiko; ndipo mwadzidzidzi kunawala momzungulira iye kuwala kochokera kumwamba, 4ndipo anagwa pansi iye namva mau akulankhula kwa iye, Saulo, Saulo, undizunziranji Ine? 5Ndipo iye anati, Ndinu ndani, Ambuye? Ndipo Iye [anati], Ndine Yesu, amene iwe ukumzunzayo. 6Koma tadzuka ndipo ulowe mu mzinda, ndipo udzauzidwa choyenera kuchita. 7Koma anthu amene anali naye pamodzi anayima kusowa cholankhula, pakumva mau koma osaona munthu wina aliyense. 8Ndipo Saulo anayimilira kuchoka pansi, ndipo maso ake ali otseguka koma osapenya kanthu. Koma pomutsogolera [iye] padzanja anamtengera iwo ku Damasiko. 9Ndipo anatha masiku atatu ali wosaona, ndipo sanadye kapena kumwa. 10Ndipo panali wophunzira wina mu Damasiko dzina lake Hananiya. Ndipo Ambuye analankhula naye m’masomphenya, Hananiya. Ndipo iye anati, Taonani, [ndili pano] ine, Ambuye . 11Ndipo Ambuye [anati] kwa iye, Tauka upite mu msewu umene umatchedwa Wolunjika, ndipo ukafufuze mnyumba mwa Yuda munthu dzina lake Saulo, waku Taruso: pakuti, taona, iye akupemphera, 12ndipo waona [m’masomphenya] munthu dzina lake Hananiya akulowa ndi kuyika dzanja lake pa iye, kuti apenye. 13Ndipo Hananiya anayankha, Ambuye, ndamva kuchokera kwa anthu ochuluka zokhudza munthu ameneyu zoipa zambiri wakhala akuchita kwa oyera mtima anu aku Yerusalemu; 14ndipo pano ali ndi ulamuliro wochokera kwa akulu ansembe kumanga onse oyitanira pa dzina lanu. 15Ndipo Ambuye anati kwa iye, Pita, pakuti [munthu] uyu ndi chida changa chosankhika kwa ine, kuchitira umboni dzina langa pamaso pa mitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli: 16pakuti Ine ndimuonetsera iye momwe azunzikire chifukwa cha dzina langa. 17Ndipo Hananiya anapita nalowa mnyumbamo; ndipo pamene anasanjika manja ake pa iye anati, Saulo, m’bale, Ambuye wandituma ine, Yesu amene anaonekera kwa iwe mnjira imene wabwerera kuno, kuti upenyenso, ndi kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera. 18Ndipo nthawi yomweyo munagwa m’maso mwake ngati mamba, ndipo anapenya, ndipo anauka nabatizidwa; 19ndipo, pamene analandira chakudya, anapeza mphamvu. Ndipo anali pamodzi ndi ophunzira amene [anali] mu Damasiko masiku ena. 20Ndipo nthawi yomweyo mu sunagoge analalikira Yesu kuti anali Mwana wa Mulungu1. 21Ndipo onse amene anamva anali odabwa ndipo anati, Kodi uyu siuja anaononga mu Yerusalemu iwo amene amaitanira pa dzina limeneli, ndipo pano wabwera pa cholinga chomwechi, kuti akawatengere iwo omangidwa kwa akulu ansembe?
22Koma Saulo anachulukirabe mu mphamvu, ndipo anadodometsa Ayuda amene amakhalira mu Damasiko, kutsimikizira kuti uyu ndi Khristu. 23Tsopano pamene masiku anakwaniritsidwa, Ayuda anagwirizana pamodzi kuti amuphe iye. 24Koma chiwembu chawo chinadziwika kwa Paulo. Ndipo iwo anayang’aniranso pa zipata masana ndi usiku omwe, kuti akamuphe iye; 25koma ophunzira anamutenga iye usiku ndipo anamutsitsira pa chipupa, namtsitsira ndi dengu.
26Ndipo pakufika ku Yerusalemu anadziphatika yekha kwa ophunzira, ndipo onse anachita naye mantha, osakhulupilira kuti iye anali ophunzira. 27Koma Barnaba anamtenga nam’bweretsa iye kwa atumwi, ndipo anawafotokozera iwo m’mene anakumanirana ndi Ambuye panjira, ndi kuti analankhula kwa iye, ndi momwe ku Damasiko analankhulira molimba mtima m’dzina la Yesu. 28ndipo iye anali nawo pamodzi polowa ndi potuluka ku Yerusalemu, 29ndi polankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye. Ndipo iye analankhula ndi kukambirana ndi Aheleniste; koma iwo anafuna kumupha iye. 30Ndipo abale podziwa ichi, anam’bweretsa ku Kaisareya namtumiza ku Tariso. 31Pamenepo mipingo yonse yozungulira Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya inali pa mtendere, polimbikitsidwa ndi kuyenda m’kuopa kwa Ambuye, ndipo anachulukitsidwa kudzera mu chitonthonzo cha Mzimu Woyera.
32Tsopano kunachitika kuti Petro, pakudutsa ku [madera] onse, anatsikiranso kwa oyera mtima amene amakhala ku Luda. 33Ndipo iye anapeza munthu wina, dzina lake Eneya, amene anagona pa mphasa kwa zaka zisanu ndi zitatu, anali wakufa ziwalo. 34Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu, akuchiritse iwe: tauka, nuyalule mphasa yako. Ndipo nthawi yomweyo anauka. 35Ndipo onse okhala ku Luda ndi ku Sarona anamuona iye, amene anatembenukira kwa Ambuye.
36Ndipo m’Yopa munali wophunzira wina wa mkazi, dzina lake Tabita, limene potanthauzira ndi Dorika. Iye anali wodzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita. 37Ndipo kunachitika mu nthawi imeneyo kuti iye anadwala namwalira; ndipoi, atamusambitsa, anamuyika m’chipinda chapamwamba. 38Koma Luda pokhala pafupi ndi Yopa, ophunzira pakumva kuti Petro anali kumeneko, anamtumizira amuna awiri kwa iye, kumudandaulira iye, Musachedwe kupita nafe. 39Ndipo Petro anauka napita nawo, pamene anafika, anamtengera m’chipinda chapamwamba; ndipo akazi onse amasiye anayima naye pamodzi akulira namuonetsa zovala ndi nsalu zimene Dorika anawasokera pamene anali pamodzi ndi iwo. 40Koma Petro, pamene anawatulutsa panja, anagwada pansi, napemphera. Ndipo anatembenukira ku mtembowo nati, Tabita, uka. Ndipo iye anatsegula maso ake, ndipo atamuona Petro anakhala tsonga. 41Ndipo anamgwira dzanja lake, namnyamutsa, ndipo anayitana oyera mtima ndi akazi amasiye, nampereka iye wamoyo. 42Ndipo zinadziwika ku Yopa yense, ndipo ambiri anakhulupilira pa Ambuye. 43Ndipo kunachitika kuti iye anakhalabe masiku ambiri ku Yopa ndi munthu wina Simoni, wofufuta zikopa.
1Elohimu