Mutu 4

1Khristu, pamenepo, atazunzika mthupi chifukwa cha ife, kodi mukudzikonzekeretsanso nokha ndi malingaliro omwewa; pakuti iye amene wavutika m’thupi wathana nalo tchimo, 2sakhalanso mu nthawi yotsalirayo ya m’thupi ku zilakolako zoipa, koma ku chifuniro cha Mulungu1. 3Pakuti nthawi yapitayi inali yokwanira kwa ife kukachita chifuniro cha Amitundu, kuyenda m’chisembwere, m’zilakolako zoipa, kumwa kachaso, mapwando, kuledzera, ndi kupembedza mafano kosaloleka. 4M’menemo iwo aganiza kuti n’chachilendo kuti inu simuthamanga nawo pamodzi m’chitsime chomwecho cha zoipa, nalankhula moipa zokhudza inu; 5amene azafotokozera kwa iye amene ali wokonzeka kuweruza anthu amoyo ndi akufa. 6Pakuti chifukwa cha ichi uthenga wabwino ulalikidwa kwa akufanso, kuti akaweruzidwe, monga anthu, anakhalako m’thupi, koma nakhala ndi moyo, molingana ndi Mulungu2, motsata Mzimu. 7Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chawandikira: pamenepo khalani maso, ndi kupenyerera m’mapempherero; 8koma koposa zinthu zonse kukhala nacho chikondi pakati panu, chifukwa chikondi chimakwilira unyinji wa machimo; 9kusamalirana wina ndi mnzake, popanda kunyinyirika; 10aliyense molingana ndi kulandira kwa mphatso ali nayo, kutumikirana wina ndi mzake, monga oyang’anira abwino a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu3. 11Ngati wina alankhula — alankhule monga mwa mau a Mulungu4; ngati wina atumikira — atumikire monga mwa mphamvu imene Mulungu5 amapereka; kuti Mulungu6 mu zinthu zonse alemekezeke mwa Yesu Khristu, kwa iye amene ali ndi ulemelero ndi mphamvu ya nthawi za nthawi. Amen.

12Okondedwa, musayese cha chilendo moto [wa chizunzo] umene wachitika pakati panu, pa mayesero anu, ngati kuti chinthu cha chilendo chikuchitika kwa inu; 13koma monga mwagawana m’mazunzo a Khristu, kondwerani, kuti m’chivumbulutso cha ulemelero kutinso mukakondwere ndi chimwemwe chachikulu. 14Ngati mudzudzulidwa m’dzina la Khristu, ndinu odala; pakuti [Mzimu] wa ulemelero ndi Mzimu wa Mulungu7 upumulira pa inu: [ku mbali yawo iye anenedwa mwano, koma ku mbali yanu iye alemekezedwa.] 15Wina wa inu asavutikedi ngati wa mbanda, kapena wakuba, kapena wochita choipa, kapena woyang’anira wa zochitika za anthu ena; 16koma monga ngati mkhristu, asachititsidwe manyazi, koma alemekeze Mulungu8 m’dzina limeneli. 17Pakuti nthawi yolandira chiweruzo choyambira m’nyumba ya Mulungu9 [yafika]; koma ngati chiyamba ndi ife, nanga chitsiriziro cha iwo osamvera uthenga wabwino wa Mulungu10 chidzakhala chotani? 18Ndipo ngati wolungama apulumutsidwa movutikira, nanga munthu wosapembedza ndi wochimwa zidzakhala bwanji? 19Pameneponso iwo amene akuvutika molingana ndi chifuniro cha Mulungu11 apereka miyoyo yawo pakuchita zabwino kwa Mlengi wokhulupirika.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu