Mutu 1
1Buku la m’badwo wa Yesu Khristu, Mwana wa Davide, Mwana wa Abrahamu.
2Abrahamu anabereka Isake; ndipo Isake anabereka Yakobo, ndipo Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake; 3ndipo Yuda anabereka Farese ndi Zara mwa Tamare; ndipo Farese anabereka Ezromu, ndipo Ezromu anabereka Aramu, 4ndipo Aramu anabereka Aminadabu, ndipo Aminadabu anabereka Naasoni, ndipo Naasoni anabereka Salimoni, 5?ndipo Salimoni anabereka Boazi mwa Rahabe; ndipo Boazi anabereka Obedi mwa Rute; ndipo Obedi anabereka Jese, 6?ndipo Jese anabereka Davide mfumuyo. Ndipo Davide anabereka Solomoni, mwa iye [amene anali mkazi] wa Uriya; 7ndipo Solomoni anabereka Roboamu, ndipo Roboamu anabereka Abiya, ndipo Abiya anabereka Asa, 8?ndipo Asa anabereka Yosafate, ndipo Yosafate anabereka Yoramu, ndipo Yoramu anabereka Uziya, 9?ndipo Uziya anabereka Yotamu, ndipo Yotamu anabereka Ahazi, ndipo Ahazi anabereka Hezekiya, 10?ndipo Hezekiya anabereka Manase, ndipo Manase anabereka Amoni, ndipo Amoni anabereka Yosiya, 11?ndipo Yosiya anabereka Yekoniya ndi abale ake, pa nthawi imene anatengedwa kupita ku Babulo. 12Ndipo pambuyo pake pamene anatengedwa kupita ku Babulo, Yekoniya anabereka Salatieli, ndipo Salatieli anabereka Zerubabele, 13ndipo Zerubabele anabereka Abiyudi, ndipo Abiyudi anabereka Eliyakimu, ndipo Eliyakimu anabereka Azoro, 14ndipo Azoro anabereka Sadoki, ndipo Sadoki anabereka Akimu, ndipo Akimu anabereka Eliyudi, 15ndipo Eliyudi anabereka Eliezara, ndipo Eliezara anabereka Matani, ndipo Matani anabereka Yakobo, 16ndipo Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wake wa Mariya, amene mwa iye munabadwa Yesu, wotchedwa Khristu.
17Kotero mibadwo yonse, kuyambira pa Abrahamu kufika pa Davide [inalipo] mibadwo khumi ndi inayi; ndipo kuyambira pa Davide kufika pamene anatengedwa kupita ku Babulo, mibadwo khumi ndi inayi.
18Tsopano kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Mayi wake, Mariya, atatomeredwa ndi Yosefe, koma asanakomane malo amodzi, anapezeka kuti ali ndi mwana [mwa] Mzimu Woyera. 19Koma Yosefe, mwamuna wake, pokhala kuti anali munthu wolungama, ndipo sanafune kumuchititsa iye manyazi poyera, analingalira zofuna kumusiya m’tseri; 20koma pamene amalingalira izi, taonani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m’maloto, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kuzitengera [wekha] Mariya, mkazi wako, pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili [cha] Mzimu Woyera. 21Ndipo adzabereka mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, pakuti Iye adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo. 22Tsopano izi zonse zinachitika kuti zikwaniritsidwe zimene zinanenedwa ndi Ambuye, kudzera mwa mneneri, kunena kuti, 23Taonani, namwali adzakhala ndi mwana, ndipo adzamutcha dzina lake Emanueli, limene limatanthauza kuti, 'Mulungu nafe.' 24Komatu Yosefe, atauka kutulo take, anachita monga zimene mngelo wa Mulungu anamulamulira iye, ndipo anadzitengera [yekha] mkazi wake, 25ndipo sanamdziwa iye kufikira atabereka mwana wake woyamba wa mwamuna: ndipo anamutcha dzina lake Yesu.