Mutu 12

1Pa nthawi imeneyo Herode mfumuyo inagwira ena mwa a m’Eklesia kuti awachitire zoipa, 2ndipo anamupha Yakobo, m’bale wake wa Yohane, ndi lupanga. 3Ndipo poona kuti zinasangalatsa Ayuda, iye anapita kukamugwiranso Petro: (ndipo anali masiku a mkate wopanda chotupitsa:) 4ndipo pamene anamugwira iye anamponya m’ndende, ndipo anampereka iye kwa magulu anayi a asilikali, okhalanso anayi anayi kuti amusunge, anakonza kuti pakutha pa pasaka amtulutse iye kwa anthu. 5Pamenepo Petro anasungidwa m’ndende; koma mapemphero osaleka okhudza iye anachitika ndi mpingo wa Mulungu1. 6Ndipo pamene Herode amakonza zomubweretsa, usiku umenewo Petro anagona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri, ndipo alonda anayima pakhomo kuyang’anira ndendeyo. 7Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anabwera pamenepo, ndipo kuwala kunaoneka m’ndende: ndipo anamumenya Petro mu mthiti, namuutsa iye, nanena, tauka mwachangu. Ndipo maunyolo ake anagwa kudzanja kwake. 8Ndipo mngelo anati kwa iye, Udzimagire wekha mchuuno, ndi kumanga nkhwayira zako. Ndipo iye anachita izi. Ndipo anati kwa iye, Vala chovala chapamwamba ndipo unditsate ine. 9Ndipo anatuluka namtsata [iye] ndipo sanazindikire chimene chimachitika ndi mngelo kuti chinalidi chenicheni, koma anayesa kuti akuona masomphenya. 10Ndipo atamudutsa londa woyamba ndi wachiwiri, iwo anafika pa chipata cha chitsulo cholowera mu mzindawo, chimene chinatsegukira iwo pachokha; ndipo popita anatsikira pa msewu wina, ndipo nthawi yomweyo mngelo anamsiya iye. 11Ndipo Petro, potsitsimuka mwini yekha, anati, Tsopano ndazindikira kuti Ambuye watumiza mngelo wake ndipo wandichotsa ine m’dzanja la Herode ndi chilingiliro chonse cha anthu Achiyuda. 12Ndipo atatsitsimuka bwinobwino [mwa iye yekha], anafika kunyumba ya Mariya, mayi wake a Yohane amenenso amatchedwa Marko, kumene anthu ochuluka anasonkhana pamodzi ndi kupemphera. 13Ndipo atagogoda pachitseko cha pakhomo polowera, anabwera mtsikana wantchito kudzaona, dzina lake Roda; 14ndipo atazindikira mau a Petro, chifukwa cha chimwemwe sanatsegule chitseko, koma anathamangira mkati, napereka uthenga kuti Petro wayima pakhomo. 15Ndipo iwo anati kwa iye, Wapenga iwe. Koma iye anatsimikizira iwo kuti zinali choncho ndithu. Ndipo iwo anati, Ameneyo ndi mngelo. 16Koma Petro anapitilizabe kugogoda: ndipo atatsegula, iwo anamuonadi iye ndipo anali odabwa. 17Ndipo ataonetsa chizindikiro ndi chala chake kuti akhale chete, anawafotokozera [iwo] m’mene Ambuye anamtulutsira iye mndende; ndipo anati, Kawuzeni zinthu izi Yakobo ndi abale. Ndipo anatuluka napita kumalo ena. 18Ndipo pamene kunacha m’mawa panali chisokonekero pakati pa asilikali, nanga chachitika ndi chiyani kwa Petro. 19Ndipo Herode anamufunafuna iye ndipo sanamupeze, ndipo atawafufuza alonda, analamulidwa kuti anyongedwe. Ndipo iye anatsikira kuchoka ku Yudeya kupita ku Kaisareya ndipo anakhala [kumeneko]. 20Ndipo Herode anapsa nawo mtima aku Turo ndi Sidoni; koma iwo anabwera kwa iye ndi mtima umodzi, ndipo m’mene anakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, chifukwa dzikolo limadyetsedwa ndi mfumuyo. 21Ndipo pa tsiku loikika, anavala zovala za chifumu nakhala pa mpando wa chifumu [wa ulemu] nawafotokozera mau poyera. 22Ndipo anthu anafuula, Mau a mulungu2 awa si amunthu. 23Ndipo nthawi yomweyo mngelo wa Ambuye anamkantha iye, chifukwa sanapereke ulemelero kwa Mulungu3, ndipo iye anafa, nadyedwa ndi mphutsi. 24Koma mau a Mulungu4 anakulabe nafalikira pa iwo okha. 25Ndipo Barnaba ndi Saulo anabwerera kuchoka ku Yerusalemu, atakwaniritsa utumiki [woyikidwa mwa iwo], ndipo anamutenganso Yohane, wotchedwanso Marko.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu