Mutu 6

1Ndipo kunachitika kuti tsiku loyamba la sabata, Iye anali kuyenda pakati pa minda, ndipo ophunzira ake anali kubudula ngala za tirigu ndi kumadya pozitikitira m’manja mwawo. 2Komatu ena mwa Afarisi anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukuchita chosayenera pa tsiku la sabata? 3Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Kodi simunawerenge zoposera izi, zimene anachita Davide pamene anamva njala, iye pamodzi ndi iwo amene anali naye, 4momwe iye analowera m’nyumba ya Mulungu1 natenga mikate yoonetsera ndi kudya, naperekanso kwa iwo amene anali naye, chimene chinali chosaloledwa kuti [aliyense] adye, kupatula wansembe yekha? 5Ndipo Iye anati kwa iwo, Mwana wa Mulungu ndiyenso Ambuye wa sabata.

6Ndipo kunachitikanso kuti tsiku lina la sabata Iye analowa m’sunagoge naphunzitsa; ndipo analipo munthu pamenepo, amene dzanja lake lamanja linali lopuwala. 7Ndipo alembi ndi Afarisi anapenyerera ngati Iye akhoza kuchiritsa pa sabata, kuti iwo amupezere kanthu kakuti amutsutse nako. 8Koma Iye anadziwa malingaliro awo, ndipo anati kwa munthu amene anali ndi dzanja lopuwala, Tadzuka, ndipo uyimilire pakatipa. Ndipo podzuka iye anayimilira [pamenepo]. 9Kotero Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani ngati ndi kololedwa pa sabata kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena ku uwononga [iwo]? 10Ndipo powunguzawunguza pa iwo onse, anati kwa iye, tambasula dzanja lako. Ndipo iye anachita [choncho] ndipo dzanja lake linabwerera bwino lomwe ngati limzake. 11Komatu iwo anadzala ndi mkwiyo, ndipo anayankhula pamodzi pakati pawo kuti adzachita chiyani kwa Yesu.

12Ndipo kunachitika kuti m’masiku amenewo Iye anapita ku phiri kukapemphera, ndipo Iye anachezera usiku onse mu pemphero kwa Mulungu2. 13Ndipo pamene kunacha Iye anaitana ophunzira ake, ndipo anasankha khumi ndi awiri pakati pawo, amenenso anawatcha atumwi: 14Simoni, amenenso anamupatsa dzina lakuti Petro, ndi Andreya m’bale wake, [ndi] Yakobo ndi Yohane, [ndi] Filipo ndi Bartolomeyo, 15[ndi] Mateyu ndi Tomasi, Yakobo [mwana] wa Alifeyo ndi Simoni amene anatchedwa Zelote, 16[ndi] Yuda [m’bale] wa Yakobo, ndi Yudase Iskariote, amenenso anali wompereka [Iye]; 17ndipo Iye atatsika nawo, anayima pamalo odikha, ndi khamu la ophunzira ake, komanso khamu lonse la anthu ochokera ku Yudeya ndi Yerusalemu, ndi magombe a nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anabwera kudzamumva Iye, ndi kuchiritsidwa ku nthenda zawo; 18ndi iwo amene anavutidwa ndi mizimu yoipa anachiritsidwa. 19Ndipo khamu lonse linafuna kumukhudza Iye, pakuti mphamvu inatuluka mwa Iye nichiritsa onse.

20Ndipo Iye, pokweza maso ake kwa ophunzira ake, anati, Odala muli inu amene muli osauka, pakuti wanu uli ufumu wa Mulungu3. 21Odala inu amene mukumva njala tsopano, pakuti mudzakhuta. Odala inu amene mukulira tsopano, pakuti mudzaseka. 22Odala inu pamene anthu adzakudani, ndi pamene iwo adzakupatulani inu [kwa iwo], ndi kukutonzani [inu], ndi kulitaya dzina lanu ngati loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu: 23kondwerani mu tsiku limenelo ndi kulumpha mwa chimwemwe, pakuti taonani, mphoto yanu ndi yaikulu m’mwamba, pakuti zonga zomwezi anachitanso makolo awo kuchitira aneneri. 24Komatu tsoka kwa inu olemera, pakuti mwalandira chisangalatso chanu. 25Tsoka kwa inu okhuta, pakuti mudzamva njala. Tsoka kwa inu amene mukuseka tsopano, pakuti mudzalira ndi kubuma. 26Tsoka, pamene anthu onse alankhula zabwino za inu, pakuti momwemo makolo awo anachitira aneneri onyenga. 27Komatu kwa inu amene mukumva ndinena, Kondani adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu; 28dalitsani iwo amene akutemberera inu; pemphererani iwo amene amakuchepsani. 29Kwa iye amene akumenyani pa tsaya, mpatseninso tsaya linalo; ndipo kwa iye amene atenga chofunda chako, usamkanizenso chovala chako. 30Kwa aliyense amene akupemphani inu, mpatseni; ndipo kwa iye amene akutengerani chimene chili chanu, musachiyitanitse kuti abweze. 31Ndipo monga mufuna kuti anthu akuchitireni, chitaninso inu kwa iwo motero. 32Ndipo ngati mukonda iwo akukonda inu, mwapezapo choyamikidwa chotani? Pakuti ngakhale ochimwa amakonda iwo amene awakonda. 33Ndipo ngati muchitira zabwino kwa iwo amene achitira zabwino kwa inu, mwapezapo choyamikidwa chotani? Pakuti ngakhale ochimwa amachita chimodzimodzi. 34Ndipo ngati mubwereketsa kwa iwo amene mukuyembekezera kuti mudzalandirako, mwapezapo choyamikidwa chotani? [pakuti] ngakhale ochimwa amabwereketsa kwa ochimwa amzawo kuti adzalandire chimodzimodzi. 35Komatu kondani adani anu, ndipo chitani zabwino, ndi kubwereketsa, osayembekezera kubwezeredwa kalikonse, ndipo mphoto yanu idzakhala yaikulu, ndipo mudzakhala ana a Wam’mwambayo; pakuti Iye ndi wabwino kwa anthu osayamika ndi ochimwa. 36Chomwecho khalani a chifundo, monga Atate wanunso ali wa chifundo. 37Musaweruze, ndipo simudzaweruzidwa; musamatsutse, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo chidzamasulidwa kwa inu. 38Perekani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; mlingo wabwino, wotsendereka, ndi wokhutchumuka, ndi wosefukira, zidzapatsidwa m’manja mwanu: pakuti ndi mlingo womwewo umene muyesera udzayesedwanso kwa inu.

39Ndipo Iye analankhulanso fanizo kwa iwo: Kodi [munthu] wa khungu akhoza kutsogolera [munthu] wa khungu mzake? Kodi onse sadzagwera m’dzenje? 40Wophunzira samaposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene adzakonzedwa mtima adzakhala ngati mphunzitsi wake. 41Koma chifukwa chiyani uyang’ana chitsotso chimene chili m’diso mwa m’bale wako, koma usiya mtanda umene uli m’diso mwako? 42kapena udzanena bwanji kwa m’bale wako, Ndilole [ine], ndidzachotsa chitsotso chili m’maso mwako, pamene iwe mwini sukuona mtanda umene uli m’diso mwako? Wachinyengo iwe, uyambe wachotsa mtanda uli m’diso mwako, ndipo pamenepo udzaona bwino ndi kuchotsa chitsotso chili m’diso mwa m’bale wako. 43Pakuti palibe mtengo wabwino umene umabereka chipatso choipa, kapena mtengo woipa kubereka chipatso chabwino; 44pakuti mtengo ulionse udziwika ndi zipatso zake, pakuti mkuyu sututidwa pa minga, kapena mpesa suthyoledwa ku mtungwi. 45Munthu wabwino, kuchokera mu chuma chabwino cha mumtima mwake, amatulutsa zabwino; ndipo [munthu] woipa kuchokera mu zoipa, amatulutsa choipa: pakuti kuchokera mu kuchuluka kwa mtima pakamwa pake pamalankhula. 46Ndipo chifukwa chiyani munditchula Ine, Ambuye, Ambuye, koma osachita zinthu zimene Ine ndinena? 47Aliyense wobwera kwa Ine, ndi kumva mau anga ndi kuwachita, ndidzakuonetserani amene afana naye. 48Ali ngati munthu wakumanga nyumba, nakumba kufika pansi, ndi kumanga maziko pa thanthwe; koma pakubwera mvula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunayigwedeza, pakuti inamangidwa pa thanthwe. 49Ndipo iye amene anamva koma sanachite kanthu, ali ngati munthu wakumanga nyumba pa nthaka popanda maziko, pamene mtsinje unagunda, ndipo nthawi yomweyo nyumbayo inagwa, ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu