Mutu 19
1Ndipo kunachitika kuti, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo, anadutsira ku madera akumtunda, nafika ku Efeso, ndipo anapeza ophunzira ena, 12iye anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupilira? Ndipo iwo [anati] kwa iye, Sitinamve n’komwe ngati Mzimu Woyera [anabwera]. 3Ndipo iye anati, Nanga tsopano munabatizidwa kwa ndani? Ndipo iwo anati, Ku ubatizo wa Yohane. 4Ndipo Paulo anati, Zoonadi Yohane anabatiza [ndi] ubatizo wa kulapa, kuwauza anthu kuti akhulupilire pa Iye amene amadza pambuyo pake, amene ali, Yesu. 5Ndipo pamene iwo anamva izi, anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. 6Ndipo Paulo atasanjika manja [ake] pa iwo, Mzimu Woyera anafika pa iwo, ndipo iwo analankhula m’malilime nanenera. 7Ndipo anthu onse analipo okwanira khumi ndi awiri. 8Ndipo polowa m’sunagoge, iye analankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa ndi kuwalimbikitsa [zinthu] zokhudza ufumu wa Mulungu1. 9Koma pamene ena anaumitsa mitima ndi kusakhulupilira, analankhula zoipa zokhudza njirayo pamaso pa anthu, iye anachoka pakati pawo nawalekanitsa ophunzirawo, kuwadzudzula m’sukulu za Turano. 10Ndipo zimenezi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti iwo onse amene amakhala ku Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene omwe. 11Ndipo Mulungu2 sanachite zozizwa za wamba ndi manja a Paulo, 12kotero kuti ngakhale zitambaya ndi nsalu zovala pophika zinachotsedwa pathupi pake [ndi kuyikidwa] pa odwala, ndi nthenda zinawaleka iwo, ndipo mizimu yoipa inatuluka. 13Ndipo Ayuda ena oyendayenda otulutsanso ziwanda, anadzitengera m’manja mwao kuitanira dzina la Ambuye Yesu pa iwo amene anali ndi mizimu yoipa, nanena, Ndikulamulira iwe m’dzina la Yesu, amene Paulo amalalikira. 14Ndipo analipo [anthu] ena, ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda, amene amapanga zimenezi. 15Koma mzimu woyipa poyankha unati kwa iwo, Yesu ndim’dziwa ine, ndipo Paulo ndimzindikira; koma inuyo, ndinu ndani? 16Ndipo munthu amene mwa iye munali mzimu woyipa anawadumphira iwo, ndipo anawagonjetsa onse, kotero kuti anathawa mnyumba ali maliseche ndi wovulala. 17Ndipo izi zinadziwika kwa onse, Ayuda ndi Ahelene omwe, amene amakhala ku Efeso, ndipo mantha anagwira iwo onse, ndipo dzina la Ambuye linakwezedwa. 18Ndipo ambiri mwa iwo amene anakhulupilira anabwera akuvomereza ndi kulalikira ntchito zawo. 19Ndipo ambiri amene amachita matsenga anabweretsa mabuku awo [a nyanga] ndipo anawatentha pamaso pa onse. Ndipo iwo anawerengetsera mitengo yake, ndipo anapeza kuti imakwanira ndalama za siliva zikwi makumi asanu. 20Chotero ndi mphamvu mau a Ambuye anachulukira ndi kulalikidwa.
21Ndipo pamene zinthu zimenezi zinakwaniritsidwa, Paulo anatsimikizika mu mtima mwake kupita ku Yerusalemu, nadutsa ku Makedoniya ndi Akaya, nanena, pamene ndikafika kumeneko ndikaonanso Roma. 22Ndipo pamene anatumiza m’Makedoniya awiri mwa iwo amene amatumikira iye, Timoteo ndi Erasto, iye yekha anakhalabe m’Asiya. 23Ndipo kumeneko kunachitika nthawi imeneyo chisokonezo osati chaching’ono pokhudza njirayo. 24Pakuti [munthu] wina dzina lake Demetriyo, wosula siliva, amene amapanga akachisi a siliva a Artemi, anabweretsa phindu osati pang’ono kwa Artemi; 25ameneyu anasonkhanitsa pamodzi, iwo amene amagwira ntchito yotere, nati, Amuna inu, mudziwa bwino lomwe kuti kukhala kwathu kumadalira ntchito imeneyi, 26ndipo inu mwaona ndi kumva kuti Paulo ameneyu wanyengerera ndi kuchotsa kwa ife khamu lalikulu, osati ku Efeso kokha, koma ku Asiya yense, nanena kuti kulibe milungu3 imene ili yopangidwa ndi manja. 27Tsopano sikuti pali chiopsezo pa ife tokha kuti malonda athu asokonekera, komanso kuti kachisi wa mulungu4 wamkazi wamkulu Artemi akhala wopanda phindu, ndipo ukulu wake uwonongeka umene dera lonse la Asiya ndi dziko lonse amampembedza. 28Ndipo pamene anamva [izi], ndi podzala ndi mkwiyo, iwo anafuula, nanena, Wamkulu [ndi] Artemi wa Aefeso. 29Ndipo mzinda [wonse] unadzala ndi chipwirikiti, ndipo iwo anathamangira ndi mtima umodzi ku bwalo la masewero, atawagwira Gayo ndi Aristarko, Amakedoniya, a paulendo amzake a Paulo. 30Koma Paulo anafunitsitsa kupita kwa anthuwo, ophunzira anamuletsa iye; 31ndipo ena amu Asiyanso, amene anali amzake, anamtumizira uthenga kuti asakaziponye yekha m’bwalo la masewero. 32Anthu osiyana anafuula zinthu zosiyananso; pakuti msonkhano unasokonezeka, ndipo ambiri sanadziwe chimene anabwerera pamodzi. 33Komatu pakati pa khamulo anayika kutsogolo Alesandro, Ayuda akumukankhira kutsogolo. Ndipo Alesandro, potukula dzanja lake, anafuna kuziteteza kwa anthuwo. 34Komatu, pozindikira kuti anali Myuda, panali kulira kumodzi kuchokera kwa onse, kufuula pafupifupi maola awiri, Wamkulu [ndi] Artemi waku Efeso. 35Ndipo mlembi wa deralo, anakhazika chete khamulo, nanena, Aefeso, ndani amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso ndi wosungira kachisi wa Artemi wamkulu, ndi [chifanizo] chimene chinagwa kuchokera kumwamba? 36Pamenepo zinthu izi ndi zosatsutsika, nkoyenera kuti inu mukhale bata kusachita kanthu ka liuma. 37Pakuti mwabweretsa anthu awa, [amene] siolanda kachisi, kapena kulankhula zamwano za mulungu5 wanu wamkazi. 38Pamenepo ngati Demetriyo ndi amisiri okhala naye ali ndi kanthu ndi wina aliyense, mabwalo a milandu alipo, ndiponso ziwanga zilipo: aloleni anenezane wina ndi mzake. 39Koma ngati mufuna kufufuza kanthu kena, zikakambidwa ku msonkhano wolamulidwa. 40Pakutinso nafe tili pa chiopsezo kunenezedwa pa mlandu wa chipolowe pa [zochitika] za lerozi, pakuti palibe chifukwa chimene tingafotokozere pa chipwirikiti ichi. 41Ndipo atalankhula zinthu izi anamasula msonkhano.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu