Mutu 26

1Ndipo inafika nthawi imene Yesu anatsiriza kulankhula zonse izi, Iye anati kwa ophunzira ake, 2Inu mukudziwa kuti pakupita kwa masiku awiri phwando la paskha lichitika ndithu, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.

3Pamenepo akulu ansembe ndi akulu anasonkhana pamodzi kunyumba kwa mkulu wa ansembe amene amatchedwa Kayafa, 4ndipo anapangana upo pamodzi cholinga kuti am’gwire Yesu mwa chinyengo ndi kumupha Iye; 5koma iwo anati, Osati patsiku la phwando, kuti pasakhale phokoso pakati pa anthu.

6Koma Yesu pakukhala m’Betaniya, m’nyumba ya Simoni wa khate, 7mzimayi, wakukhala nayo nsupa ya mafuta onunkhira, anabwera kwa Iye natsanulira mafutawo pamutu pake pamene amakhala pa gome. 8Koma ophunzira pakuona ichi anapsa mtima, nanena, Chifukwa chiyani kuononga kumeneku? 9pakuti mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa ndalama zochuluka ndi kudzipereka kwa osauka. 10Koma Yesu pakudziwa [ichi] anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukumvuta mayiyu? Pakuti iye wachita ntchito yabwino kwa Ine. 11Pakuti osauka muli nawo nthawi zonse inu, koma Ine simudzakhala nane nthawi zonse. 12Pakuti pakutsanulira mafutawa pathupi langa, iye wachita ichi pa kuikidwa kwanga m’manda. 13Zoonadi ndinena kwa inu, Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwa padziko lapansi, zimenenso wachita [mzimayi] uyu zidzalankhulidwa ngati chikumbutso cha iye.

14Pamenepo m’modzi wa khumi ndi awiri, amene anatchedwa Yudase Isikariote, anapita kwa akulu ansembe 15ndipo anati, Kodi mufuna kundipatsa chiyani ine, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo anamukonzera iye ndalama za siliva makumi atatu. 16Ndipo kuyambira nthawi imeneyo anafuna mpata wabwino kuti ampereke Iye.

17Tsopano pa [tsiku] loyamba la [phwando la] mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anabwera kwa Yesu, nanena, Kodi mufuna kuti tikakonzere kuti paskha kuti inu mukadye? 18Ndipo anati, Pitani mu mzinda kwa munthu, ndipo mukati kwa iye, Mphunzitsi akuti, Nthawi yanga yayandikira, ndidzadya paskha m’nyumba mwako pamodzi ndi ophunzira anga. 19Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawalamulira iwo, ndipo anakonza paskha.

20Ndipo pamene madzulo anafika Iye anakhala pagome pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. 21Ndipo pamene anali kudya Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka Ine. 22Ndipo pakukhala nacho chisoni chachikulu iwo anayamba kulankhula kwa Iye, Kodi ndine, Ambuye? 23Koma Iye pakuyankha anati, Iye amene akusunsa dzanja lake ndi Ine m’mbale, iyeyu ndi amene adzandipereka Ine. 24Mwana wa munthu adzapita ndithu, molingana ndi momwe zinalembedwera zokhudza Iye, koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa munthu; kukanakhala bwino kwa munthu ameneyu akanapanda kubadwa. 25Ndipo Yudase, amene anampereka Iye, pakuyankha anati, Kodi ndine, Rabi? Anati kwa iye, watero iwe.

26Ndipo pamene anali kudya, Yesu, pakutenga mkate ndi kuudalitsa, anaunyema [iwo] naupereka [iwo] kwa ophunzira ake, nati, Tengani, idyani: limeneli ndi thupi langa. 27Ndipo pakutenga chikho ndi kuyamika, anachipereka [icho] kwa iwo, nanena, Imwani inu nonse chimenechi. 28Pakuti umenewu ndi mwazi wanga, umene uli wa chipangano [chatsopano], umene unakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo. 29Koma ndinena kwa inu, kuti sindidzamwa konse chipatso ichi cha mpesa, kufikira tsiku ilo limene ndidzamwa ichi kwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate wanga. 30Ndipo atayimba nyimbo, iwo anapita ku phiri la Azitona.

31Pamenepo Yesu anati kwa iwo, nonsenu mukhumudwa nane mu usiku uwu. Pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha m’busa, ndipo gulu la nkhosa lidzabalalika. 32Komatu zikapita zimenezi ndidzauka, ndipo ndidzapita patsogolo panu ku Galileya. 33Ndipo Petro pakuyankha anati kwa Iye, Ngati ena onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nanu. 34Yesu anati kwa iye, Zoonadi ndinena kwa iwe, kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, uzandikana Ine katatu. 35Petro anati kwa Iye, Ngati ine ndikafuna ndidzafa ndi Inu, ine mwanjira ina iliyonse sindingakukaneni Inu. Chimodzimodzinso anatero ophunzira onse.

36Pamenepo Yesu anabwera nawo ku malo otchedwa Getsemane, ndipo anati kwa ophunzira, Bakhalani pano kufikira ndipita ndi kukapemphera uko. 37Ndipo pamene anatengana pamodzi ndi [Iye] Petro ndi ana awiri a Zebedayo, Iye anayamba kumva chisoni ndi kupsinjika mtima kwambiri. 38Pamenepo anati kwa iwo, Moyo wanga uli ndi chisoni chofikira ku imfa; bakhalani pano mupenyerere pamodzi ndi Ine. 39Ndipo pakupita patsogolo pang’ono Iye anagwetsa nkhope yake pansi, napemphera ndi kuti, Atate wanga, ngati ndi kotheka lolani chikho ichi chindipitirire; komatu simonga Ine ndifuna, koma monga Inu [mufuna]. 40Ndipo Iye anabwera kwa ophunzira ndipo anawapeza iwo akugona, ndipo anati kwa Petro, Kodi simungakwanitse kukhala chipenyere kwa ola limodzi ndi Ine? 41Penyererani ndi kupemphera, kuti musalowe m’mayesero: mzimudi [uli] wokonzeka, koma thupi ndi lofooka. 42Atapitanso kachiwiri Iye anapemphera nati, Atate wanga ngati ichi sichindipitirira [Ine] kufikira ndikamwera ichi, chifuniro chanu chichitike. 43Ndipo Iye pakubwera anawapezanso akugona, pakuti maso awo anali atalemedwa. 44Ndipo pakuwaleka iwo, Iye anapitanso nakapemphera kachitatu, nanena chinthu chomwecho. 45Pamenepo Iye anabwera kwa ophunzira ndipo anena kwa iwo, Zigonani tsopano ndipo bapumulani; taonani, ola lawandikira, ndipo Mwana wa munthu akuperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa. 46Dzukani, tiyeni tidzipita; taonani, iye wakundipereka Ine wayandikira.

47Ndipo akali chilankhulire, taonani, Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiri aja, anabwera, ndipo anali nalo khamu lalikulu la anthu lili ndi malupanga komanso zindodo ochokera kwa akulu ansembe ndi akulu a anthu. 48Tsopano iye wakumperekayo anawapatsa iwo chizindikiro, nanena, Iye amene nditampsopsone, ndi ameneyo: mgwireni Iye. 49Ndipo nthawi yomweyo pakubwera kwa Yesu anati, Tikuoneni, Rabi, ndipo anampsopsonetsa Iye. 50Koma Yesu anati kwa iye, Mzanga, wabwera pa cholinga chanji? Pamenepo pakubwera anaika manja awo pa Yesu ndipo anamgwira Iye. 51Ndipo taonani, m’modzi wa iwo amene anali ndi Yesu anatambasula dzanja lake natenga lupanga lake, ndipo anamkantha kapolo wa mkulu wansembe nadula khutu lake. 52Pamenepo Yesu anati kwa iye, Bwezera lupanga lako m’malo mwake; pakuti iwo akuyenda ndi lupanga adzaonongeka ndi lupanga. 53Kapena ukuganiza kuti sindingathe kuitanira pa Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira khamu la angelo oposa makumi ndi awiri? 54Kodi pamenepo malembo adzakwaniritsidwa bwanji kuti chimenechi chichitike?

55Mu ola lomwelo Yesu anati kwa makamu, Kodi mukubwera kudzandigwira Ine ndi malupanga komanso ndodo monga mukufuna wachifwamba? Ine ndinakhala [ndi inu] tsiku ndi tsiku kuphunzitsa mkachisi, ndipo inu simunandigwire. 56Komatu izi zachitika kuti malembo a mneneri akwaniritsidwe. Pamenepo ophunzira onse anamusiya Iye nathawa.

57Tsopano iwo amene anamgwira Yesu anamtsogolera [Iye] kwa Kayafa wamkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anasonkhanako. 58Ndipo Petro anamtsatira Iye patali, ngakhale kunyumba kwa wamkulu wa ansembe kumene, ndipo pakulowa iye anakhala ndi asilikali kuti aone chimaliziro.

59Ndipo wamkulu wa ansembe ndi akulu komanso bwalo lonse anafuna umboni wabodza wotsutsana ndi Yesu, cholinga kuti akamuphe Iye. 60Ndipo iwo sanapeze umboni ulionse, ngakhale kuti mboni zochuluka zabodza zinabweretsa maumboni awo. Komatu kunadza mboni zina zabodza ziwiri zotsiriza 61ndipo zinati, Uyu anati, ndikhoza kuphwasula kachisi wa Mulungu1, ndipo kwa masiku atatu kumumanganso. 62Ndipo wamkulu wa ansembe pakuimilira anati kwa Iye, Kodi suyankha kanthu? Kodi maumboni awa akuneneza Iwe ndi otani? 63Koma Yesu anakhala chete. Ndipo wamkulu wa ansembe pakuyankha anati kwa Iye, Ndikulumbiritsa ine pa Mulungu2 wa moyo kuti utiuze ife ngati Iwe uli Khristu mwana wa Mulungu3. 64Yesu anati kwa iye, Inu mwatero. Komabe, ndinena kwa inu, Kuyambira tsopano inu mudzaona Mwana wa munthu akukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kubwera pa mitambo ya kumwamba. 65Pamenepo wamkulu wa ansembe anang’amba zovala zake, nanena, Uyu wachitira mwano Mulungu: kodi tifuniranji umboni wina woonjezera? Taonani, tsopano mwamva mwano wakuchitira Mulungu. 66Kodi inu mukuganiza bwanji? Ndipo iwo pakuyankha anati, Akuyenera kulandira chilango cha imfa. 67Pamenepo anamulavulira pa nkhope pake, ndi kum’bwanyula Iye, ndipo ena anamumenya makofu, 68nanena, Nenera kwa ife, Khristu, kodi ndi ndani wakumenya iwe khofu?

69Koma Petro anakhala kunja kwa bwalo la milandu; ndipo mdzakazi anabwera kwa iye, nanena, Ndipo iwe unali ndi Yesu m’Galileya. 70Komatu iye anakana pamaso pa onse, nanena, Sindikudziwa zimene ukulankhulazo. 71Ndipo pamene iye amatuluka kunja kwa chipata, [mdzakazi] wina anamuona iye, ndipo analankhula kwa iwo amene anali pamenepo, [Munthu] uyu analinso ndi Yesu m’Nazarayo. 72Ndipo iye anakananso ndi lumbiro: Ine sindimudziwa munthuyu. 73Ndipo itapita nthawi yochepa, iwo amene anaimirira [pamenepo], pakubwera kwa [iye], anati kwa Petro, Zoonadi iwenso ndiwe m’modzi wa iwo, pakuti malankhulidwe ako akusonyeza choncho. 74Pamenepo anayamba kutemberera ndi kulumbira, Ine sindikum’dziwa munthu ameneyu. Ndipo nthawi yomweyo tambala analira. 75Ndipo Petro anakumbukira mau a Yesu, amene ananena [kwa iye], asanalire tambala udzandikana Ine katatu. Ndipo iye anatuluka kunja, nalira mosweka mtima.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu