Mutu 9

1Pakuti zokhudza kutumikira kumene kuli kwa oyera mtima, sikofunika kuti ndikulembereni. 2Pakuti ndikudziwa kukonzeka kwanu, kumene ndimanyada nako pokhudza inu kwa Amakedoniya, kuti Akaya anali wokonzeka kuyambira chaka chatha, ndi changu chanu chalimbikitsa ambiri [mwa abale]. 3Koma ndawatuma abale, cholinga kuti kunyada kwathu pa inu kusakhale chabe m’menemo, cholinga kuti, monga ndalankhula kale, mukakhale okonzeka; 4Ndidzakhala wosakondwa, ngati Amakedoniya adzabwera ndi ine napeza muli osakonzeka, ifeyo, osati inu ayi tidzachititsidwa manyazi m’kulimbika kumeneku. 5Pamenepo ndiganiza kuti nkofunikira ndiwapemphe abale kuti abwere kwa inu, ndi kumalidzitsiratu kulengezedwa kwa mdalitso wanu, kuti mdalitso wanu ukakhale wokonzeka, ndipo osati ochotsedwa kwa inu. 6Koma choonadi ndi ichi, iye wofetsa mouma manja adzakololanso mouma manja; ndipo iye wofetsa mu [mzimu wa] mdalitso adzakololanso mu mdalitso: 7aliyense molingana ndi kutsimikiza kwa mtima wake; osati mwa chisoni, kapena mokakamiza; pakuti 1Mulungu amaondwera ndi opereka mokondwera. 8Koma 2Mulungu ali wakutha kupanga mphatso iliyonse ya chisomo kumangilirika kwa inu, kuti, mwanjira ina iliyonse nthawi zonse mukakhale nacho chikwaniro chonse, mukamangilirike ku ntchito iliyonse yabwino: 9monga kunalembedwa, Anawabalalitsira kunja, napereka kwa osauka, kulungama kwake kudzakhala muyaya. 10Tsopano iye amene apereka mbeu kwa wofetsayo, ndi mkate ukhale chakudya adzapereka ndi kuchulukitsa zofetsa zanu, nachulukitsa zipatso za kulungama kwanu: 11nalemeretsa njira zonse ku kupereka konse kwa ufulu, kumene kuchita mwa ife polemekeza 3Mulungu. 12Chifukwa utumiki wa ntchito iyi siongodzazitsa mlingo wa zosoweka za oyera mtima, komanso mkuchuluka pa zoyamika zambiri kwa 4Mulungu; 13iwo polemekeza 5Mulungu kudzera mu umboni wa utumiki umenewu, pa chifukwa cha kumvera kwanu, pa kulalikidwa, kwa uthenga wabwino wa Khristu, ndi ufulu wa mumtima polumikizana ndi iwo komanso anthu onse; 14ndipo m’mapemphero awo pa inu, adzala ndi kukhumbitsa pa inu, pa cholinga chakuti chichuluke chisomo cha 6Mulungu pa inu. 159Atamandike 7Mulungu pa mphatso ya ulere yosasimbika.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu