Mutu 3

1Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalandira chilango choposa. 2Pakuti ife tonse timakhumudwitsa kawirikawiri. Ngati wina sakhumudwitsa m’mau, iye [ali] munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lake. 3Taonani, timayika zogwirira mkamwa akavalo, kuti atimvere ife, ndipo timatembenuza thupi lawo lonse. 4Taonaninso sitima ya pamadzi, imakhala yaikulu kwambiri, ndipo imayendetsedwa ndi mphepo za mkuntho, zimatembenuzidwa ndi chiongolero chaching’ono, kupita kulikonse kumene woyendetsayo afuna. 5Chomwechonso lilime ndi chiwalo chaching’ono, ndipo limazikweza pa zinthu zazikulu. Taonani kuchepa kwa moto, umayatsa chikuni chachikulu! 6ndipo lilime [ndi] moto, dziko la chisalungamo; lilime linayikidwa mwa ziwalo zathu, chodetsa cha thupi lonse, ndipo limayatsa moto ku moyo wa chilengedwe, ndipo limayatsa moto wa gehena. 7Pakuti mtundu ulionse wa zinyama ndi mbalame, zokwawa ndi za m’madzi, zimazolowetsedwa ndi mtundu wa anthu; 8koma lilime palibe m’modzi mwa anthu akhoza kulizoloweretsa; [lili] choipa chosakhazikika, lodzala ndi imfa – yobweretsa mwavi. 9Pamenepo ife tiyamika nalo Ambuye ndi Atate, ndiponso pamenepo titembelera nalo anthu opangidwa m’chifanizo cha Mulungu1. 10Kutuluka mkamwa momwemo mdalitso ndi thembelero. Chimenechi sicholondola, abale anga, kuti zinthu zimenezi zikhale chomwechi. 11Kodi kasupe, pa una lomwelo, akhoza kutulutsa madzi okoma ndi owawa? 12Kodi abale anga, mkuyu ukhoza kubereka azitona kapena mpesa kubereka mkuyu? Kotero madzi a mchere sangathe kutulutsa madzi okoma.

13Ndani wa nzeru ndi wozindikira pakati panu; mlekeni awonetsere ndi malankhulidwe abwino ntchito zake ndi nzeru zofatsa; 14koma ngati mukhala nako kuwawidwa ndi makangano m’mitima mwanu, musazitamandire ndi kunama motsutsana ndi choonadi. 15Imeneyi sinzeru yochokera kumwamba, koma yadziko lapansi, ya umunthu, ya mdierekezi. 16Pakuti pamene pali kuwawidwa mtima ndi makangano, pamakhala chipwirikiti ndi zoipa zonse. 17Koma nzeru yakumwamba poyambilira ndi yoyera, kenako ya mtendere, yofatsa, imalolera, yodzala ndi chifundo ndi zipatso zabwino, yosakayikitsa, yopanda chinyengo. 18 Koma chipatso cha chilungamo mu mtendere chimaonetsedwa pa iwo obweretsa mtendere.

1Elohimu