Mutu 28

1Tsopano litapita sabata, pamene kunali m’bandakucha wa tsiku lotsatira, anabwera Mariya wa Magadala ndi Mariya wina kudzazonda mandawo.

2Ndipo taonani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye, wakutsika kuchokera kumwamba, anabwera ndi kugubuduza mwalawo ndi kukhala pa iwo. 3Ndipo maonekedwe ake anali ong’anima, ndipo zovala zake zinali zoyera ngati matalala. 4Ndipo pakumuopa iye alonda ananjenjemera nakhala ngati anthu akufa. 5Ndipo mngeloyo pakuyankha anati kwa akaziwo, Musaope inu, pakuti ndikudziwa kuti mukufuna Yesu wopachikidwayo. 6Iyetu sali muno, pakuti wauka, monga Iye ananenera. Bwerani, dzaoneni pamalo pamene Ambuye anagona. 7Ndipo pitani mwachangu ndi kunena kwa ophunzira ake kuti Iye wauka kwa akufa; ndipo taonani, Iye akutsogolerani inu m’Galileya, kumeneko inu mudzamuona Iye. Taonani, ine ndakuuzani inu. 8Ndipo pakutuluka mwachangu kuchoka kumanda ali ndi mantha komanso chimwemwe chachikulu, iwo anathamanga kukapereka mawu kwa ophunzira ake. 9Ndipo pamene iwo amapita kukapereka mawu kwa ophunzira ake, taonaninso, Yesu anakumana nawo, nanena, Tikuoneni! Ndipo iwo pakubwera kwa Iye anagwada pa mapazi ake, ndipo anamlemekeza Iye. 10Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Musachite mantha; pitani, kaperekeni mawu kwa abale anga kuti apite m’Galileya, ndipo kumeneko iwo akandiona Ine.

11Ndipo pamene iwo amapita, taonani, ena mwa alonda analowa mu mzinda, nakapereka mawu kwa akulu ansembe pa zinthu zonse zimene zinachitika. 12Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, natenga uphungu, iwo anapereka ndalama zochuluka kwa asilikali, 13nanena, Nenani kuti ophunzira ake pakubwera usiku anamuba Iye [pamene] ife [tinali] kugona. 14Ndipo zimenezi akazimva kazembe, ife tidzamlimbikitsa iye, ndipo tidzakupulumutsani inu ku nkhawa. 15Ndipo anatenga ndalama nachita iwo monga anawaphunzitsira. Ndipo uthenga umenewu udakalipobe pakati pa Ayuda kufikira lerolino.

16Koma ophunzira khumi ndi m’modzi aja anapita ku Galileya ku phiri kumene Yesu adawasonyeza iwo. 17Ndipo pamene iwo anamuona Iye, anamlambira: komabe ena anakaika. 18Ndipo Yesu pakubwera analankhula kwa iwo, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine kumwamba ndi dziko lapansi. 19Pitani [pamenepo] ndipo kapangeni ophunzira a mitundu yonse, pakuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera; 20kuwaphunzitsa iwo kutsatira zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu. Ndipo taonani, Ine ndili nanu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.