Mutu 5
1Akulu amene ali pakati panu ndiwadandaulira, ine amenenso ndili mkulu mnzawo ndi mboni ya mazunzo a Khristu, ine amenenso ndili wotenga gawo wa ulemelero umene udzavumbulutsidwa: 2wetani gulu la nkhosa la Mulungu1 limene lili pakati panu, liyang’anireni, osati mokakamiza, koma mwaufulu; osati potengera kupeza phindu, koma modzipereka; 3osati kuchita umbuye pa iwo, koma kukhala chitsanzo chabwino pa gulu la nkhosazo. 4Ndipo pamene m’busa wamkulu adzaonekera mudzalandira chisoti chosafota cha ulemelero.
5Chimodzimodzinso inu achinyamata, mverani akulu, ndipo inu nonse mumangilirike pa kudzichepetsa kwa wina ndi mzake; pakuti Mulungu2 akaniza odzikuza, koma kwa odzichepetsa apereka chisomo. 6Zichepetseni nokha pamenepo pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu3, kuti akakukwezeni inu mu nthawi yoyikika; 7mutataya nkhawa zanu zonse kwa iye, pakuti iye amasamala za inu.
8Khalani odzisungira, dikirani. Mdani wanu mdierekezi monga mkango wobuma uyenda kufunafuna wina kuti umlikwire. 9Ameneyo mkanizeni, khazikikani m’chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zikukwaniritsidwa mwa abale anu m’dziko lapansi. 10Koma Mulungu4 wa chisomo amene wakuyitanani inu ku ulemelero wake mwa Khristu Yesu, pamene inu mwazunzika mwa kanthawi, mwini wake adzakupangani kukhala angwiro, okhazikika, olimbika, ochilimika: 11kwa iye kukhale ulemelero ndi mphamvu ya kunthawi za nthawi. Amen.
12Mwa Silvano, m’bale wokhulupirikayo, monga ndiganiza, ndakulemberani mwachidule; kudandaulira ndi kuchitira umboni kuti chimenechi ndi chisomo chenicheni cha Mulungu5 chimene inu muimamo. 13Iye amene anasankhidwa ndi inu m’Babulo akulonjerani, ndi Marko mwana wanga. 14Lonjeranani wina ndi mzake ndi chipsopsono cha chikondi. Mtendere ukhale kwa inu nonse mwa Khristu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu