Mutu 11
1Khalani onditsanza ine, monga insenso ndili wotsanza Khristu.
2Tsopano ndikutamandani inu, kuti mu zinthu zonse mumandiganizira ine; ndipo kuti pamene ine ndakulangizani, musunga malangizowo. 3Koma ndikufuna kuti inu mudziwe kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, koma mutu wa mkazi ndiye mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu1. 4Mwamuna wina aliyense popemphera kapena ponenera, akaphimba kumutu kwake, anyazitsa mutu wake. 5Koma mkazi aliyense popemphera kapena ponenera wosaphimba kumutu kwake anyazitsa mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa. 6Pakuti ngati mkazi akhala wosaphimba kumutu, tsitsi lake limetedwe. Koma ngati achita manyazi kusenga kapena kumeta tsitsi, aphimbe tsitsi lakelo. 7Pakuti mwamuna zoonadi sayenera kuphimba kumutu kwake, pokhala iye chifanizo cha Mulungu2 ndi ulemelero; koma mkazi ndiye ulemelero wa mwamuna. 8Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna. 9Pakutinso mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwa chifukwa cha mwamuna. 10Chotero mkazi akhale ndi ulamuliro pa mutu wake, pa chifukwa cha angelo. 11Komabe mwamuna sakhalako popanda mkazi, kapena mkazi sakhalako popanda mwamuna, mwa Ambuye. 12Pakuti mkazi ndi wamwamuna, koteronso mwamuna ndi wamkazi, koma zinthu zonse ndi za Mulungu3. 13Weruzani nokha: ndi koyenera kuti mkazi apemphere kwa Mulungu4 wosaphimba kumutu? 14Kodi chilengedwe sichikuphunzitsani inu, kuti mwamuna, ngati ali ndi tsitsi lalitali, limchotsera iye ulemu? 15Koma ngati mkazi, ali nalo tsitsi lalitali, likhala ulemelero kwa iye; pakuti tsitsi lalitali linapatsidwa kwa iye monga chophimba kumutu. 16Koma ngati wina aganiza kutsutsana nazo, ife tilibe machitidwe ena, kapenanso mpingo wa Mulungu5.
17Koma pokufotokozerani izi kwa inu [zimene ndifuna kukuuzani], sindikukuyamikirani, ponena kuti mumasonkhana pamodzi osati pochita zabwino, koma zoipa. 18Pakuti choyamba pamene mubwera pamodzi mu mpingo, ndimamva kuti pali kusankhana pakati panu, ndipo ndivomereza zimenezi. 19Pakuti pali kugawikana pakati panu, kuti iwo ovomerezedwa awonetsedwe pakati panu. 20Pamene inu mwabwera malo amodzi, simukhala kuti mukudya mgonero wa Ambuye. 21Pakuti aliyense wa inu pakudya amadya mgonero wake pamaso pa wina, ndipo wina ali ndi njala pamene wina akumwa mopyola muyeso. 22Kodi inu mulibe nyumba zanu zimene mukhoza kudyera ndi kumwera? Kapena mukupeputsa mpingo wa Mulungu6, ndi kuchititsa manyazi iwo amene alibe kanthu? Kodi ndilankhule nanu chiyani? Kodi ndikuyamikireni? Pa mfundo iyi sindingakuyamikireni. 23Pakuti ndinalandira kuchoka kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu, usiku uja umene anaperekedwa, anatenga mkate, 24ndipo atayamika anaunyema, nati, Ili ndi thupi langa, limene lili kwa inu: chitani ichi pokumbukira Ine. 25Momwemonso anatenga chikho, atamwa anati, Chikho ichi ndi pangano latsopano la mwazi wanga: chitani ichi, nthawi zonse pamene mumwa, pokumbukira Ine. 26Pakuti nthawi zonse pamene mudya mkate uwu, ndi kumwera chikho ichi, mulalikira imfa ya Ambuye, kufikira Iye akadza. 27Kotero kuti amene akadya mkate, kapena kumwera chikho ichi, kosayenera, adzakhala wochimwira pokhudza thupi ndi mwazi wa Ambuye. 28Koma munthu adzisanthule yekha, ndipo pamenepo akadye mkate, ndi kumwera chikho. 29Pakuti wakudya ndi kumwayo adzimwera yekha chiweruziro, posazindikira thupilo. 30Pa nkhani imeneyi ambiri mwa inu ndi ofooka ndi odwala, ndipo ambiri anamwalira. 31Koma tikanaziyesa tokha, sitikanaweruzidwa. 32Koma pokhala taweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tisatsitsidwe pamodzi ndi dziko lapansi. 33Kotero kuti, abale, pamene mubwera pamodzi kudya, dikiranani wina ndi mzake. 34Ngati wina ali ndi njala, mloleni adye kunyumba kwake, kuti mungasonkhane pamodzi mkuweruzidwa. Koma zinthu zina zonse, ndidzakuuzani pamene ndibwera.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu