Mutu 16
1Ndipo Afarisi ndi Asaduki, anabwera kwa [Iye], namfunsa, pomuyesa [Iye], kuti awaonetse iwo chizindikiro cha kumwamba. 2Koma Iye powayankha anati kwa iwo, Pamene madzulo afika, mumanena kuti, Nyengo yabwino, pakuti thambo lili lacheza; 3ndipo mamawa munena, Lero ndi kwa mphepo, pakuti thambo lili lacheza chodera [ndi] chotsika m’munsi; inutu mudziwa [momwe] musiyanitsira nkhope ya thambo, koma simudziwa zizindikiro za nyengo yino. 4M’badwo woipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzaperekedwa kwa iwo koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya iwo ndi kuchokapo.
5Ndipo pamene ophunzira ake anafika kumbali ina, iwo anaiwalira kutenga mkate. 6Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang’anirani ndipo mupewe chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki. 7Ndipo iwo anafunsana pakati pa iwo okha, nanena, Chifukwa sitinatenge mkate. 8Ndipo Yesu pakudziwa [ichi], anati, Chifukwa chiyani mukufunsana pakati panu, Inu a chikhulupiriro chochepa, chifukwa simunatenge mkate? 9Kodi simukumvetsetsabe kapena kukumbukira mikate isanu imene anadya anthu zikwi zisanu, komanso mitanga yotsala ya makombo? 10kapena mikate isanu ndi iwiri imene anadya anthu zikwi zinayi, komanso mitanga yotsala ya makombo? 11Kodi simukumvetsetsa pati kuti [sunali] mkate umene ndinanena kwa inu, Yang’anirani ndipo mupewe chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki? 12Kenako iwo anazindikira kuti Iye samalankhula za kuyang’anira mkate wa chotupitsa, koma kuti chinali chiphunzitso chokhudza Afarisi ndi Asaduki.
13Koma pamene Yesu amapita mbali ya Kaisareya wa Filipi, Iye analamulira ophunzira ake, nanena, Kodi anthu amati Ine Mwana wa munthu ndine ndani? 14Ndipo iwo anati, Ena amati, Yohane m’batizi; ndipo ena, Eliya; ndipo enanso, Yeremiya kapena m’modzi wa aneneri. 15Iye anati kwa iwo, Koma inu, mumati Ndine ndani? 16Ndipo Simoni Petro pakuyankha anati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa °Mulungu1. 17Ndipo Yesu pakuyankha anati kwa iye, Wodala iwe, Simoni Bar-Yona, pakuti mwazi ndi thupi sizinakuululire [zimenezi] kwa iwe, koma Atate wanga amene ali kumwamba. 18Ndiponso Ine, ndinena kuti iwe Petro, pa thanthwe limeneli ndidzamangapo mpingo wanga, ndipo makomo a dziko la anthu akufa sadzaulaka iwo. 19Ndipo ine ndidzakupatsa zifungulo za ufumu wa kumwamba; ndipo chilichonse chimene udzachimanga padziko lapansi chidzamangidwa kumwamba; ndipo chimene udzachimasula padziko lapansi chidzamasulidwa kumwamba. 20Pamenepo Iye analamulira ophunzira ake kuti asauze munthu wina aliyense kuti Iye anali Khristu.
21Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuonetsera kwa ophunzira ake kuti Iye akuyenera kupita ku Yerusalemu, ndipo akazunzika mu zinthu zambiri kuchoka kwa akulu ndi ansembe akulu ndi alembi, ndipo akaphedwa, ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa. 22Ndipo Petro anamutengera [Iye] pambali nayamba kumdzudzula, nanena, [Mulungu] akuchitireni chifundo, Ambuye; zimenezi sizidzachitika kwa Inu. 23Koma potembenuka, Iye anati kwa Petro, Choka pita kumbuyo kwanga, Satana; ndiwe chokhumudwitsa Ine, pakuti malingaliro ako sali pa zinthu za Mulungu1, koma ali pa zinthu zimene zili za anthu. 24Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kubwera pambuyo panga, adzikanize yekha ndi kunyamula mtanda wake nanditsate Ine. 25Pakuti aliyense amene adzafuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; koma iye amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzaupeza. 26Kodi munthu adzapindula chiyani, ngati adzapeza dziko lonse lapansi ndi kutaya moyo wake? Kapena munthu adzapereka chiyani chosinthanitsa ndi moyo wake? 27Pakuti Mwana wa munthu watsala pang’ono kubwera mu ulemelero wa Atate wake ndi angelo, ndipo adzapereka kwa aliyense molingana ndi machitidwe ake. 28Indetu ndinena kwa inu, Alipo ena akuima pano amene sadzalawa konse imfa kufikira adzaona Mwana wa munthu akubwera mu ufumu wake.
1Elohimu